Ezekieli 28:1-26

  • Ulosi wokhudza mfumu ya Turo (1-10)

    • “Ndine mulungu” (2, 9)

  • Nyimbo yoimba polira yokhudza mfumu ya Turo (11-19)

    • “Iwe unali mu Edeni” (13)

    • “Kerubi wodzozedwa amene amagwira ntchito yoteteza” (14)

    • “Unayamba kuchita zinthu zosalungama” (15)

  • Ulosi wokhudza Sidoni (20-24)

  • Isiraeli adzabwezeretsedwa mwakale (25, 26)

28  Yehova anandiuzanso kuti:  “Iwe mwana wa munthu, uza mtsogoleri wa Turo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Chifukwa chakuti wadzikuza mumtima mwako,+ ukumanena kuti, ‘Ndine mulungu. Ndakhala pampando wachifumu wa mulungu pakatikati pa nyanja.’+ Koma ndiwe munthu basi, osati mulungu,Ngakhale kuti mumtima mwako umadziona kuti ndiwe mulungu.   Iwe umaganiza kuti ndiwe wanzeru kuposa Danieli.+ Umaganiza kuti palibe chinsinsi chimene sukuchidziwa.   Chifukwa chakuti ndiwe wanzeru ndiponso wozindikira, walemera kwambiri,Ndipo ukupitiriza kusonkhanitsa golide ndi siliva mʼnyumba zako zosungiramo chuma.+   Luso lako pa malonda linakubweretsera chuma chochuluka,+Ndipo mtima wako unayamba kudzikuza chifukwa cha chuma chakocho.”’  ‘Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Chifukwa chakuti mumtima mwako umadziona kuti ndiwe mulungu,   Ine ndikubweretsa anthu ochokera mʼmayiko ena kuti adzakuukire, anthu ankhanza kwambiri a mitundu ina.+Iwo adzasolola malupanga awo nʼkuwononga chilichonse chokongola chimene unapeza chifukwa cha nzeru zakoNdipo adzaipitsa ulemerero wako waukulu.+   Iwo adzakutsitsira kudzenje,*Ndipo udzafa imfa yowawa pakatikati pa nyanja.+   Kodi amene adzakuphe udzamuuzabe kuti, ‘Ine ndine mulungu?’ Kwa anthu amene adzakuipitse, iwe udzakhala munthu wamba, osati mulungu.”’ 10  ‘Udzafa ngati anthu osadulidwa ndipo anthu amʼmayiko ena ndi amene adzakuphe,Ine ndanena,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” 11  Yehova anandiuzanso kuti: 12  “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira yokhudza mfumu ya Turo. Uuze mfumuyo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe unali chitsanzo changwiro,Unali ndi nzeru zochuluka+ ndiponso wokongola kwambiri.+ 13  Iwe unali mu Edeni, munda wa Mulungu. Unakongoletsedwa ndi miyala yamtengo wapatali yamitundu yonseMonga rube, topazi, yasipi, kulusolito, onekisi, yade, safiro, nofeki+ ndi emarodi.Zoikamo miyala imeneyi zinali zagolide. Ndinazipanga pa tsiku limene ndinakulenga. 14  Ine ndinakupatsa udindo kuti ukhale kerubi wodzozedwa amene amagwira ntchito yoteteza. Unkakhala paphiri loyera la Mulungu+ ndipo unkayendayenda pakati pa miyala yamoto. 15  Unali wopanda cholakwa pa zochita zako kuchokera pa tsiku limene unalengedwa,Mpaka pamene unayamba kuchita zinthu zosalungama.+ 16  Chifukwa cha kuchuluka kwa malonda amene unkachita,+Unayamba kuchita zachiwawa komanso machimo.+ Choncho ndidzakuchotsa mʼphiri la Mulungu nʼkukuponya kunja monga wodetsedwa ndipo ndidzakuwononga.+Iwe kerubi amene umagwira ntchito yoteteza, ndidzakuchotsa pakati pa miyala yamoto. 17  Mtima wako unadzikweza chifukwa cha kukongola kwako.+ Unawononga nzeru zako chifukwa cha ulemerero wako waukulu.+ Ndidzakuponyera kudziko lapansi,+ Ndipo mafumu azidzakuyangʼanitsitsa. 18  Iwe waipitsa malo ako opatulika chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zako komanso malonda ako opanda chilungamo. Ndidzachititsa kuti moto uyake pakati pako ndipo udzakupsereza.+ Ndidzakusandutsa phulusa padziko lapansi, pamaso pa anthu onse amene akukuyangʼana. 19  Onse amene ankakudziwa pakati pa mitundu ya anthu adzakuyangʼanitsitsa modabwa.+ Mapeto ako adzakhala odzidzimutsa komanso oopsa,Ndipo sudzakhalaponso mpaka kalekale.”’”+ 20  Yehova anandiuzanso kuti: 21  “Iwe mwana wa munthu, yangʼana ku Sidoni+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzamuchitikire. 22  Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe Sidoni, ine ndikupatsa chilango ndipo ndidzalemekezedwa pakati pako.Ndikadzapereka chiweruzo kwa iwe komanso ndikadzayeretsedwa kudzera mwa iwe, anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova. 23  Ndidzakutumizira mliri ndipo magazi adzayenderera mʼmisewu yako. Anthu ambiri adzaphedwa pakati pako lupanga likadzabwera kudzakuukira kuchokera kumbali zonse,Ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 24  Zikadzatero, nyumba ya Isiraeli sidzazunguliridwanso ndi anthu amene amawanyoza, omwe ali ngati zitsamba zobaya komanso minga zaululu.+ Ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’ 25  ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndikadzasonkhanitsanso pamodzi nyumba ya Isiraeli kuchokera kwa anthu a mitundu ina kumene anabalalikira,+ ndidzayeretsedwa pakati pawo pamaso pa mitundu ina ya anthu.+ Ndipo anthuwo adzakhala mʼdziko+ limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo.+ 26  Adzakhala mʼdzikolo motetezeka+ ndipo adzamanga nyumba komanso kulima minda ya mpesa.+ Iwo azidzakhala motetezeka ndikadzapereka chiweruzo kwa onse owazungulira amene amawanyoza.+ Ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wawo.”’”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mʼmanda.”