Ezekieli 29:1-21

  • Ulosi wokhudza Farao (1-16)

  • Babulo anapatsidwa Iguputo monga malipiro ake (17-21)

29  Mʼchaka cha 10, mʼmwezi wa 10, pa tsiku la 12 la mweziwo, Yehova anandiuza kuti:  “Iwe mwana wa munthu, yangʼana kwa Farao mfumu ya Iguputo ndipo ulosere zoipa zimene zidzachitikire iyeyo ndi dziko lonse la Iguputo.+  Umuuze kuti: ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikulanga iwe Farao mfumu ya Iguputo,+Iwe chilombo chachikulu chamʼnyanja chimene chagona mʼngalande zotuluka mumtsinje wake wa Nailo,+Ndipo wanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga. Ineyo ndinaupanga ndekha.’+   Koma ine ndidzakukola ndi ngowe munsagwada zako nʼkuchititsa kuti nsomba zamʼngalande za mtsinje wa Nailo zikakamire kumamba ako. Ndidzakutulutsa mumtsinje wako wa Nailo pamodzi ndi nsomba zonse zamumtsinje wa Nailo zimene zakakamira kumamba ako.   Iwe pamodzi ndi nsomba zonse zamumtsinje wa Nailo ndidzakutayani mʼchipululu. Mudzagwera panthaka yopanda chilichonse ndipo palibe amene adzakutengeni nʼkukakuikani mʼmanda.+ Ndidzakuperekani kwa zilombo zakutchire ndi mbalame zouluka mumlengalenga kuti mukhale chakudya chawo.+   Choncho anthu onse amene akukhala ku Iguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova,Chifukwa sanalinso ngati ndodo yothandiza nyumba ya Isiraeli poyenda, koma anali ngati tsekera.*+   Atakugwira dzanja, unaphwanyika,Ndipo unachititsa kuti athyole phewa lawo. Atakutsamira ngati ndodo yoyendera, unathyoka,Ndipo unachititsa kuti miyendo yawo injenjemere.”*+  Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndibweretsa lupanga mʼdziko lako+ ndipo ndidzapha anthu ndi nyama zomwe.  Dziko la Iguputo lidzakhala malo owonongeka komanso bwinja.+ Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova, chifukwa chakuti iwe wanena kuti,* ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga. Ineyo ndinaupanga ndekha.’+ 10  Choncho, iwe ndikulanga ndipo ndiwononga mtsinje wako wa Nailo ndipo dziko la Iguputo ndiliwononga nʼkulisandutsa malo ouma komanso bwinja,+ kuchokera ku Migidoli+ mpaka ku Seyene+ nʼkukafika kumalire a dziko la Itiyopiya. 11  Ndipo munthu kapena chiweto sichidzadutsa mʼdziko lako,+ ndipo simudzakhala munthu aliyense kwa zaka 40. 12  Ndidzachititsa kuti dziko la Iguputo likhale lowonongeka kwambiri kuposa mayiko ena onse, ndipo mizinda yake idzakhala yowonongeka kwambiri pa mizinda yonse kwa zaka 40.+ Ndidzamwaza Aiguputo pakati pa anthu a mitundu ina ndipo ndidzawabalalitsira mʼmayiko ena.”+ 13  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Zaka 40 zikadzatha, ndidzasonkhanitsanso Aiguputowo nʼkuwabwezera kudziko lawo kuchokera kwa anthu a mitundu ina kumene anabalalikira.+ 14  Aiguputo amene anagwidwa nʼkupita nawo kudziko lina ndidzawabwezeretsa ku Patirosi,+ mʼdziko limene anachokera ndipo kumeneko Iguputo adzakhala ufumu wonyozeka. 15  Ufumu wa Iguputo udzakhala wochepa mphamvu kusiyana ndi maufumu ena ndipo sudzalamuliranso mitundu ina ya anthu.+ Ine ndidzawachepetsa kwambiri moti sadzathanso kugonjetsa mitundu ina ya anthu.+ 16  Nyumba ya Isiraeli sidzadaliranso ufumu umenewu.+ Koma udzangowakumbutsa zolakwa zimene anachita podalira Aiguputo kuti awathandize. Ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’” 17  Tsopano mʼchaka cha 27, mʼmwezi woyamba, pa tsiku loyamba la mweziwo, Yehova analankhula nane kuti: 18  “Iwe mwana wa munthu, Nebukadinezara*+ mfumu ya Babulo anachititsa kuti asilikali ake agwire ntchito yaikulu pomenyana ndi Turo.+ Mutu wa msilikali aliyense unameteka ndipo mapewa awo ananyuka. Koma mfumuyo ndi asilikali akewo sanalandire malipiro aliwonse pa ntchito imene anagwira pomenyana ndi Turo. 19  Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndikupereka dziko la Iguputo kwa Nebukadinezara* mfumu ya Babulo.+ Iye adzatenga chuma cha dzikolo komanso kulanda zinthu zake zochuluka. Zimenezi zidzakhala malipiro a asilikali ake. 20  Ndimupatsa dziko la Iguputo monga chipukutamisozi pa ntchito imene anagwira pomenyana ndi Turo, chifukwa iwo anachita zimene ine ndinkafuna,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 21  Pa tsiku limenelo, ndidzaphukitsira nyumba ya Isiraeli nyanga*+ ndipo iwe ndidzakupatsa mpata kuti ulankhule pakati pawo, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “bango.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chiuno chawo chinjenjemere.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “iye wanena kuti.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “nyumba ya Isiraeli ndidzaipatsa mphamvu.”