Ezekieli 42:1-20

  • Nyumba imene inali ndi zipinda zodyera (1-14)

  • Anayeza mbali 4 za kachisi (15-20)

42  Kenako munthu uja anandipititsa kubwalo lakunja mbali yakumpoto.+ Ndiyeno anandipititsa kunyumba imene inali ndi zipinda zodyera yomwe inali pafupi ndi malo opanda kanthu,+ kumpoto kwa nyumba imene inali kumadzulo.*+  Mulitali mwa nyumbayo kumbali yakhomo lakumpoto, munali mikono 100* ndipo mulifupi mwake inali mikono 50.  Nyumbayi inali pakati pa bwalo lamkati lomwe linali mikono 20 mulifupi+ ndi malo owaka miyala amʼbwalo lakunja. Panali nyumba ziwiri zoyangʼanizana, zomwe zinali ndi zipinda zodyera. Nyumbazo zinali zosanjikizana katatu ndipo zinali ndi makonde omwe anali moyangʼanizana.  Pakati pa nyumbazo* panali njira+ imene inali mikono 10 mulifupi ndi mikono 100 mulitali* ndipo makomo olowera mʼnyumbazo anali mbali yakumpoto.  Zipinda zodyera zamʼmwamba zinali zocheperapo kusiyana ndi zapakati komanso zapansi chifukwa chakuti makonde anatenga malo ena a zipindazo.  Nyumbazo zinali zosanjikizana katatu koma zinalibe zipilala ngati zamʼmabwalo. Nʼchifukwa chake zipinda zamʼmwamba zinali zazingʼono kusiyana ndi zipinda zapakati komanso zapansi.  Mpanda wamiyala umene unali kunja, pafupi ndi zipinda zodyera unali mikono 50 mulitali mwake. Mpandawo unali mbali yakubwalo lakunja ndipo unayangʼanizana ndi zipinda zina zodyera.  Zipinda zodyera zimene zinali kumbali ya bwalo lakunja zinali mikono 50 mulitali, koma zimene zinali kumbali ya kachisi zinali mikono 100 mulitali mwake.  Kumʼmawa kwa nyumba yodyera, kunali khomo limene munthu ankatha kulowa akamachokera mʼbwalo lakunja. 10  Pafupi ndi malo opanda kanthu komanso nyumba imene inali kumadzulo, mkati* mwa mpanda wamiyala wa bwalo, kumbali yakumʼmawa, kunalinso nyumba zodyera.+ 11  Pakati pa nyumba zodyerazo panali njira yofanana ndi ya nyumba zodyera za mbali yakumpoto.+ Mulitali ndi mulifupi mwa nyumbazo, makomo otulukira komanso kamangidwe kake zinali zofanana ndi za nyumba za kumpoto zija. Makomo ake olowera 12  anali ofanana ndi makomo olowera a nyumba zimene zinali kumbali yakumʼmwera zija. Pamene panayambira njira panali khomo lolowera. Khomoli linali pafupi ndi mpanda wamiyala kumbali yakumʼmawa, pamene munthu ankatha kulowera.+ 13  Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Nyumba zodyera zakumpoto ndi zakumʼmwera zimene zili pafupi ndi malo opanda kanthu,+ ndi nyumba zodyera zopatulika, kumene ansembe otumikira Yehova amadyerako nsembe zopatulika koposa.+ Mʼnyumbazo amaikamo nsembe zopatulika koposa zomwe ndi nsembe zambewu, nsembe zamachimo ndi nsembe zakupalamula, chifukwa malo amenewa ndi oyera.+ 14  Ansembe akalowa mʼnyumbazo asamatuluke mʼmalo oyerawo kupita kubwalo lakunja asanavule zovala zimene amavala potumikira,+ chifukwa zovala zimenezi nʼzopatulika. Akafuna kupita kumalo amene anthu ena onse amaloledwa kufikako, azivala zovala zina.” 15  Atamaliza kuyeza malo amkati a kachisi,* ananditulutsa kunja kudzera pageti limene linayangʼana kumʼmawa+ ndipo anayeza malo onsewo. 16  Iye anayeza mbali yakumʼmawa ndi bango loyezera.* Mogwirizana ndi bango loyezeralo, malo onsewo anakwana mabango 500. 17  Anayezanso mbali yakumpoto ndipo mogwirizana ndi bango loyezera, malowo anakwana mabango 500. 18  Anayezanso mbali yakumʼmwera ndipo mogwirizana ndi bango loyezera, malowo anakwana mabango 500. 19  Kenako anazungulira kupita mbali yakumadzulo. Kumeneko anayeza malowo ndi bango loyezera ndipo anakwana mabango 500. 20  Anayeza malowo mbali zonse 4. Malo onsewo anali ndi mpanda+ umene unali mabango 500 mulitali ndi mabango 500 mulifupi mwake.+ Mpandawo unkasiyanitsa malo opatulika ndi malo wamba.+

Mawu a M'munsi

Imeneyi ndi nyumba imene inali kumbuyo kwa kachisi.
Imeneyi ndi mikono yaitali. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “zipindazo.”
Baibulo la Chigiriki la Septuagint limati: “Mikono 100 mulitali.” Malemba a Chiheberi amati: “Njira yokwana mkono umodzi.” Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mulifupi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Atamaliza kuyeza nyumba yamkati.”