Ezekieli 40:1-49

  • Ezekieli anamupititsa ku Isiraeli mʼmasomphenya (1, 2)

  • Ezekieli anaona masomphenya a kachisi (3, 4)

  • Mabwalo ndi mageti (5-47)

    • Geti lakunja lakumʼmawa (6-16)

    • Bwalo lakunja; mageti ena (17-26)

    • Bwalo lamkati ndi mageti (27-37)

    • Zipinda zochitiramo utumiki wapakachisi (38-46)

    • Guwa lansembe (47)

  • Khonde la kachisi (48, 49)

40  Mʼchaka cha 25 kuchokera pamene tinatengedwa kupita ku ukapolo,+ kuchiyambi kwa chakacho, pa tsiku la 10 la mwezi woyamba, mʼchaka cha 14 pambuyo poti mzinda wawonongedwa,+ pa tsiku limeneli mphamvu za Yehova zinayamba kugwira ntchito pa ine,* ndipo iye ananditenga nʼkupita nane kumzinda.+  Kudzera mʼmasomphenya ochokera kwa Mulungu, iye ananditenga nʼkupita nane mʼdziko la Isiraeli nʼkukandikhazika paphiri lalitali kwambiri.+ Mbali yakumʼmwera paphiripo panali chinachake chooneka ngati mzinda.  Atafika nane kumeneko, ndinaona munthu wamwamuna amene maonekedwe ake anali ofanana ndi kopa.*+ Mʼmanja mwake munali chingwe cha fulakesi* ndi bango loyezera*+ ndipo anaima pakhomo lapageti.  Munthuyo anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, uonetsetse, umvetsere mwatcheru ndipo uchite chidwi ndi zonse* zimene ndikuonetse, chifukwa ndakubweretsa kuno kuti udzachite zimenezi. Ukauze nyumba ya Isiraeli zonse zimene uone.”+  Ndiyeno ndinaona mpanda umene unazungulira kachisi.* Mʼmanja mwa munthu uja munali bango loyezera lokwana mikono 6 kutalika kwake (pa mkono uliwonse anawonjezerapo chikhatho chimodzi).* Iye anayamba kuyeza mpandawo ndipo anapeza kuti unali wochindikala bango limodzi komanso kuchoka pansi kupita mʼmwamba unali wautali bango limodzi.  Kenako anafika pageti limene linayangʼana kumʼmawa+ nʼkukwera masitepe ake. Atayeza malo apafupi ndi khomo la kanyumba kapagetiko, anapeza kuti anali bango limodzi mulifupi. Malo apafupi ndi khomo lambali ina ya kanyumbako analinso bango limodzi mulifupi mwake.  Chipinda cha alonda chilichonse chinali bango limodzi mulitali ndi bango limodzi mulifupi. Kuchoka pachipinda chimodzi kukafika pachipinda china panali mikono 5.+ Malo apafupi ndi khomo la kanyumbako, pafupi ndi khonde limene linayangʼanizana ndi kachisi, anali bango limodzi.  Munthu uja anayeza khonde la kanyumbako loyangʼana bwalo lakunja, ndipo anapeza kuti linali bango limodzi.  Kenako anayeza khonde la kanyumba kapageti nʼkupeza kuti linali mikono 8. Anayezanso zipilala zake zamʼmbali, nʼkupeza kuti zinali mikono iwiri. Khonde la kanyumbako linali kumbali imene inayangʼanizana ndi kachisi. 10  Kumbali iliyonse ya geti lakumʼmawa kunali zipinda zitatu za alonda. Zipinda zitatuzo zinali zazikulu mofanana, ndipo zipilala zamʼmbali zimene zinali mbali iliyonse zinalinso zofanana. 11  Kenako anayeza mulifupi mwa malo apafupi ndi khomo la kanyumba kapageti nʼkupeza mikono 10. Mulitali mwa getilo munali mikono 13. 12  Malo otchinga ndi mpanda, kutsogolo kwa zipinda za alonda, anali mkono umodzi mbali zonse. Chipinda cha alonda chilichonse pa kanyumbako, chinali mikono 6. 13  Kenako anayeza kanyumba kapagetiko kuchokera padenga la chipinda chimodzi cha alonda* kukafika padenga la chipinda china ndipo anapeza mikono 25. Khomo lililonse la chipinda cha alonda linali moyangʼanizana ndi khomo la chipinda cha mbali inayo.+ 14  Kenako anayeza zipilala zamʼmbali ndipo anapeza kuti zinali zazitali mikono 60. Zinalinso chimodzimodzi ndi zipilala zamʼmbali zimene zinali mʼmageti a mbali zina za bwaloli. 15  Kuchokera kutsogolo kwa khomo lakunja la kanyumba kapageti, kukafika kutsogolo kwa khonde, kumbali imene yayangʼanizana ndi kachisi, panali mikono 50. 16  Zipinda za alondazo komanso zipilala zimene zinali mʼmbali mwa zipindazo zinali ndi mawindo amene anali ndi mafelemu aakulu mkati koma aangʼono kunja+ kuzungulira kanyumba konseko. Mkati mwa makonde munalinso mawindo mbali zonse ndipo pazipilala zamʼmbali panali zithunzi za mtengo wa kanjedza.+ 17  Kenako anandipititsa mʼbwalo lakunja. Kumeneko ndinaona zipinda zodyera*+ ndipo pansi pa bwalo lonselo panali powaka. Pabwalo lowakalo panali zipinda zodyera zokwana 30. 18  Mulifupi mwa malo owaka miyala amʼmbali mwa tinyumba tapageti munali mofanana ndi mulitali mwa tinyumbato. Malo owaka amenewa anali otsika poyerekezera ndi bwalo lamkati. 19  Kenako munthu uja anayeza mtunda* wochokera kutsogolo kwa kanyumba kapageti lamʼmunsi kukafika pamene panayambira bwalo lamkati. Malo amenewa anali mikono 100, kumʼmawa ndi kumpoto. 20  Bwalo lakunja linali ndi kanyumba kapageti kamene kanayangʼana kumpoto. Iye anayeza mulitali ndi mulifupi mwake. 21  Kanyumba kapagetiko kanali ndi zipinda zitatu za alonda mbali iliyonse. Miyezo ya zipilala zake zamʼmbali komanso khonde lake, inali yofanana ndi ya kanyumba kapageti koyamba kaja. Kanyumbako kanali mikono 50 mulitali ndi mikono 25 mulifupi. 22  Miyezo ya mawindo ake, khonde lake ndi zithunzi zake za mtengo wa kanjedza,+ inali yofanana ndi zimene zinali pakanyumba kapageti kakumʼmawa. Anthu akafuna kulowa mʼkanyumbako amakwera masitepe 7 ndipo khonde lake linali kutsogolo kwa masitepewo. 23  Mʼbwalo lamkati munali geti limene linayangʼanizana ndi geti lakumpoto ndipo geti lina linayangʼanizana ndi geti lakumʼmawa. Munthu uja anayeza mtunda wochokera pageti limodzi kukafika pageti lina ndipo anapeza kuti unali mikono 100. 24  Kenako ananditengera kumbali yakumʼmwera ndipo ndinaona kuti kumeneko kuli kanyumba kapageti kamene kanayangʼana kumʼmwera.+ Iye anayeza zipilala zake zamʼmbali ndi khonde lake ndipo miyezo yake inali yofanana ndi ya tinyumba tina tija. 25  Kumbali iliyonse ya kanyumba kameneka komanso khonde lake kunali mawindo ofanana ndi a tinyumba tina tija. Kanyumbako kanali mikono 50 mulitali ndi mikono 25 mulifupi. 26  Munthu akafuna kulowa mʼkanyumbako amakwera masitepe 7+ ndipo khonde lake linali kutsogolo kwa masitepewo. Kumbali iliyonse ya khondelo kunali chipilala chimodzi ndipo pazipilalazo panali zithunzi za mtengo wa kanjedza. 27  Bwalo lamkati linali ndi geti limene linayangʼana kumʼmwera. Iye anayeza kuchokera pagetipo kulowera kumʼmwera kukafika pageti lina ndipo anapeza kuti panali mtunda wokwana mikono 100. 28  Kenako anandipititsa mʼbwalo lamkati kudzera pageti lakumʼmwera. Atayeza kanyumba kapageti kakumʼmwera anapeza kuti miyezo yake inali yofanana ndi tinyumba tina tija. 29  Miyezo ya zipinda za alonda za kanyumba kapagetiko, zipilala zake zamʼmbali ndi khonde lake inali yofanana ndi ya tinyumba tina tija. Kumbali iliyonse ya kanyumbako komanso khonde lake kunali mawindo. Kanyumbako kanali mikono 50 mulitali ndi mikono 25 mulifupi.+ 30  Tinyumba tonse tapageti tinali ndi khonde. Khonde lililonse linali mikono 25 mulitali ndi mikono 5 mulifupi. 31  Khonde lake linayangʼana kubwalo lakunja ndipo pazipilala zake zamʼmbali panali zithunzi za mtengo wa kanjedza+ ndipo anthu akafuna kulowa mʼkanyumbako amakwera masitepe 8.+ 32  Atandilowetsa mʼbwalo lamkati kudzera kumʼmawa, anayeza kanyumba kapagetiko ndipo anapeza kuti miyezo yake ndi yofanana ndi ya tinyumba tina tija. 33  Miyezo ya zipinda za alonda za kanyumba kapagetiko, zipilala zake zamʼmbali ndi khonde lake inali yofanana ndi miyezo ya tinyumba tina tija. Kumbali iliyonse ya kanyumbako komanso khonde lake kunali mawindo. Kanyumbako kanali mikono 50 mulitali ndi mikono 25 mulifupi. 34  Khonde lake linayangʼana kubwalo lakunja ndipo pazipilala zake zamʼmbali panali zithunzi za mtengo wa kanjedza ndipo anthu akafuna kulowa mʼkanyumbako amakwera masitepe 8. 35  Kenako anandipititsa kugeti la kumpoto.+ Atayeza kanyumba kapagetiko, anapeza kuti miyezo yake inali yofanana ndi ya tinyumba tina tija. 36  Miyezo ya zipinda za alonda za kanyumba kapagetiko, zipilala zake zamʼmbali ndi khonde lake inali yofanana ndi miyezo ya tinyumba tina tija. Kumbali iliyonse ya kanyumbako komanso khonde lake kunali mawindo. Kanyumbako kanali mikono 50 mulitali ndi mikono 25 mulifupi. 37  Zipilala zake zamʼmbali zinayangʼana kubwalo lakunja ndipo pazipilala zonsezo panali zithunzi za mtengo wa kanjedza. Anthu akafuna kulowa mʼkanyumbako amakwera masitepe 8. 38  Pafupi ndi zipilala zamʼmbali mwa tinyumba tapagetito panali chipinda chodyera komanso khomo lake, kumene ankatsukira nsembe zopsereza zathunthu.+ 39  Kumbali iliyonse ya khonde la kanyumba kapagetiko kunali matebulo awiri, pamene ankapherapo nsembe zopsereza zathunthu,+ nsembe zamachimo+ ndi nsembe zakupalamula.+ 40  Panja pa khomo lolowera mʼkanyumba kambali ya kumpoto panali matebulo awiri. Kumbali ina ya khonde la kanyumbako, kunalinso matebulo ena awiri. 41  Kumbali iliyonse ya kanyumba kapageti kunali matebulo 4 ndipo mkati mwa kanyumbako munalinso matebulo 4. Matebulo onse amene ankapherapo nyama zoti apereke nsembe analipo 8. 42  Matebulo 4 a nsembe zopsereza zathunthuwo anali amiyala yosema. Mulitali mwake anali mkono umodzi ndi hafu, mulifupi mwake anali mkono umodzi ndi hafu ndipo kuchoka pansi kufika pamwamba anali mkono umodzi. Pamatebulo amenewa ankaikapo zida zophera nyama ya nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zina. 43  Kuzungulira khoma lonse lamkati anaikamo mashelefu amene anali chikhatho chimodzi mulifupi. Nyama za nsembe zimene ankapereka ngati mphatso ankaziika pamatebulo aja. 44  Kunja kwa kanyumba kapageti kamkati kunali zipinda zodyeramo oimba.+ Zipindazi zinali mʼbwalo lamkati pafupi ndi geti lakumpoto ndipo zinayangʼana kumʼmwera. Chipinda china chinali pafupi ndi geti lakumʼmawa ndipo chinayangʼana kumpoto. 45  Munthu uja anandiuza kuti: “Chipinda chodyeramo ichi, chimene chayangʼana kumʼmwera, ndi cha ansembe amene amagwira ntchito zokhudza utumiki wapakachisi.+ 46  Chipinda chodyeramo chimene chayangʼana kumpoto ndi cha ansembe amene amagwira ntchito zokhudza utumiki wapaguwa lansembe,+ omwe ndi ana a Zadoki.+ Amenewa ndi Alevi amene anapatsidwa udindo woti azifika pamaso pa Yehova nʼkumamutumikira.”+ 47  Kenako munthu uja anayeza bwalo lamkati. Iye anapeza kuti mulitali linali mikono 100 ndipo mulifupi linalinso mikono 100. Bwalolo linali lofanana mbali zonse 4. Guwa lansembe linali kutsogolo kwa kachisi. 48  Kenako anandipititsa pakhonde la kachisi+ ndipo anayeza chipilala chamʼmbali cha khondelo nʼkupeza kuti chinali mikono 5 mbali imodzi komanso mikono 5 mbali inayo. Mulifupi mwa geti la kachisiyo munali mikono itatu mbali imodzi komanso mikono itatu mbali inayo. 49  Khondelo linali mikono 20 mulitali ndi mikono 11* mulifupi. Kuti anthu afike pakhondepo ankakwera masitepe. Pafupi ndi zipilala zamʼmbalizo panali nsanamira, imodzi mbali iyi, ina mbali inayo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “pa tsiku dzanja la Yehova linali pa ine.”
Kapena kuti, “mkuwa.”
“Fulakesi” ndi mbewu imene ankalima ku Iguputo ndipo ankaigwiritsa ntchito popanga ulusi wowombera nsalu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mtima wako ukhale pa zonse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nyumba.” Mawu akuti “nyumba” agwiritsidwa ntchito mʼchaputala 40 mpaka 48 pamene akunena za malo onse pamene pali kachisi kapena ponena za kachisi weniweniyo.
Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu, ndipo “chikhatho” ndi chofanana ndi masentimita 7.4. Tikaphatikiza mkono ndi chikhatho ndi masentimita pafupifupi 51.8 ndipo zinkaimira muyezo umene unkadziwika kuti “mkono wautali.” Choncho bango loyezera la mikono 6 linali lalitali mamita 3.11. Onani Zakumapeto B14.
Nʼkutheka kuti akunena pamwamba pa khoma la chipinda cha alonda.
Kapena kuti, “ndinaona zipinda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mulifupi.”
Mabaibulo ena amati, “12.”