Ezekieli 22:1-31

  • Yerusalemu, mzinda wa mlandu wokhetsa magazi (1-16)

  • Isiraeli ali ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga zitsulo (17-22)

  • Anadzudzula atsogoleri komanso anthu a mu Isiraeli (23-31)

22  Yehova analankhulanso nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, kodi ndiwe wokonzeka kupereka uthenga wachiweruzo kwa mzinda* umene uli ndi mlandu wa magaziwu+ komanso kuudziwitsa zonyansa zake zonse?+  Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe mzinda umene uli ndi mlandu wokhetsa magazi,+ umene nthawi yako yoti uweruzidwe ikubwera,+ umenenso umapanga mafano onyansa* kuti udzidetse nawo,+  magazi amene wakhetsa apangitsa kuti ukhale ndi mlandu+ ndipo mafano ako onyansa apangitsa kuti ukhale wodetsedwa.+ Wafupikitsa masiku a moyo wako ndipo ulangidwa posachedwapa. Nʼchifukwa chake ndachititsa kuti anthu a mitundu ina azikunyoza komanso kuti anthu amʼmayiko onse azikuseka.+  Mayiko amene uli nawo pafupi ndiponso amene ali kutali ndi iwe adzakuseka,+ iwe amene dzina lako ndi lodetsedwa komanso uli ndi mavuto ambiri.  Taona! Mtsogoleri aliyense wa Isiraeli pakati pako akugwiritsa ntchito udindo wake kuti akhetse magazi.+  Mwa iwe muli anthu amene amanyoza bambo awo komanso mayi awo.+ Mlendo amamuchitira zinthu mwachinyengo ndipo amazunza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.”’”+  “‘Iwe wanyoza malo anga oyera ndipo wadetsa sabata langa.+  Mwa iwe muli anthu amiseche amene amafuna kukhetsa magazi.+ Mulinso anthu amene amadya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano mʼmapiri ndipo amachita khalidwe lonyansa pakati panu.+ 10  Mwa iwe muli anthu amene salemekeza pogona pa bambo awo*+ ndipo amakakamiza mkazi wodetsedwa amene akusamba kuti agone naye.+ 11  Mwa iwe muli munthu amene amachita zonyansa ndi mkazi wa mnzake.+ Wina amadetsa mpongozi wake wamkazi pochita naye khalidwe lonyansa+ ndipo wina amagona ndi mchemwali wake, mwana wamkazi wa bambo ake enieni.+ 12  Mwa iwe muli anthu amene akulandira ziphuphu kuti akhetse magazi.+ Iwe ukabwereketsa ndalama umafuna kuti akupatse chiwongoladzanja+ kapena kuti upeze phindu* ndipo ukubera anzako ndalama mwachinyengo.+ Ndithu, ine wandiiwaliratu,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 13  ‘Ine ndawomba mʼmanja chifukwa chonyansidwa ndi phindu lachinyengo limene wapeza komanso chifukwa cha magazi amene anakhetsedwa pakati pako. 14  Kodi udzapitiriza kukhala wolimba mtima ndipo kodi dzanja lako lidzakhalabe lamphamvu pa tsiku limene ndidzakulange?+ Ine Yehova ndanena ndipo ndidzachitapo kanthu. 15  Anthu ako ndidzawabalalitsira ku mitundu ina ya anthu ndipo ndidzawamwaza mʼmayiko osiyanasiyana.+ Komanso ndidzathetsa khalidwe lako lonyansa.+ 16  Udzanyozeka pamaso pa mitundu ina ya anthu ndipo udzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+ 17  Yehova anandiuzanso kuti: 18  “Iwe mwana wa munthu, kwa ine nyumba ya Isiraeli yakhala ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga zitsulo. Onse ali ngati kopa,* tini, chitsulo ndi mtovu zimene zili mungʼanjo. Iwo akhala ngati zinthu zimene zimatsalira akayenga siliva.+ 19  Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chifukwa chakuti nonsenu mwakhala ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga zitsulo,+ ine ndikusonkhanitsani pamodzi mu Yerusalemu. 20  Ndidzakusonkhanitsani pamodzi ngati mmene amasonkhanitsira siliva, kopa, chitsulo, mtovu ndi tini mungʼanjo kuti azikolezere moto nʼkuzisungunula. Ndidzachita zimenezi nditakwiya komanso mwaukali ndipo ndidzakukolezerani moto nʼkukusungunulani.+ 21  Ndidzakusonkhanitsani pamodzi nʼkukukolezerani moto wa mkwiyo wanga,+ ndipo mudzasungunuka mumzindawo.+ 22  Mofanana ndi siliva amene amamusungunulira mungʼanjo, inenso ndidzakusungunulirani mumzindawo. Choncho mudzadziwa kuti ine Yehova ndadzakukhuthulirani mkwiyo wanga.’” 23  Yehova anandiuzanso kuti: 24  “Iwe mwana wa munthu, uza dzikoli kuti, ‘Iwe ndi dziko limene silidzayeretsedwa ndipo mwa iwe simudzagwa mvula pa tsiku limene ndidzakusonyeze mkwiyo wanga. 25  Aneneri ako akukonza chiwembu mʼdzikoli.+ Iwo ali ngati mkango wobangula umene wagwira nyama+ ndipo akupha anthu. Akulanda anthu chuma ndi zinthu zawo zamtengo wapatali. Apangitsa kuti akazi amasiye achuluke mʼdzikolo. 26  Ansembe ako aphwanya chilamulo changa+ ndipo akupitiriza kuipitsa malo anga oyera.+ Sakusiyanitsa zinthu zoyera ndi zinthu wamba+ ndipo akulephera kuuza anthu kuti zinthu zodetsedwa ndi ziti komanso zinthu zoyera ndi ziti.+ Iwo akukana kusunga sabata langa ndipo adetsa dzina langa pakati pawo. 27  Akalonga amʼdzikoli ali ngati mimbulu yomwe ikukhadzula nyama. Iwo akukhetsa magazi ndiponso kupha anthu nʼcholinga chopeza phindu mwachinyengo.+ 28  Koma aneneri amʼdzikomo apaka laimu zochita za akalongawo. Iwo amaona masomphenya onama ndipo amalosera zinthu zabodza.+ Aneneriwo amanena kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti,” pamene Yehova sananene chilichonse. 29  Anthu amʼdzikolo abera anthu mwachinyengo komanso achita zauchifwamba.+ Iwo achitira nkhanza anthu ovutika ndi osauka. Abera mlendo mwachinyengo komanso sanamuchitire zinthu mwachilungamo.’ 30  ‘Ndinafunafuna munthu pakati pawo amene angathe kukonzanso mpanda wamiyala kapena kuima pamalo ogumuka a mpandawo kuti ateteze dzikolo nʼcholinga choti ine ndisaliwononge,+ koma sindinapeze aliyense. 31  Choncho ndidzawakhuthulira mkwiyo wanga ndipo ndidzawawononga onse ndi moto wa ukali wanga. Ndidzawalanga mogwirizana ndi zochita zawo,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “kodi uweruza, kodi uweruza mzinda.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “amavula bambo awo.”
Kapena kuti, “akupatse katapira.”
Kapena kuti, “mkuwa.”