Ezekieli 30:1-26

  • Ulosi wokhudza Iguputo (1-19)

    • Ananeneratu kuti Nebukadinezara adzaukira Iguputo (10)

  • Mphamvu za Farao zidzathyoka (20-26)

30  Yehova anandiuzanso kuti:  “Iwe mwana wa munthu, losera kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Lirani mofuula kuti, ‘Mayo ine, Tsiku lija likubwera!’   Tsikulo lili pafupi, inde tsiku la Yehova lili pafupi.+ Tsikulo lidzakhala la mitambo+ ndiponso nthawi yoikidwiratu yoti mitundu ya anthu iweruzidwe.+   Lupanga lidzabwera kudzaukira Iguputo, ndipo anthu a ku Itiyopiya adzachita mantha kwambiri anthu akadzaphedwa ku Iguputo.Chuma cha Iguputo chidzalandidwa ndipo maziko ake adzagwetsedwa.+   Itiyopiya,+ Puti,+ Ludi, anthu onse ochokera mʼmitundu yosiyanasiyana,Kubi limodzi ndi anthu amʼdziko lapangano,*Onsewa adzaphedwa ndi lupanga.”’   Yehova wanena kuti: ‘Anthu amene akuthandiza Iguputo nawonso adzaphedwa,Ndipo mphamvu zimene amazinyadira zidzatha.+ Anthu adzaphedwa ndi lupanga mʼdzikolo kuchokera ku Migidoli+ mpaka ku Seyene,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.  ‘Onsewo adzawonongeka kwambiri pa mayiko onse ndipo mizinda yawo idzakhala yowonongeka kwambiri pa mizinda yonse.+  Ndikadzayatsa moto mu Iguputo komanso ndikadzaphwanya onse amene akuthandizana nawo, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.  Pa tsikulo, ndidzatumiza amithenga pasitima zapamadzi kuti akaopseze Itiyopiya yemwe ndi wodzidalira. Itiyopiya adzachita mantha kwambiri pa tsiku limene Iguputo adzawonongedwe, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.’ 10  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ndidzawononga magulu a anthu a ku Iguputo pogwiritsa ntchito dzanja la Nebukadinezara,* mfumu ya Babulo.+ 11  Mfumuyo ndi asilikali ake, omwe ndi ankhanza kwambiri pa mayiko onse,+ adzabweretsedwa kuti adzawononge dzikolo. Iwo adzasolola malupanga awo nʼkuukira Iguputo ndipo adzadzaza dzikolo ndi anthu ophedwa.+ 12  Ndidzaumitsa ngalande zamumtsinje wa Nailo+ ndipo ndidzagulitsa dzikolo kwa anthu oipa. Ndidzachititsa kuti dzikolo ndi zonse zimene zili mmenemo ziwonongedwe ndi anthu ochokera kudziko lina.+ Ine Yehova, ndanena zimenezi.’ 13  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ndidzawononganso mafano onyansa* nʼkuthetsa milungu yopanda pake ya ku Nofi.*+ Sipadzapezekanso kalonga* wochokera mʼdziko la Iguputo ndipo ndidzachititsa kuti anthu amʼdzikolo azikhala mwamantha.+ 14  Mzinda wa Patirosi+ ndidzausandutsa bwinja. Mzinda wa Zowani ndidzauwotcha ndi moto ndipo ndidzaweruza mzinda wa No.*+ 15  Ndidzakhuthulira mkwiyo wanga pa Sini, mzinda umene Iguputo amaudalira kwambiri ndipo ndidzapha anthu ambiri a ku No. 16  Ndidzayatsa moto mu Iguputo. Sini adzachita mantha kwambiri ndipo adani adzagumula mpanda wa No nʼkulowa mumzindamo. Adani adzaukira mzinda wa Nofi* dzuwa likuswa mtengo. 17  Anyamata a ku Oni* ndi ku Pibeseti adzaphedwa ndi lupanga ndipo anthu amʼmizinda imeneyi adzatengedwa kupita ku ukapolo. 18  Mumzinda wa Tahapanesi mudzagwa mdima masana ndikadzathyola magoli a Iguputo kumeneko.+ Mphamvu zimene amanyadira zidzatha.+ Mitambo idzamuphimba ndipo anthu amʼmatauni ake adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ 19  Ndidzapereka chiweruzo mu Iguputo ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’” 20  Ndiyeno mʼchaka cha 11, mʼmwezi woyamba, pa tsiku la 7 la mweziwo, Yehova anandiuza kuti: 21  “Iwe mwana wa munthu, ine ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Iguputo. Dzanjalo silidzamangidwa kuti lichire kapena kukulungidwa ndi bandeji kuti likhale ndi mphamvu zoti nʼkugwira lupanga.” 22  “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ine ndilanga Farao mfumu ya Iguputo+ ndipo ndidzathyola manja ake onse, dzanja lamphamvu ndi lothyoka lomwe.+ Ndidzachititsa kuti lupanga ligwe mʼdzanja lake.+ 23  Kenako ndidzabalalitsira Aiguputo ku mitundu ina ya anthu nʼkuwamwaza mʼmayiko ena.+ 24  Ndidzalimbitsa manja a mfumu* ya Babulo+ ndipo ndidzaipatsa lupanga langa.+ Ndidzathyola manja a Farao ndipo adzabuula kwambiri ngati munthu amene watsala pangʼono kufa pamaso pa mfumu ya Babulo. 25  Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya Babulo koma manja a Farao adzafooka. Ndikadzapereka lupanga langa mʼmanja mwa mfumu ya Babulo, iye nʼkuligwiritsa ntchito pomenyana ndi dziko la Iguputo,+ iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova. 26  Ine ndidzabalalitsira Aiguputo ku mitundu ina ya anthu nʼkuwamwaza mʼmayiko ena+ ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”

Mawu a M'munsi

Nʼkutheka kuti akunena za Aisiraeli amene anachita mgwirizano ndi Aiguputo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “mtsogoleri.”
Kapena kuti, “Memfisi.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Amene ndi Thebesi.
Kapena kuti, “Memfisi.”
Amene ndi Heliyopolisi.
Kapena kuti, “Ndidzawonjezera mphamvu za mfumu.”