Ezekieli 3:1-27

  • Ezekieli anauzidwa kuti adye mpukutu umene Mulungu anamupatsa (1-15)

  • Ezekieli anaikidwa kuti akhale mlonda (16-27)

    • Kunyalanyaza kungapangitse kuti tikhale ndi mlandu wamagazi (18-21)

3  Kenako anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, idya chimene chili pamaso pakochi.* Idya mpukutu uwu ndipo upite kukalankhula ndi nyumba ya Isiraeli.”+  Choncho ndinatsegula pakamwa panga, ndipo iye anandipatsa mpukutuwo kuti ndidye.  Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, idya mpukutu umene ndikukupatsawu kuti mimba yako ikhute.” Choncho ndinayamba kudya mpukutuwo ndipo unali wotsekemera ngati uchi.+  Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, pita pakati pa nyumba ya Isiraeli ndipo ukawauze mawu anga.  Chifukwa sindikukutuma kwa anthu amene amalankhula chilankhulo chovuta kumva kapena chilankhulo chimene iwe sukuchidziwa, koma ndikukutuma ku nyumba ya Isiraeli.  Sindikukutuma kwa mitundu yambiri ya anthu amene amalankhula chilankhulo chovuta kumva kapena chilankhulo chimene sukuchidziwa, amene sungathe kumvetsetsa zimene akunena. Ndikanakhala kuti ndakutumiza kwa anthu amenewo, akanakumvera.+  Koma a nyumba ya Isiraeli akakana kukumvera, chifukwa iwo sakufuna kundimvera.+ Anthu onse a nyumba ya Isiraeli ndi amakani komanso osamva.+  Koma ndachititsa kuti nkhope yako ikhale yolimba mofanana ndi nkhope zawo, ndiponso chipumi chako kuti chikhale cholimba mofanana ndi zipumi zawo.+  Ndachititsa kuti chipumi chako chikhale ngati mwala wa dayamondi, cholimba kuposa mwala wa nsangalabwi.+ Usawaope kapena kuchita mantha ndi nkhope zawo,+ chifukwa iwo ndi anthu opanduka.” 10  Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, mvetsera mawu onse amene ndikukuuza ndipo uwaganizire mozama. 11  Pita pakati pa anthu a mtundu wako* amene anatengedwa kupita ku ukapolo+ ndipo ukalankhule nawo. Ukawauze kuti, ‘Izi nʼzimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa wanena,’ kaya akamvetsera kapena ayi.”+ 12  Kenako mzimu unanditenga+ ndipo ndinayamba kumva mawu amphamvu kumbuyo kwanga ngati chimkokomo chachikulu akuti: “Ulemerero wa Yehova utamandike kumalo amene amakhala.” 13  Kenako ndinamva phokoso la mapiko a angelo pamene mapikowo ankakhulana.+ Ndinamvanso phokoso la mawilo amene anali pambali pawo+ komanso chimkokomo chachikulu. 14  Mzimu unandinyamula nʼkupita nane ndili wachisoni komanso wokwiya kwambiri. Dzanja la Yehova linandigwira mwamphamvu. 15  Choncho ndinapita kwa anthu amene anatengedwa kupita ku ukapolo omwe anali ku Tele-abibu. Anthuwa ankakhala pafupi ndi mtsinje wa Kebara.+ Ndinakhala nawo kumeneko masiku 7 nditasokonezeka maganizo.+ 16  Masiku 7 atatha, Yehova anandiuza kuti: 17  “Iwe mwana wa munthu, ine ndakuika kuti ukhale mlonda wa nyumba ya Isiraeli.+ Choncho ukamva mawu ochokera pakamwa panga ukuyenera kuwachenjeza.+ 18  Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’ koma iwe osalankhula naye nʼkumuchenjeza kuti asiye zoipa zimene akuchita kuti akhalebe ndi moyo,+ munthuyo adzafa chifukwa cha zolakwa zake popeza ndi woipa,+ koma iwe ndidzakuimba mlandu chifukwa cha magazi ake.*+ 19  Iweyo ukachenjeza munthu woipa koma iye osasiya zoipa zakezo ndi njira zake zoipa, munthuyo adzafa chifukwa cha zolakwa zake, koma iweyo udzapulumutsadi moyo wako.+ 20  Munthu amene amachita zinthu zabwino akasiya kuchita zabwinozo nʼkumachita zoipa,* ndidzamubweretsera tsoka ndipo adzafa.+ Ngati sunamuchenjeze, adzafa chifukwa cha tchimo lake ndipo zabwino zimene ankachita sizidzakumbukiridwa, koma magazi ake ndidzawafuna kuchokera kwa iwe.*+ 21  Koma ngati iweyo unachenjeza munthu wolungama kuti asachimwe, iye osachimwadi, munthuyo adzakhalabe ndi moyo chifukwa anachenjezedwa,+ ndipo iweyo udzakhala utapulumutsa moyo wako.” 22  Kenako dzanja la Yehova linafika pa ine kumeneko ndipo iye anandiuza kuti: “Nyamuka, pita kuchigwa ndipo ndikalankhula nawe kumeneko.” 23  Choncho ndinanyamuka nʼkupita kuchigwako ndipo ndinaona kuti ulemerero wa Yehova uli kumeneko.+ Ulemerero umenewu unali wofanana ndi umene ndinauona pafupi ndi mtsinje wa Kebara+ ndipo ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi. 24  Kenako mzimu unalowa mwa ine nʼkuchititsa kuti ndiimirire,+ ndipo Mulungu anandiuza kuti: “Pita ukadzitsekere mʼnyumba mwako. 25  Iwe mwana wa munthu, dziwa kuti anthu adzakumanga ndi zingwe kuti usapite pakati pawo. 26  Ndidzachititsa kuti lilime lako lidzaze mʼkamwa mwako ndipo sudzatha kulankhula kapena kuwadzudzula, chifukwa iwo ndi anthu opanduka. 27  Koma ndikamalankhula nawe ndizikutsegula pakamwa ndipo iweyo uziwauza kuti,+ ‘Izi nʼzimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa wanena.’ Wakumva amve,+ ndipo amene sakufuna kumva asamve, chifukwa iwo ndi anthu opanduka.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “idya chimene wapeza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa ana a anthu ako.”
Kapena kuti, “koma magazi ake ndidzawafuna kuchokera kwa iwe.”
Kapena kuti, “nʼkumachita zopanda chilungamo.”
Kapena kuti, “ndidzakuimba mlandu chifukwa cha magazi ake.”