Ezekieli 36:1-38

  • Ulosi wokhudza mapiri a ku Isiraeli (1-15)

  • Isiraeli adzabwereranso mwakale (16-38)

    • ‘Ndidzayeretsa dzina langa lalikulu’ (23)

    • “Ngati munda wa Edeni” (35)

36  “Koma iwe mwana wa munthu, losera zokhudza mapiri a ku Isiraeli ndipo unene kuti, ‘Inu mapiri a ku Isiraeli, imvani mawu a Yehova. 2  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Mdani wanu wakunenani kuti, ‘Eyaa! Ngakhale malo okwezeka akalekale tawatenga kuti akhale athu!’”’+ 3  Choncho losera ndipo unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Adani anu akusandutsani bwinja ndipo akuukirani kuchokera kumbali zonse. Achita zimenezi kuti anthu a mitundu ina amene anapulumuka* akutengeni kuti mukhale awo ndipo anthu akunena za inu komanso kukunenerani miseche.+ 4  Choncho inu mapiri a ku Isiraeli, imvani mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wauza mapiri ndi zitunda, mitsinje ndi zigwa, mabwinja a malo amene anawonongedwa+ komanso mizinda yopanda anthu imene anthu a mitundu ina amene anapulumuka anaitenga kuti ikhale yawo. Anthuwo ankakhala moizungulira ndipo ankainyoza.+ 5  Mawu amene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, akuwauza ndi akuti: ‘Ndidzadzudzula anthu a mitundu ina amene anapulumuka komanso Edomu yense nditakwiya kwambiri.+ Ndidzadzudzula amene anatenga dziko langa kuti likhale lawo akusangalala kwambiri komanso akunyoza+ nʼcholinga choti dzikolo ndi malo ake odyetserako ziweto zikhale zawo.’”’+ 6  Choncho losera zokhudza dziko la Isiraeli ndipo uuze mapiri, zitunda, mitsinje ndi zigwa kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ineyo ndidzalankhula mwaukali ndiponso nditakwiya kwambiri chifukwa chakuti anthu a mitundu ina akhala akukunyozani.”’+ 7  Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ine ndikulumbira nditakweza dzanja langa kuti mitundu imene yakuzungulirani idzachita manyazi.+ 8  Koma inu mapiri a Isiraeli, mudzatulutsa nthambi nʼkuberekera zipatso anthu anga Aisiraeli,+ chifukwa chakuti abwerera mʼdziko lawo posachedwapa. 9  Chifukwa ine ndili ndi inu ndipo ndidzakukomerani mtima moti anthu adzalima minda mwa inu nʼkudzala mbewu. 10  Ndidzachulukitsa anthu anu. Ndidzachulukitsa nyumba yonse ya Isiraeli. Anthu adzayamba kukhala mʼmizinda+ ndipo malo amene anali mabwinja adzamangidwanso.+ 11  Inde, ndidzachulukitsa anthu anu ndi ziweto zanu.+ Adzachuluka nʼkuberekana kwambiri. Ndidzachititsa kuti anthu akhale mwa inu ngati mmene zinalili poyamba+ ndipo ndidzachititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino kwambiri kuposa poyamba.+ Choncho inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 12  Ndidzachititsa kuti anthu, anthu anga Aisiraeli, azidzayendayenda mwa inu ndipo adzakutengani kuti mukhale awo.+ Inu mudzakhala cholowa chawo ndipo simudzawalandanso ana awo.’”+ 13  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Anthu akukunenani kuti: “Inu ndinu dziko limene limadya anthu ndipo mumapha ana a mitundu ya anthu anu.”’ 14  ‘Pa chifukwa chimenechi inu simudzadyanso anthu kapena kuchititsa kuti mitundu ya anthu anu ikhale yopanda ana,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 15  ‘Sindidzachititsanso kuti anthu a mitundu ina azikunyozani kapena kuti anthu azikunenerani mawu achipongwe+ ndipo simudzakhumudwitsanso mitundu ya anthu amene akukhala mwa inu,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” 16  Yehova anandiuzanso kuti: 17  “Iwe mwana wa munthu, pa nthawi imene a nyumba ya Isiraeli ankakhala mʼdziko lawo, analidetsa ndi makhalidwe awo komanso zochita zawo.+ Kwa ine, khalidwe lawo linali ngati zonyansa za mkazi amene akusamba.+ 18  Choncho ndinawakhuthulira mkwiyo wanga chifukwa cha magazi amene iwo anakhetsa mʼdzikoli+ komanso chifukwa chakuti anadetsa dzikoli ndi mafano awo onyansa.*+ 19  Ndiye ndinawabalalitsira kwa anthu a mitundu ina ndipo ndinawamwaza mʼmayiko osiyanasiyana.+ Ndinawaweruza mogwirizana ndi njira zawo komanso zochita zawo. 20  Koma atapita kwa anthu a mitundu inawo, anthuwo anadetsa dzina langa loyera+ ponena za iwowo kuti, ‘Awa ndi anthu a Yehova, koma anachoka mʼdziko lake.’ 21  Ndidzachita zinthu zosonyeza kuti ndikudera nkhawa dzina langa loyera, limene nyumba ya Isiraeli yalidetsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene iwo anapita.”+ 22  “Choncho uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo a nyumba ya Isiraeli, koma chifukwa cha dzina langa loyera limene munalidetsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene munapita.”’+ 23  ‘Ndidzayeretsadi dzina langa lalikulu+ limene linadetsedwa pakati pa anthu a mitundu ina. Inu munadetsa dzina langalo pakati pa anthu a mitundu ina. Anthu a mitundu inawo adzadziwa kuti ine ndine Yehova,+ akadzaona zimene ndakuchitirani komanso adzadziwa kuti ndine Mulungu woyera,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 24  ‘Ndidzakutengani kuchokera kwa anthu a mitundu ina nʼkukusonkhanitsani pamodzi kuchokera mʼmayiko onse ndipo ndidzakubwezeretsani mʼdziko lanu.+ 25  Ndidzakuwazani madzi oyera ndipo mudzakhala oyera.+ Ndidzakuyeretsani pokuchotserani zonyansa zanu zonse+ ndi mafano anu onse onyansa.+ 26  Ndidzakupatsani mtima watsopano+ ndipo ndidzaika mzimu watsopano mwa inu.+ Ndidzachotsa mtima wamwala+ mʼmatupi anu nʼkukupatsani mtima wamnofu.* 27  Ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo ndidzachititsa kuti muziyenda motsatira malamulo anga.+ Mudzasunga zigamulo zanga komanso kuzitsatira. 28  Mukadzachita zimenezi mudzakhala mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu. Mudzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu.’+ 29  ‘Ndidzakupulumutsani ku zinthu zanu zonse zodetsa ndipo ndidzauza mbewu kuti zibereke kwambiri moti sindidzakubweretseraninso njala.+ 30  Ndidzachititsa kuti zipatso za mtengo komanso zokolola zakumunda zichuluke nʼcholinga choti musadzanyozekenso chifukwa cha njala pakati pa anthu a mitundu ina.+ 31  Pa nthawiyo mudzakumbukira njira zanu zoipa ndi zochita zanu zimene sizinali zabwino. Mudzadzimvera chisoni chifukwa cha machimo anu komanso zinthu zonyansa zimene munkachita.+ 32  Koma dziwani izi: Ine sindikuchita zimenezi chifukwa cha inu,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Koma inu a nyumba ya Isiraeli, muchite manyazi ndipo muone kuti mwanyozeka chifukwa cha njira zanu.’ 33  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Pa tsiku limene ndidzakuyeretseni nʼkuchotsa zolakwa zanu zonse, ndidzachititsa kuti mʼmizinda yanu muzikhala anthu+ komanso kuti malo amene anali mabwinja amangidwenso.+ 34  Anthu adzalima mʼdziko limene linawonongedwa, limene aliyense wodutsa ankaliona kuti ndi bwinja. 35  Anthu adzanena kuti: “Dziko limene linali bwinja tsopano lakhala ngati munda wa Edeni.+ Mizinda imene inawonongedwa ija, imene inali mabwinja ndiponso imene nyumba zake zinagwetsedwa, tsopano ili ndi mipanda yolimba kwambiri ndipo mukukhala anthu.”+ 36  Anthu a mitundu ina amene anatsala omwe akuzungulirani, adzadziwa kuti ine Yehova, ndamanga zinthu zimene zinagwetsedwa komanso kuti ndadzala mitengo mʼdziko limene linali bwinja. Ine Yehova ndanena zimenezi ndipo ndazichita.’+ 37  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ine ndidzalolanso kuti a nyumba ya Isiraeli andipemphe kuti ndiwachulukitsire anthu awo ngati gulu la nkhosa ndipo ndidzachitadi zimenezo. 38  Mizinda imene inali mabwinja idzadzaza ndi anthu ochuluka+ ngati gulu la oyera ndiponso ngati nkhosa za ku Yerusalemu* pa nthawi ya zikondwerero,+ ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu amene anatsala.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Kutanthauza mtima wofuna kutsogoleredwa ndi Mulungu.
Mabaibulo ena amati, “ngati nkhosa zomwe ankapereka ngati nsembe ku Yerusalemu.”