Ezekieli 24:1-27
24 Yehova analankhulanso nane mʼchaka cha 9, mʼmwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, lemba deti lalero,* ulembe tsiku lalero. Lero mfumu ya Babulo yayamba kuukira mzinda wa Yerusalemu.+
3 Nena mwambi wokhudza anthu opanduka. Unene zokhudza anthu amenewa kuti:
‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Ika mphika* pamoto ndipo uthiremo madzi.+
4 Uikemo nthuli za nyama,+ nthuli zabwinozabwino.Uikemo mwendo wamʼmbuyo ndi wakutsogolo. Udzazemo mafupa abwino kwambiri.
5 Tenga nkhosa yabwino kwambiri+ ndipo usonkhezere nkhuni kuzungulira mphikawo.
Uwiritse nthuli za nyamazo limodzi ndi mafupa amene ali mumphikawo.”’
6 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
‘Tsoka mzinda wokhetsa magazi,+ umene uli ngati mphika wadzimbiri, womwe dzimbiri lakelo silikuchoka.
Muchotsemo nthulizo imodziimodzi.+ Musachite maere pa nthulizo.
7 Chifukwa magazi amene mzindawo wakhetsa ali mkati mwake.+ Wathira magaziwo pathanthwe lopanda chilichonse.
Mzindawo sunathire magaziwo pansi kuti uwakwirire ndi dothi.+
8 Ine ndathira magazi amene mzindawo wakhetsa pathanthwe lopanda chilichonseKuti asakwiriridwe.+Ndachita zimenezi kuti mkwiyo wanga uyakire mzindawo nʼkuulanga chifukwa cha zochita zake.’
9 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
‘Tsoka mzinda wokhetsa magazi!+
Ine ndidzaunjika mulu waukulu wa nkhuni.
10 Sonkhanitsani zikuni zambiri nʼkukoleza moto,Wiritsani nyamayo mpaka ipse. Khuthulani msuzi wake ndipo mafupawo muwasiye kuti apserere.
11 Ikani mphika wakopa* wopanda kanthu pamakala amoto kuti utenthe kwambiriNdipo ufiire chifukwa cha kutentha.
Zonyansa zake zisungunukemo+ ndipo dzimbiri lake lipse ndi motowo.
12 Ntchito yake ndi yaikulu komanso yotopetsa,Chifukwa dzimbiri lake, lomwe ndi lambiri, silikuchoka.+
Uponyeni pamoto ndi dzimbiri lakelo.’
13 ‘Ndiwe wodetsedwa chifukwa cha khalidwe lako lonyansa.+ Ine ndinayesa kukuyeretsa, koma sunayere chifukwa zonyansa zako sizinachoke. Sudzayera mpaka mkwiyo wanga utatha.+
14 Ine Yehova ndanena ndipo zidzachitikadi. Ndidzachitapo kanthu mosazengereza, popanda kumva chisoni kapena kusintha maganizo.+ Iwo adzakuweruza mogwirizana ndi njira zako komanso zochita zako,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
15 Yehova analankhulanso nane kuti:
16 “Iwe mwana wa munthu, ine ndichititsa kuti mkazi wako afe mwadzidzidzi.+ Koma iwe usamve chisoni,* kulira kapena kugwetsa misozi.
17 Ulire mosatulutsa mawu ndipo usachite miyambo yamaliro.+ Uvale nduwira kumutu+ ndipo uvale nsapato zako.+ Usaphimbe ndevu zako zapamlomo+ ndipo usadye chakudya chimene anthu angakupatse.”+
18 Mʼmawa ndinalankhula ndi anthu ndipo madzulo, mkazi wanga anamwalira. Choncho mʼmawa wa tsiku lotsatira ndinachita zonse zimene anandilamula.
19 Anthu ankandifunsa kuti: “Kodi sutiuza kuti zimene ukuchitazi zikutikhudza bwanji?”
20 Ine ndinawayankha kuti: “Yehova wandiuza kuti,
21 ‘Uza nyumba ya Isiraeli kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndatsala pangʼono kudetsa malo anga opatulika,+ chinthu chimene mumachinyadira kwambiri, chinthu chimene mumachikonda komanso chapamtima panu. Ana anu aamuna ndi aakazi amene munawasiya mumzindawo adzaphedwa ndi lupanga.+
22 Zikadzatero inu mudzachita zimene ine ndachita. Simudzaphimba ndevu zanu zapamlomo ndipo simudzadya chakudya chimene anthu adzakupatseni.+
23 Mudzavala nduwira zanu ndiponso nsapato zanu. Simudzamva chisoni kapena kulira pagulu. Mʼmalomwake, mudzavutika chifukwa cha zolakwa zanu+ ndipo mudzalira mosatulutsa mawu.
24 Ezekieli wakhala chizindikiro kwa inu.+ Mudzachita zonse zimene iye wachita. Tsokali likadzakugwerani, mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’”’”
25 “Koma iwe mwana wa munthu, pa tsiku limene ndidzawachotsere mpanda wawo wolimba, chinthu chokongola chimene chimawasangalatsa, chinthu chimene amachikonda komanso chapamtima pawo, limodzi ndi ana awo aamuna ndi aakazi,+
26 munthu amene wapulumuka adzabwera kwa iwe nʼkudzakuuza zimene zachitika.+
27 Pa tsiku limenelo udzatsegula pakamwa pako nʼkulankhula ndi munthu amene wapulumukayo ndipo sudzakhalanso chete.+ Iwe udzakhala chizindikiro kwa iwo, ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”