Ezekieli 31:1-18

  • Kugwa kwa Iguputo, yemwe ndi mtengo wautali wa mkungudza (1-18)

31  Mʼchaka cha 11, mʼmwezi wachitatu, pa tsiku loyamba la mweziwo, Yehova anandiuzanso kuti:  “Iwe mwana wa munthu, uza Farao mfumu ya Iguputo ndi magulu a anthu amene amamutsatira+ kuti,‘Kodi ndi ndani amene ali wamphamvu ngati iwe?   Iwe uli ngati Msuri, mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni,Wa nthambi zokongola ngati ziyangoyango za masamba ambiri, mtengo wautali kwambiri,Umene nsonga yake inafika mʼmitambo.   Mtengowo unakula kwambiri chifukwa cha madzi. Akasupe ozama anachititsa kuti mtengowo utalike. Pamalo amene mtengowo unadzalidwa panali mitsinje yambiri yamadzi.Ngalande za madziwo zinkathirira mitengo yonse yamʼmundamo.   Nʼchifukwa chake mtengowo unatalika kwambiri kuposa mitengo yonse yamʼmundamo. Nthambi zake zinachuluka komanso zinatalikaChifukwa cha kuchuluka kwa madzi mʼmitsinje yake.   Mbalame zonse zouluka mumlengalenga zinkamanga zisa zawo mʼnthambi zake,Nyama zonse zakutchire zinkaberekera pansi pa nthambi zake,Ndipo mitundu yonse ya anthu ambiri inkakhala mumthunzi wake.   Mtengowo unakhala wokongola kwambiri ndipo nthambi zake zinatalika kwambiri,Chifukwa chakuti mizu yake inapita pansi nʼkukafika pamadzi ambiri.   Mitengo ina ya mkungudza sinafanane ndi mtengo umenewu mʼmunda wa Mulungu.+ Panalibe mtengo uliwonse wa junipa* umene unali ndi nthambi ngati zake,Panalibe mtengo uliwonse wa katungulume umene nthambi zake zinali zofanana ndi za mtengowo. Panalibenso mtengo wina mʼmunda wa Mulungu umene unali wokongola ngati mtengo umenewu.   Mtengo umenewu ndinaukongoletsa pouchulukitsira masamba,Ndipo mitengo ina yonse ya mu Edeni, munda wa Mulungu woona, inkauchitira nsanje.’ 10  Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chifukwa chakuti mtengowu* unatalika kwambiri moti nsonga yake inakafika mʼmitambo, ndipo mtima wake unayamba kudzikuza chifukwa cha kutalika kwake, 11  ndidzaupereka mʼmanja mwa wolamulira wamphamvu wa anthu a mitundu ina.+ Iye adzaukhaulitsa ndithu, ndipo ine ndidzaukana chifukwa cha kuipa kwake. 12  Anthu amʼmayiko ena, mitundu ya anthu yankhanza kwambiri, adzadula mtengowo ndipo adzausiya mʼmapiri. Masamba ake adzagwera mʼzigwa zonse ndipo nthambi zake zidzathyoka nʼkugwera mʼmitsinje yonse yamʼdzikolo.+ Mitundu yonse ya anthu apadziko lapansi idzachoka mumthunzi wake nʼkuusiya. 13  Mbalame zonse zouluka mumlengalenga zizidzakhala pamtengo umene unagwetsedwawo, ndipo nyama zonse zakutchire zizidzakhala munthambi zake.+ 14  Zidzakhala choncho kuti pasadzapezekenso mtengo uliwonse umene uli pafupi ndi madzi, womwe udzatalike kwambiri kapena umene nsonga zake zidzafike mʼmitambo. Komanso kuti mtengo uliwonse umene uli pamadzi ambiri usadzatalike kukafika mʼmitambo. Chifukwa mitengo yonse idzafa nʼkutsikira pansi pa nthaka pamodzi ndi ana a anthu amene akutsikira kudzenje.’* 15  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Pa tsiku limene mtengowo udzatsikire ku Manda,* ndidzachititsa kuti anthu alire. Choncho ndidzaphimba madzi akuya komanso kutseka mitsinje yake kuti madzi ambiri asamadutse. Ndidzachititsa mdima mu Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse yakutchire idzafota. 16  Phokoso la kugwa kwake likadzamveka, ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu injenjemere ndikamadzatsitsira mtengowo ku Manda* pamodzi ndi onse amene akutsikira kudzenje.* Ndipo mitengo yonse ya mu Edeni+ komanso mitengo yonse yabwino kwambiri ya ku Lebanoni imene ili pamadzi ambiri, idzatonthozedwa pansi pa nthaka. 17  Mitengo imeneyi yatsikira ku Manda* pamodzi ndi mtengo wa mkungudzawo. Yatsikira kwa ophedwa ndi lupanga+ limodzi ndi amene ankamuthandiza* omwe ankakhala mumthunzi wake pakati pa mitundu ina ya anthu.’+ 18  ‘Kodi ndi mtengo uti pakati pa mitengo ya mu Edeni umene unkafanana ndi iwe pa nkhani ya ulemerero ndi kukula?+ Koma ndithu udzafa* limodzi ndi mitengo ya mu Edeni. Udzagona pakati pa anthu osadulidwa limodzi ndi ophedwa ndi lupanga. Mtengo umenewu ukuimira Farao ndi magulu onse a anthu amene amamutsatira,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

Mawu a M'munsi

Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.
Mʼchilankhulo choyambirira, “iwe.”
Kapena kuti, “kumanda.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “kumanda.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “limodzi ndi dzanja lake.”
Kapena kuti, “udzatsitsidwira kumanda.”