Ezekieli 19:1-14

  • Nyimbo yoimba polira yokhudza atsogoleri a Isiraeli (1-14)

19  “Ukuyenera kuimba nyimbo yoimba polira yokhudza atsogoleri a Isiraeli.  Unene kuti,‘Kodi mayi anu anali ngati ndani? Anali ngati mkango waukazi pakati pa mikango ina. Ankagona pakati pa mikango yamphamvu,* nʼkumalera ana ake.   Mkangowo unalera mwana wake wina ndipo mwanayo anakula nʼkukhala mkango wamphamvu.+ Anaphunzira kupha nyamaNdipo anayamba kudya ngakhale anthu.   Mitundu ya anthu inamva za mwana wa mkangoyo ndipo inakumba dzenje limene anagweramo,Kenako anamukola ndi ngowe nʼkupita naye ku Iguputo.+   Mkango waukazi uja unadikira koma patapita nthawi unaona kuti palibe chiyembekezo chakuti mwanayo adzabwereranso. Choncho unatenga mwana wake wina nʼkumutumiza ngati mkango wamphamvu.   Mkangowo unayambanso kuyendayenda pakati pa mikango ina ndipo unakhala mkango wamphamvu. Unaphunzira kupha nyama ndipo unayamba kudya ngakhale anthu.+   Mkangowo unkasaka nyama pakati pa nsanja zawo zokhala ndi mipanda yolimba ndipo unawononga mizinda yawo.Moti mʼdziko labwinjalo munkangomveka kubangula kwa mkangowo.+   Mitundu ya anthu imene inkakhala mʼzigawo zozungulira inabwera kudzauukira ndipo inautchera ukonde,Mkangowo unagwera mʼdzenje lawo.   Kenako anaukola ndi ngowe nʼkuuika mʼkakhola ndipo anapita nawo kwa mfumu ya Babulo. Atafika nawo anautsekera kuti mawu ake asadzamvekenso mʼmapiri a ku Isiraeli. 10  Mayi anu anali ngati mtengo wa mpesa*+ umene unadzalidwa mʼmphepete mwa madzi. Mtengowo unabereka zipatso ndipo unali ndi nthambi zambiri chifukwa unali pamadzi ambiri. 11  Nthambi* za mtengowo zinakhala zolimba, zoyenera kupangira ndodo za olamulira. Mtengowo unakula nʼkutalika kwambiri kuposa mitengo ina,Ndipo unkaonekera patali chifukwa cha kutalika kwake ndiponso kuchuluka kwa masamba ake. 12  Koma mtengowo unazulidwa mwaukali+ nʼkuponyedwa pansi,Ndipo mphepo yakumʼmawa inaumitsa zipatso zake. Nthambi zake zimene zinali zolimba zinathyoledwa nʼkuuma+ ndipo zinawotchedwa ndi moto.+ 13  Tsopano mtengo wa mpesawo wadzalidwa mʼchipululu,Mʼdziko lopanda madzi komanso louma.+ 14  Motowo unafalikira kuchokera kunthambi* zake ndipo unawotcha mphukira ndi zipatso zake,Ndipo mtengowo unalibenso nthambi zolimba komanso ndodo ya olamulira.+ Imeneyi ndi nyimbo yoimba polira ndipo idzakhala nyimbo yotchuka.’”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mikango yaingʼono yamanyenje.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mtengo wa mpesa umene uli mʼmagazi anu.”
Kapena kuti, “Ndodo.”
Kapena kuti, “kundodo.”