Ezekieli 4:1-17
4 “Iwe mwana wa munthu, tenga njerwa ndipo uiike patsogolo pako. Panjerwapo ujambulepo mzinda wa Yerusalemu.
2 Umenye nkhondo ndi mzindawo+ ndipo umange mpanda womenyerapo nkhondo kuzungulira mzinda wonsewo.+ Umangenso malo okwera omenyerapo nkhondo+ komanso misasa ya asilikali. Uikenso zida zankhondo zogumulira mpanda wa mzindawo kuzungulira mzinda wonsewo.+
3 Utenge chiwaya ndipo uchiike pakati pa iweyo ndi mzindawo kuti chikhale ngati khoma lachitsulo. Uziyangʼana mzindawo monyansidwa ndipo usonyeze zimene adani adzachite poukira mzindawo. Chimenechi chikhale chizindikiro ku mtundu wa Isiraeli.+
4 Kenako ugonere kumanzere kwako ndipo ugonere zolakwa za nyumba ya Isiraeli.+ Kwa masiku amene udzagonere kumanzereko, udzanyamula zolakwa zawo.
5 Ine ndidzafuna kuti uchite zimenezi kwa masiku 390, mogwirizana ndi zaka za kulakwa kwawo.+ Ndipo iweyo udzanyamula zolakwa za nyumba ya Isiraeli.
6 Udzakwanitse masiku onsewo.
Kenako udzagonere kumanja kwako, ndipo udzanyamule zolakwa za nyumba ya Yuda+ kwa masiku 40. Ndakupatsa tsiku limodzi kuti liimire chaka chimodzi.
7 Nkhope yako izidzayangʼana Yerusalemu+ atazunguliridwa ndi asilikali. Udzapinde malaya ako kuti dzanja lako lidzakhale pamtunda ndipo udzalosere zinthu zoipa zimene zidzachitikire mzindawo.
8 Ine ndidzakumanga ndi zingwe kuti usathe kutembenukira kumbali ina, mpaka utamaliza masiku ako ozungulira mzindawo.
9 Ndipo utenge tirigu, balere, nyemba zikuluzikulu, mphodza, mapira ndi sipeloti.* Zonsezo uziike mumphika umodzi kuti zikhale chakudya chako. Pa masiku 390 amene udzakhale ukugonera mbali imodzi uzidzadya chakudya chimenechi.+
10 Tsiku lililonse uzidzadya chakudya chochita kuyeza. Uzidzadya chakudya chokwana masekeli 20.* Uzidzadya chakudyachi nthawi yofanana tsiku lililonse.
11 Uzidzamwa madzi ochita kuyeza, ndipo uzidzamwa makapu awiri okha.* Uzidzamwa madziwo nthawi yofanana tsiku lililonse.
12 Uzidzadya chakudyacho ngati mmene umadyera mkate wozungulira wa balere. Uzidzachiphika iwo akuona pogwiritsa ntchito tudzi touma ta anthu.”
13 Yehova anapitiriza kunena kuti: “Mofanana ndi zimenezi, Aisiraeli azidzadya chakudya chodetsedwa pakati pa anthu a mitundu ina kumene ndidzawabalalitsireko.”+
14 Kenako ndinanena kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndiloleni ndisachite zimenezo. Kuyambira ndili mwana mpaka pano sindinadzidetsepo podya nyama yopezeka itafa kapena nyama yochita kukhadzulidwa ndi chilombo,+ ndipo mʼkamwa mwanga simunalowepo nyama yodetsedwa.”+
15 Choncho iye anandiuza kuti: “Chabwino, ndikulola kuti uzigwiritsa ntchito ndowe za ngʼombe mʼmalo mwa tudzi ta anthu kuti uziphikira chakudya chako.”
16 Kenako anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, ine ndidzachititsa kuti chakudya chisowe* mu Yerusalemu.+ Anthu azidzadya chakudya chochita kuyeza ndipo adzachidya ali ndi nkhawa yaikulu.+ Azidzamwa madzi ochita kuyeza ali ndi mantha aakulu.+
17 Zimenezi zikadzachitika azidzayangʼanizana modabwa posowa chakudya ndi madzi ndipo adzaonda chifukwa cha zolakwa zawo.”
Mawu a M'munsi
^ Sipeloti ndi mtundu wina wa tirigu koma wosakoma.
^ Pafupifupi magalamu 230. Onani Zakumapeto B14.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “gawo limodzi la magawo 6 a muyezo wa hini,” lomwe ndi pafupifupi hafu ya 1 lita. Onani Zakumapeto B14.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndidzathyola ndodo za mkate.” Nʼkutheka kuti akutanthauza ndodo zimene ankagwiritsira ntchito posunga mikate.