Ezekieli 18:1-32

  • Aliyense adzaimbidwa mlandu chifukwa cha machimo ake (1-32)

    • Moyo umene wachimwa ndi umene udzafe (4)

    • Mwana sadzakhala ndi mlandu uliwonse pa zolakwa za bambo ake (19, 20)

    • Sasangalala ndi imfa ya munthu woipa (23)

    • Munthu wolapa amapulumutsa moyo wake (27, 28)

18  Yehova analankhulanso nane kuti:  “Kodi mwambi umene mumanena mʼdziko la Isiraeli wakuti, ‘Bambo adya mphesa zosapsa koma mano a ana ndi amene ayezimira,’+ umatanthauza chiyani?  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali ine Mulungu wamoyo, simudzanenanso mwambi umenewu mu Isiraeli.  Tamverani! Miyoyo yonse ndi yanga. Moyo wa bambo komanso moyo wa mwana, yonse ndi yanga. Moyo umene wachimwa ndi umene udzafe.*  Tiyerekeze kuti munthu ndi wolungama ndipo amachita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo.  Iye sadya zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano mʼmapiri+ komanso sadalira mafano onyansa* a nyumba ya Isiraeli. Iye sagona ndi mkazi wa mnzake+ kapena kugona ndi mkazi amene akusamba.+  Sazunza munthu aliyense+ koma amabweza chikole kwa munthu amene anakongola zinthu zake.+ Salanda zinthu za ena mwauchifwamba+ koma amapereka chakudya chake kwa munthu amene ali ndi njala+ ndiponso amaphimba munthu wamaliseche ndi chovala.+  Iye sauza anthu kuti amupatse chiwongoladzanja akabwereketsa zinthu ndipo sakongoza zinthu mwa katapira+ koma amapewa kuchita zinthu mopanda chilungamo.+ Iye amatsatira chilungamo chenicheni akamaweruza munthu ndi mnzake.+  Ndipo amapitiriza kuyenda motsatira malamulo anga ndi kusunga zigamulo zanga kuti azichita zinthu mokhulupirika. Munthu ameneyu ndi wolungama, ndithu adzapitiriza kukhala ndi moyo,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 10  ‘Koma ngati munthuyo wabereka mwana wamwamuna, mwanayo nʼkukhala wakuba+ kapena wopha anthu+ kapenanso amachita chilichonse cha zinthu zimenezi, 11  (ngakhale kuti bamboyo sanachitepo chilichonse mwa zinthu zimenezi), ngati mwanayo amadya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano mʼmapiri ndipo amagona ndi mkazi wa mnzake, 12  ngati amazunza munthu wovutika ndi wosauka,+ ngati amalanda zinthu za ena mwauchifwamba, ngati sabweza chikole, ngati amadalira mafano onyansa,+ ngati amachita makhalidwe onyansa,+ 13  ngati amakongoza zinthu zake mwa katapira ndipo amauza anthu kuti apereke chiwongoladzanja,+ ndiye kuti mwanayo sadzapitiriza kukhala ndi moyo. Chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi, iye adzaphedwa ndithu. Magazi ake adzakhala pamutu pake. 14  Koma tiyerekeze kuti bambo ali ndi mwana wamwamuna amene amaona machimo onse amene bambo akewo amachita. Ngakhale kuti mwanayo amaona bambo ake akuchita machimowo, iye sachita nawo. 15  Iye sadya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano mʼmapiri. Sadalira mafano onyansa a nyumba ya Isiraeli ndipo sagona ndi mkazi wa mnzake. 16  Sazunza munthu aliyense. Satenga chikole ndipo salanda chilichonse mwauchifwamba. Munthu wanjala amamupatsa chakudya ndipo munthu wamaliseche amamuphimba ndi chovala. 17  Iye amapewa kupondereza munthu wosauka, sakongoza zinthu mwa katapira ndipo sauza anthu kuti apereke chiwongoladzanja. Amatsatira zigamulo zanga komanso kuyenda motsatira malamulo anga. Munthu wotere sadzafa chifukwa cha zolakwa za bambo ake. Iye adzapitiriza kukhala ndi moyo ndithu. 18  Koma popeza kuti bambo akewo ankachita zachinyengo, ankabera mʼbale wawo mwauchifwamba ndipo ankachita zinthu zoipa pakati pa anthu a mtundu wawo, iwo adzafa chifukwa cha zolakwa zawo. 19  Koma mudzanena kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwanayo alibe mlandu uliwonse pa zolakwa za bambo akewo?” Popeza kuti mwanayo anachita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo, anasunga malamulo anga onse komanso kuwatsatira, ndithu iye adzapitiriza kukhala ndi moyo.+ 20  Moyo umene ukuchimwawo ndi umene udzafe.*+ Mwana sadzakhala ndi mlandu uliwonse pa zolakwa za bambo ake ndipo bambo sadzakhala ndi mlandu uliwonse pa zolakwa za mwana wake. Munthu wolungama adzaweruzidwa yekha mogwirizana ndi zinthu zachilungamo zimene amachita, ndipo munthu woipa adzaweruzidwa yekha mogwirizana ndi zinthu zoipa zimene amachita.+ 21  Koma ngati munthu woipa wasiya kuchita machimo ake onse amene ankachita ndipo akusunga malamulo anga nʼkumachita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo, ndithu iye adzapitiriza kukhala ndi moyo. Sadzafa ayi.+ 22  Iye sadzalangidwa chifukwa cha zolakwa zonse zimene anachita.*+ Adzapitiriza kukhala ndi moyo chifukwa chochita zinthu zolungama.’+ 23  ‘Kodi ine ndimasangalala ndi imfa ya munthu wochimwa?+ Kodi zimene ine ndimafuna si zoti munthu wochimwayo alape nʼkupitiriza kukhala ndi moyo?’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 24  ‘Munthu amene amachita zinthu zabwino akasiya kuchita zabwinozo nʼkumachita zoipa,* akamachita zinthu zonse zonyansa zimene munthu woipa amachita, kodi angapitirize kukhala ndi moyo? Zinthu zabwino zimene ankachita sizidzakumbukiridwa.+ Iye adzafa chifukwa chochita zinthu mosakhulupirika ndiponso chifukwa cha machimo ake amene anachita.+ 25  Koma inu mudzanena kuti: “Njira za Yehova nʼzopanda chilungamo.”+ Tamverani inu a nyumba ya Isiraeli. Kodi njira zanga nʼzimene zili zopanda chilungamo?+ Kodi njira zanu si zimene zili zopanda chilungamo?+ 26  Munthu amene amachita zinthu zabwino akasiya kuchita zabwinozo nʼkumachita zoipa,* nʼkufa chifukwa cha zochita zakezo, adzakhala kuti wafa chifukwa cha zoipa zake. 27  Ndipo ngati munthu woipa wasiya kuchita zinthu zoipa zimene ankachita nʼkuyamba kuchita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo, iye adzapulumutsa moyo wake.+ 28  Munthu woipayo akazindikira kuti zimene akuchita ndi zoipa nʼkusiya kuchita zoipazo, ndithu iye adzapitiriza kukhala ndi moyo. Sadzafa ayi. 29  Koma nyumba ya Isiraeli idzanena kuti: “Njira za Yehova nʼzopanda chilungamo.” Kodi nʼzoona kuti njira zanga nʼzimene zili zopanda chilungamo, inu a nyumba ya Isiraeli?+ Kodi njira zanu si zimene zili zopanda chilungamo?’ 30  ‘Choncho ine ndidzaweruza aliyense wa inu mogwirizana ndi njira zake,+ inu a nyumba ya Isiraeli,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Lapani ndipo musiyiretu zolakwa zanu zonse kuti zisakhale chinthu chokupunthwitsani chimene chingachititse kuti mukhale ndi mlandu. 31  Siyani zolakwa zanu zonse zimene munkachita+ ndipo mukhale ndi mtima watsopano* komanso mzimu watsopano.+ Kodi muferenji+ inu a nyumba ya Isiraeli?’ 32  ‘Inetu sindisangalala ndi imfa ya munthu aliyense,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Choncho siyani kuchita zoipa kuti mupitirize kukhala ndi moyo.’”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Munthu amene wachimwa ndi amene adzafe.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Kapena kuti, “Munthu amene akuchimwayo ndi amene adzafe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Zolakwa zake sizidzakumbukiridwa.”
Kapena kuti, “nʼkumachita zopanda chilungamo.”
Kapena kuti, “nʼkumachita zopanda chilungamo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo mudzipangire mtima watsopano.”