Ezekieli 23:1-49

  • Akazi awiri apachibale omwe ndi osakhulupirika (1-49)

    • Ohola ndi Asuri (5-10)

    • Oholiba ndi Babulo komanso Iguputo (11-35)

    • Chilango chimene akazi awiriwo analandira (36-49)

23  Yehova anandiuzanso kuti:  “Iwe mwana wa munthu, panali akazi awiri amene anali ana a mayi mmodzi.+  Akazi amenewa anayamba kuchita uhule mʼdziko la Iguputo.+ Anayamba uhulewu ali atsikana angʼonoangʼono. Kumeneko amuna anafinya mabere awo komanso kusisita pamtima pawo ali anamwali.  Wamkulu dzina lake anali Ohola,* wamngʼono anali Oholiba.* Akazi amenewa anakhala anga ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi. Ohola akuimira Samariya+ ndipo Oholiba akuimira Yerusalemu.  Ohola anayamba kuchita uhule+ ngakhale kuti anali mkazi wanga. Ankalakalaka kugona ndi amuna amene ankamukonda kwambiri+ omwe ndi Asuri amene ankakhala moyandikana naye.+  Amunawo anali abwanamkubwa amene ankavala zovala zabuluu ndiponso achiwiri kwa olamulira. Onsewa anali anyamata osiririka, akatswiri okwera mahatchi.  Iye anapitiriza kuchita uhule ndi amuna onse olemekezeka amʼdziko la Asuri ndipo anadziipitsa+ ndi mafano onyansa* a amuna amene ankawalakalakawo.  Iye sanasiye uhule umene ankachita ali ku Iguputo. Aiguputowo ankagona naye kuyambira ali kamtsikana. Iwo ankasisita pamtima pake ali namwali ndipo ankachita naye zachiwerewere.+  Choncho ndinamʼpereka mʼmanja mwa anthu amene ankamukonda kwambiri, omwe ndi amuna amʼdziko la Asuri+ amene ankalakalaka kugona naye. 10  Amunawo anamuvula,+ anagwira ana ake aamuna ndi aakazi+ ndipo iyeyo anamupha ndi lupanga. Iye anatchuka ndi khalidwe loipa pakati pa akazi ena ndipo anapatsidwa chilango. 11  Mchemwali wake Oholiba ataona zimenezi, chilakolako chake chinafika poipa kwambiri ndipo uhule wake unafika poipa kuposa wa mkulu wake.+ 12  Iye ankalakalaka kwambiri kugona ndi amuna amʼdziko la Asuri+ omwe anayandikana nawo. Amuna amenewa anali abwanamkubwa ndi achiwiri kwa olamulira amene ankavala zovala zokongola ndipo anali akatswiri okwera mahatchi. Onsewa anali anyamata osiririka. 13  Oholiba atadziipitsa, ine ndinaona kuti akazi awiri onsewa anali ndi khalidwe lofanana.+ 14  Koma iye anapitiriza kuwonjezera zochita zake zauhule. Iye anaona zithunzi za amuna zogoba pakhoma, zithunzi zogoba za Akasidi zopaka penti yofiira. 15  Anaona zithunzi za amuna atavala malamba mʼchiuno ndipo kumutu kwawo anavala nduwira zazitali zolendewera. Amuna onsewo ankaoneka ngati asilikali komanso ngati amuna a ku Babulo, obadwira mʼdziko la Akasidi. 16  Ataona zithunzizo, anayamba kulakalaka kwambiri kugona ndi amunawo ndipo anatumiza anthu ku Kasidi+ kuti akawaitane. 17  Choncho amuna a ku Babulowo ankabwera pabedi pake nʼkumachita zachikondi ndipo anamuipitsa ndi chiwerewere chawo. Amunawo atamuipitsa, iye anawasiya chifukwa anayamba kunyansidwa nawo. 18  Oholiba atapitiriza kuchita uhule mopanda manyazi komanso kudzivula,+ ine ndinamusiya chifukwa chonyansidwa naye, ngati mmene ndinasiyira mchemwali wake chifukwa chonyansidwa naye.+ 19  Oholiba anapitiriza kuwonjezera zochita zake zauhule+ mpaka kufika pokumbukira masiku amene anali kamtsikana, pamene ankachita uhule mʼdziko la Iguputo.+ 20  Iye ankalakalaka kugona ndi anthu amene ankawakonda mofanana ndi adzakazi* amene amuna awo ali ndi ziwalo ngati za abulu amphongo komanso ngati ziwalo za mahatchi amphongo. 21  Iwe unkalakalaka khalidwe lonyansa limene unkachita ku Iguputo+ uli kamtsikana pamene amuna ankasisita mabere ako.+ 22  Choncho iwe Oholiba, Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ndichititsa kuti amuna omwe unkawakonda,+ amene unawasiya chifukwa chonyansidwa nawo akuukire. Ndidzawabweretsa kuchokera kumbali zonse kuti adzakuukire.+ 23  Ndidzabweretsa amuna a ku Babulo,+ Akasidi onse,+ amuna a ku Pekodi,+ a ku Sowa, a ku Kowa pamodzi ndi amuna onse amʼdziko la Asuri. Onsewa ndi anyamata osiririka, abwanamkubwa, achiwiri kwa olamulira, asilikali komanso amuna osankhidwa mwapadera.* Onsewa ndi akatswiri okwera mahatchi. 24  Iwo adzabwera kudzakuukira ndipo akamadzabwera, padzamveka phokoso la magaleta ankhondo ndi la mawilo. Adzabwera ndi gulu lalikulu la asilikali, atatenga zishango zazikulu, zishango zazingʼono ndiponso atavala zipewa. Iwo adzakuzungulira ndipo ndidzawapatsa mphamvu zoweruza, moti adzakuweruza mmene akufunira.+ 25  Ndidzasonyeza mkwiyo wanga pa iwe ndipo iwo adzakulanga mwaukali. Adzakudula mphuno ndi makutu ndipo ena a inu amene adzatsale adzaphedwa ndi lupanga. Iwo adzatenga ana ako aamuna ndi aakazi ndipo anthu ena amene adzatsale adzawotchedwa ndi moto.+ 26  Adzakuvula zovala zako+ ndipo adzatenga zinthu zako zodzikongoletsera.+ 27  Ine ndidzathetsa khalidwe lako lonyansa ndiponso uhule wako+ umene unauyambira mʼdziko la Iguputo.+ Udzasiya kuyangʼana amuna a ku Iguputo ndipo dziko la Iguputo sudzalikumbukiranso.’ 28  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ndatsala pangʼono kukupereka mʼmanja mwa amuna amene ukudana nawo, amuna amene unawasiya chifukwa chonyansidwa nawo.+ 29  Iwo adzakuchitira zinthu zosonyeza kuti amadana nawe ndipo adzatenga zinthu zonse zimene unazipeza movutikira+ nʼkukusiya wosavala ndi wamaliseche. Umaliseche umene unauonetsa pochita chiwerewere, khalidwe lako lonyansa ndiponso uhule wako zidzaonekera poyera.+ 30  Adzakuchitira zimenezi chifukwa chakuti unkalakalaka anthu a mitundu ina ngati hule+ komanso chifukwa chakuti unadziipitsa ndi mafano awo onyansa.+ 31  Iwe wachita zinthu zofanana ndi zimene mchemwali wako anachita+ ndipo ndidzakupatsa kapu yake.’+ 32  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Udzamwa zamʼkapu ya mkulu wako, yomwe ndi yaitali komanso yaikulu.+Ndipo anthu azidzakuseka komanso kukunyoza chifukwa mʼkapumo muli zambiri.+ 33  Udzaledzera kwambiri ndipo udzakhala ndi chisoni.Udzaledzera ndi zinthu zamʼkapu ya mchemwali wako Samariya,Zinthu zochititsa mantha kwambiri komanso zowononga. 34  Iwe udzamwa ndi kugugudiza zamʼkapuyo+ ndipo udzatafuna zidutswa za kapuyoKenako udzakhadzula mabere ako. “Ine ndanena,” akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’ 35  Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chifukwa chakuti wandiiwala ndipo sukundilabadiranso,*+ udzalangidwa chifukwa cha khalidwe lako lonyansa ndi zochita zako zauhule.’” 36  Kenako Yehova anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ndiwe wokonzeka kupereka uthenga wachiweruzo kwa Ohola ndi Oholiba+ komanso kuwauza zinthu zonyansa zimene achita? 37  Iwo achita chigololo*+ ndipo mʼmanja mwawo muli magazi. Kuwonjezera pa kuchita chigololo ndi mafano awo onyansa, iwo awotcha pamoto ana awo aamuna amene anandiberekera kuti akhale chakudya cha mafano awowo.+ 38  Komanso anandichitira zinthu izi: Pa tsikulo anaipitsa malo anga opatulika ndiponso sabata langa. 39  Atapha ana awo aamuna nʼkuwapereka nsembe kwa mafano onyansa,+ tsiku lomwelo anabwera kumalo anga opatulika kudzawadetsa.+ Izi ndi zimene anachita mʼnyumba yanga. 40  Kuwonjezera apo, akaziwo anatumiza uthenga kwa amuna ochokera kutali kuti abwere.+ Amunawo akubwera, iwe unasamba nʼkupaka zodzikongoletsera mʼmaso mwako ndipo unavala zodzikongoletsera.+ 41  Kenako unakhala pampando wabwino kwambiri+ ndipo patsogolo pake panali tebulo loyalidwa bwino.+ Patebulopo unaikapo zofukiza zanga zonunkhira+ komanso mafuta anga.+ 42  Kumeneko kunamveka phokoso la gulu la anthu amene akucheza mosangalala. Pagulu limeneli panalinso zidakwa zimene anazibweretsa kuchokera kuchipululu. Amuna amenewa anaveka akaziwo zibangili ndi zipewa zachifumu zokongola kumutu kwawo. 43  Kenako ndinalankhula zokhudza mkazi amene anali atatoperatu chifukwa cha chigololo kuti: ‘Komabe apitiriza kuchita uhule.’ 44  Choncho amuna aja anapitiriza kupita kwa iye ngati mmene amuna amapitira kwa hule. Umu ndi mmene ankapitira kwa Ohola ndi Oholiba, akazi akhalidwe lonyansa. 45  Koma amuna olungama adzamupatsa chiweruzo choyenera chimene amapereka kwa munthu wachigololo+ komanso wokhetsa magazi.+ Chifukwa iwowa ndi akazi achigololo ndipo mʼmanja mwawo muli magazi.+ 46  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Adzawabweretsera gulu la asilikali kuti lidzawaukire nʼkuwasandutsa chinthu chochititsa mantha komanso chinthu choyenera kutengedwa ndi adani.+ 47  Asilikaliwo adzawagenda ndi miyala+ nʼkuwapha ndi malupanga. Adzaphanso ana awo aamuna ndi aakazi+ ndipo adzawotcha nyumba zawo.+ 48  Ndidzathetsa khalidwe lonyansa mʼdzikoli ndipo akazi onse adzaphunzirapo kanthu, moti sadzatengera khalidwe lanu lonyansa.+ 49  Asilikaliwo adzakulangani chifukwa cha khalidwe lanu lonyansa komanso machimo amene munachita ndi mafano anu onyansa, ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’”+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza, “Tenti Yanga Ili mwa Iye.”
Kutanthauza, “Tenti Yake.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “oitanidwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wandiponya kumbuyo.”
Kutanthauza kuti anachita chigololo polambira mafano.