Ezekieli 37:1-28

  • Masomphenya a chigwa cha mafupa ouma (1-14)

  • Ndodo ziwiri adzaziphatikiza pamodzi (15-28)

    • Mtundu umodzi wolamulidwa ndi mfumu imodzi (22)

    • Pangano la mtendere limene lidzakhalepo mpaka kalekale (26)

37  Mphamvu za Yehova zinayamba kugwira ntchito pa ine* moti mzimu wa Yehova unanditenga nʼkukandikhazika pakati pa chigwa+ ndipo mʼchigwamo munali mafupa okhaokha.  Iye anandiyendetsa mʼchigwamo kuti ndione mafupa onsewo ndipo ndinaona kuti mʼchigwamo munali mafupa ambiri ndipo anali ouma kwambiri.+  Ndiyeno anandifunsa kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi mafupawa angakhale ndi moyo?” Ine ndinayankha kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, inu ndi amene mukudziwa zimenezo.”+  Ndiye anandiuza kuti: “Losera zokhudza mafupa amenewa ndipo uwauze kuti, ‘Inu mafupa ouma, imvani mawu a Yehova:  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wauza mafupa awa kuti: “Ndichititsa kuti mpweya ulowe mwa inu ndipo mukhala amoyo.+  Ndidzakuikirani mitsempha komanso mnofu ndipo ndidzakukutirani ndi khungu nʼkuika mpweya mwa inu ndipo mudzakhala ndi moyo. Choncho mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”  Choncho ine ndinalosera mogwirizana ndi zimene anandilamula. Nditangolosera, panamveka phokoso la mafupa kuti gobedegobede! Ndipo mafupawo anayamba kubwera pamodzi nʼkumalumikizana.  Kenako ndinaona mitsempha ndi mnofu zikukuta mafupawo ndipo khungu linabwera pamwamba pake. Koma mʼmafupawo munalibe mpweya.  Kenako anandiuza kuti: “Losera kwa mphepo. Iwe mwana wa munthu, losera ndipo uuze mphepoyo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe mphepo,* bwera kuchokera kumbali zonse 4 nʼkuwomba anthu amene anaphedwawa kuti akhalenso ndi moyo.”’” 10  Choncho ndinalosera mogwirizana ndi zimene anandilamula ndipo mpweya* unalowa mwa iwo. Iwo anakhala ndi moyo ndipo anaimirira.+ Anali gulu lalikulu kwambiri la asilikali. 11  Kenako anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, mafupawa akuimira nyumba yonse ya Isiraeli.+ Iwo akunena kuti, ‘Mafupa athu auma ndipo tilibenso chiyembekezo chilichonse.+ Tatheratu!’ 12  Choncho losera, uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndidzatsegula manda anu,+ inu anthu anga ndipo ndidzakutulutsani mʼmandamo nʼkukubweretsani mʼdziko la Isiraeli.+ 13  Inu anthu anga, ine ndikadzatsegula manda anu nʼkukutulutsani mʼmandamo, mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”+ 14  Ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhala amoyo.+ Ndidzakukhazikani mʼdziko lanu ndipo mudzadziwa kuti ine Yehova ndinanena zimenezi ndipo ndazichita,’ akutero Yehova.” 15  Yehova anandiuzanso kuti: 16  “Koma iwe mwana wa munthu, tenga ndodo nʼkulembapo kuti, ‘Ndodo ya Yuda ndi Aisiraeli amene ali naye.’*+ Kenako utengenso ndodo ina nʼkulembapo kuti, ‘Ndodo ya Yosefe yoimira Efuraimu ndi onse amʼnyumba ya Isiraeli amene ali naye.’*+ 17  Ndiyeno uziike pamodzi kuti zikhale ndodo imodzi mʼdzanja lako.+ 18  Anthu a mtundu wako* akakufunsa kuti, ‘Kodi sutiuza kuti zinthu zimenezi zikutanthauza chiyani?’ 19  Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine nditenga ndodo ya Yosefe ndi mafuko a Isiraeli amene ali naye. Ndodo imeneyi ili mʼdzanja la Efuraimu. Ndidzaiphatikiza ndi ndodo ya Yuda ndipo idzakhala ndodo imodzi.+ Iwo adzakhala ndodo imodzi mʼdzanja langa.”’ 20  Ndodo zimene wazilembazo zikhale mʼdzanja lako kuti azione. 21  Ndiye uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine nditenga Aisiraeli kuchokera kwa anthu a mitundu ina kumene anapita. Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumbali zonse ndipo ndidzawabweretsa mʼdziko lawo.+ 22  Ndidzawachititsa kuti akhale mtundu umodzi mʼdzikolo+ ndipo azidzakhala mʼmapiri a Isiraeli. Onse azidzalamulidwa ndi mfumu imodzi+ ndipo sadzakhalanso mitundu iwiri kapena kugawanika nʼkukhala maufumu awiri.+ 23  Iwo sadzadziipitsanso ndi mafano awo onyansa,* zochita zawo zonyansa ndi zolakwa zawo zonse.+ Ndidzawapulumutsa ku zochita zawo zosakhulupirika zimene zinachititsa kuti achimwe ndipo ndidzawayeretsa. Iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.+ 24  Mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yawo+ ndipo onsewo adzakhala ndi mʼbusa mmodzi.+ Iwo adzayenda motsatira zigamulo zanga ndiponso kusunga malamulo anga mosamala kwambiri.+ 25  Anthu amenewa adzakhala mʼdziko limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo, dziko limene makolo anu ankakhala.+ Iwo adzakhala mʼdzikomo ndi ana awo* komanso zidzukulu zawo+ mpaka kalekale.+ Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri* wawo mpaka kalekale.+ 26  Ndidzachita nawo pangano lamtendere+ ndipo pangano limeneli lidzakhalapo mpaka kalekale. Ine ndidzachititsa kuti akhazikike mʼdzikolo ndipo ndidzawachulukitsa+ komanso ndidzaika malo anga opatulika pakati pawo mpaka kalekale. 27  Tenti yanga idzakhala* pakati pawo.* Ine ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga.+ 28  Malo anga opatulika akadzakhala pakati pawo mpaka kalekale, anthu a mitundu ina adzadziwa kuti ine Yehova, ndikuyeretsa Isiraeli.”’”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Dzanja la Yehova linafika pa ine.”
Kapena kuti, “mpweya; mzimu.”
Kapena kuti, “mzimu.”
Kapena kuti, “amene ndi anzake.”
Kapena kuti, “amene ndi anzake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana aamuna a anthu ako.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Kapena kuti, “kalonga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana awo aamuna.”
Kapena kuti, “Malo anga okhala adzakhala; Nyumba yanga.”
Kapena kuti, “idzawaphimba.”