Ezekieli 35:1-15

  • Ulosi wokhudza dera lamapiri la Seiri (1-15)

35  Yehova anandiuzanso kuti:  “Iwe mwana wa munthu, yangʼana dera lamapiri la Seiri+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzachitikire deralo.+  Uuze deralo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe dera lamapiri la Seiri, ine ndikupatsa chilango. Nditambasula dzanja langa nʼkukukhaulitsa ndipo ndikusandutsa bwinja lowonongeka kwambiri.+  Mizinda yako ndidzaisandutsa bwinja komanso udzakhala malo owonongeka kwambiri+ ndipo udzadziwa kuti ine ndine Yehova.  Chifukwa chakuti unasonyeza chidani chachikulu+ ndipo unapha Aisiraeli ndi lupanga pa nthawi ya tsoka lawo, pamene ankalandira chilango chawo chomaliza.”’+  ‘Choncho pali ine Mulungu wamoyo,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ‘Ndidzakonza zoti magazi ako akhetsedwe ndipo mlandu wa magazi udzakutsatira.+ Chifukwa unkadana ndi anthu amene unakhetsa magazi awo, mlandu wa magazi udzakutsatira.+  Dera lamapiri la Seiri ndidzalisandutsa bwinja lowonongeka kwambiri+ ndipo ndidzawononga aliyense amene akudutsa kumeneko komanso aliyense wochokera kumeneko.  Mʼmapiri amʼderalo ndidzadzazamo anthu amene aphedwa ndipo anthu amene aphedwa ndi lupanga adzagwera mʼzitunda zako, mʼzigwa zako ndi mʼmitsinje yako yonse.  Ndidzakusandutsa malo omwe adzakhale owonongeka mpaka kalekale. Mʼmizinda yako simudzakhalanso anthu+ ndipo udzadziwa kuti ine ndine Yehova.’ 10  Chifukwa unanena kuti, ‘Mitundu iwiri iyi ya anthu ndi mayiko awiri awa zidzakhala zanga ndipo ife tidzatenga zonsezi.’+ Unanena zimenezi ngakhale kuti Yehova anali komweko. 11  ‘Choncho pali ine Mulungu wamoyo,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ‘Ndidzakulanga mogwirizana ndi mkwiyo komanso nsanje imene unaisonyeza chifukwa chakuti unkadana nawo,+ ndipo ndikadzakuweruza, iwo adzandidziwa. 12  Pa nthawi imeneyo udzadziwa kuti ine Yehova, ndinamva mawu onse achipongwe amene unanenera mapiri a ku Isiraeli. Pamene unanena kuti, “Mapiri aja awonongedwa ndipo aperekedwa kwa ife kuti tiwadye.”* 13  Iwe unalankhula modzitama kwa ine ndipo unachulukitsa mawu ako ondinyoza.+ Ine ndinamva zonsezo.’ 14  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Dziko lonse lapansi lidzasangalala ndikadzakusandutsa bwinja lowonongeka kwambiri. 15  Mofanana ndi mmene unasangalalira cholowa cha nyumba ya Isiraeli chitawonongedwa, ine ndidzachitanso chimodzimodzi kwa iwe.+ Iwe dera lamapiri la Seiri, kutanthauza Edomu yense,+ udzasanduka bwinja, ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “aperekedwa kwa ife ngati chakudya.”