Ezekieli 25:1-17

  • Ulosi wokhudza Amoni (1-7)

  • Ulosi wokhudza Mowabu (8-11)

  • Ulosi wokhudza Edomu (12-14)

  • Ulosi wokhudza Filisitiya (15-17)

25  Yehova anandiuzanso kuti:  “Iwe mwana wa munthu, yangʼana kwa Aamoni+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzawachitikire.+  Uuze Aamoniwo kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inu munanena kuti ‘Eyaa! Zakhala bwino.’ Munanena zimenezi malo anga opatulika atadetsedwa, dziko la Isiraeli litasanduka bwinja komanso nyumba ya Yuda itatengedwa kupita ku ukapolo.  Pa chifukwa chimenechi, ndikuperekani kwa anthu a Kumʼmawa kuti mukhale chuma chawo. Iwo adzamanga misasa yokhala ndi mipanda komanso adzakhoma matenti awo mʼdziko lanu. Adzadya zokolola zanu ndipo adzamwa mkaka wa ziweto zanu.  Mzinda wa Raba+ ndidzausandutsa malo odyetserako ngamila, ndipo dziko la Aamoni ndidzalisandutsa malo opumilako ziweto ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chifukwa chakuti munawomba mʼmanja+ ndi kuponda pansi mwamphamvu, komanso munasangalala monyoza poona zimene zinachitikira dziko la Isiraeli,+  ine nditambasula dzanja langa nʼkukulangani ndipo ndikuperekani kwa anthu a mitundu ina kuti akutengeni. Ndidzakuwonongani kuti musakhalenso mtundu wa anthu ndipo ndidzakuchotsani pakati pa mayiko ena.+ Ndidzakufafanizani ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chifukwa chakuti Mowabu+ ndi Seiri+ anena kuti, “Taonani! Nyumba ya Yuda ili ngati mitundu ina yonse ya anthu,”  ine ndidzachititsa kuti adani aukire mizinda imene ili mʼmalire mwa Mowabu,* kuphatikizapo mizinda yake yabwino kwambiri.* Mizindayo ndi Beti-yesimoti, Baala-meoni mpaka kukafika ku Kiriyataimu.+ 10  Ndidzapereka Mowabu limodzi ndi Aamoni kwa anthu a Kumʼmawa+ kuti akhale chuma chawo. Ndidzachita zimenezi kuti Aamoni asadzakumbukiridwenso pakati pa mitundu ya anthu.+ 11  Ndidzapereka chiweruzo mʼdziko la Mowabu+ ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’ 12  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Edomu wabwezera zoipa kwa nyumba ya Yuda ndipo wapalamula mlandu waukulu chifukwa chowabwezera.+ 13  Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Nditambasulanso dzanja langa nʼkulanga Edomu ndipo ndipha anthu ndi ziweto mʼdzikolo, moti ndidzalisandutsa bwinja.+ Anthu adzaphedwa ndi lupanga kuyambira ku Temani mpaka ku Dedani.+ 14  ‘Ine ndidzabwezera Edomu pogwiritsa ntchito anthu anga Aisiraeli.+ Aisiraeliwo adzachitira Edomu mogwirizana ndi mkwiyo komanso ukali wanga, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndikuwabwezera,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’ 15  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Popeza Afilisiti akupitiriza kuchitira zoipa Aisiraeli chifukwa chodana nawo, iwo akufuna kubwezera komanso kuwononga Aisiraeliwo mwankhanza.*+ 16  Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikutambasula dzanja langa kuti ndilange Afilisiti,+ ndipo ndidzapha Akereti+ nʼkuwononga anthu onse omwe anatsala, amene amakhala mʼmbali mwa nyanja.+ 17  Anthu amenewa ndidzawachitira zinthu zopweteka powabwezera ndipo ndidzawalanga mwaukali. Ndikadzawalanga, adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mʼmalo otsetsereka a Mowabu.”
Kapena kuti, “mizinda imene imakongoletsa dzikolo.”
Kapena kuti, “moipidwa.”