Ezekieli 2:1-10

  • Ezekieli anamupatsa ntchito ya uneneri (1-10)

    • ‘Kaya akamvetsera kapena ayi’ (5)

    • Anamuonetsa mpukutu wa nyimbo zoimba polira (9, 10)

2  Kenako iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu,* imirira kuti ndikulankhule.”+  Atalankhula nane, mzimu unalowa mwa ine ndipo unandipangitsa kuti ndiimirire+ kuti ndizitha kumva zomwe amene ankalankhula ndi ineyo ankanena.  Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, ndikukutumiza kwa Aisiraeli,+ ku mitundu ya anthu amene andipandukira.+ Iwo ndi makolo awo akhala akuphwanya malamulo anga mpaka lero.+  Ndikukutumiza kwa ana osamvera komanso ouma mtima+ ndipo ukawauze kuti, ‘Izi nʼzimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena.’  Kaya akamvetsera kapena ayi, popeza iwo ndi anthu opanduka,+ adzadziwabe ndithu kuti pakati pawo panali mneneri.+  Koma iwe mwana wa munthu, usawaope+ ndipo usachite mantha ndi zimene akunena ngakhale kuti wazunguliridwa ndi anthu amene ali ngati minga*+ komanso ukukhala pakati pa zinkhanira. Usachite mantha ndi zimene akunena+ ndipo usaope nkhope zawo,+ chifukwa iwo ndi anthu opanduka.  Ukawauze mawu anga, kaya akamvetsera kapena ayi, chifukwa iwo ndi anthu opanduka.+  Koma iwe mwana wa munthu, mvetsera zimene ndikukuuza. Usapanduke ngati anthu opandukawa. Tsegula pakamwa pako kuti udye zimene ndikukupatsa.”+  Nditayangʼana, ndinaona dzanja litatambasukira kwa ine.+ Mʼdzanjalo munali mpukutu wolembedwa.+ 10  Atautambasula, ndinaona kuti mpukutuwo unali wolembedwa kumbali zonse.+ Mumpukutumo munalembedwa nyimbo zoimba polira, mawu odandaula ndi mawu olira.+

Mawu a M'munsi

Amenewa ndi malo oyamba pa malo 93 pamene mawu amenewa akupezeka mʼbuku la Ezekieli.
Mabaibulo ena amati, “ngakhale kuti ndi anthu osamva ndipo ali ngati zinthu zokulasa.”