Ezekieli 43:1-27

  • Ulemerero wa Yehova unadzaza mʼkachisi (1-12)

  • Guwa lansembe (13-27)

43  Kenako munthu uja anandipititsa kugeti limene linayangʼana kumʼmawa.+  Kumeneko ndinaona ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli ukubwera kuchokera kumʼmawa+ ndipo mawu ake ankamveka ngati mkokomo wa madzi.+ Dziko lapansi linawala chifukwa cha ulemerero wake.+  Zimene ndinaonazo zinali zofanana ndi zimene ndinaona mʼmasomphenya ena pamene ndinapita* kukawononga mzinda. Ndinaona zinthu zofanana ndi zimene ndinaona mʼmphepete mwa mtsinje wa Kebara.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi.  Ndiyeno ulemerero wa Yehova unalowa mʼkachisi* kudzera pageti limene linayangʼana kumʼmawa.+  Kenako mzimu unandidzutsa mʼkupita nane mʼbwalo lamkati ndipo ndinaona kuti ulemerero wa Yehova wadzaza mʼkachisi muja.+  Ndiyeno ndinamva wina akulankhula nane kuchokera mʼkachisi ndipo munthu uja anabwera nʼkudzaima pambali panga.+  Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, awa ndi malo a mpando wanga wachifumu+ ndiponso poikapo mapazi anga.+ Ndidzakhala pamalo amenewa, pakati pa Aisiraeli mpaka kalekale.+ Nyumba ya Isiraeli ndi mafumu awo sadzaipitsanso dzina langa loyera+ pochita uhule ndi milungu ina komanso ndi mitembo ya mafumu awo.  Iwo anaipitsa dzina langa loyera chifukwa cha zinthu zonyansa zimene anachita pamene anaika khomo lawo pafupi ndi khomo langa, nʼkuika felemu la khomo lawo pafupi ndi felemu la khomo langa moti pakati pa iwowo ndi ine nʼkungokhala khoma lokha lotisiyanitsa.+ Choncho ndinawawononga nditakwiya.+  Tsopano asiye kuchita zauhule ndi milungu ina ndipo achotse mitembo ya mafumu awo nʼkukaiika kutali ndi ine. Akatero ine ndidzakhala pakati pawo mpaka kalekale.+ 10  Koma iwe mwana wa munthu, ufotokozere nyumba ya Isiraeli za kachisiyu+ kuti achite manyazi chifukwa cha zolakwa zawo,+ ndipo iwo aonetsetse pulani ya kachisiyu* kuti adziwe mmene anamangidwira. 11  Ngati atachita manyazi chifukwa cha zonse zimene anachita, uwauze za pulani ya kachisiyu, kamangidwe kake, makomo ake olowera ndi otulukira.+ Uwasonyeze pulani yake yonse komanso uwadziwitse malangizo ndi malamulo ake. Uwalembe iwo akuona nʼcholinga choti adziwe mbali zosiyanasiyana za kachisiyo nʼkumatsatira malamulo apakachisipo.+ 12  Ili ndi lamulo lokhudza kachisi. Malo onse apamwamba pa phiri ndi oyera koposa.+ Limeneli ndi lamulo lokhudza kachisi. 13  Iyi ndi miyezo ya guwa lansembe pogwiritsa ntchito muyezo wa mkono+ (pa mkono uliwonse anawonjezerapo chikhatho chimodzi).* Chigawo chapansi cha guwa lansembe nʼchachitali mkono umodzi ndipo mulifupi mwake ndi mkono umodzi. Guwali lili ndi mkombero wokwana chikhatho* chimodzi mulifupi ndipo wazungulira mʼmbali mwake. Chimenechi ndi chigawo chapansi cha guwa la nsembe. 14  Kuchokera pachigawo chapansi, chigawo chachiwiri cha guwa la nsembe nʼchachitali mikono iwiri ndipo mʼmbali mwake nʼchachikulu mkono umodzi kuposa chigawo chachitatu kumbali zonse. Chigawo chachitatu nʼchachitali mikono 4 ndipo mʼmbali mwake nʼchachikulu mkono umodzi kuposa malo osonkhapo moto kumbali zonse. 15  Malo osonkhapo moto ndi aatali mikono 4 ndipo mʼmakona mwa malo osonkhapo motowo muli nyanga 4.+ 16  Malo osonkhapo motowo ndi ofanana mbali zonse. Mulitali mwake ndi mikono 12 ndipo mulifupi mwake ndi mikononso 12.+ 17  Mbali zonse 4 za chigawo chachitatu ndi zokwana mikono 14 mulitali ndiponso mikono 14 mulifupi. Kakhoma kamʼmphepete mwake ndi kokwana hafu ya mkono, ndipo pansi pake ndi pokwana mkono umodzi kumbali zonse. Masitepe a guwalo ali kumʼmawa.” 18  Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa wanena kuti: ‘Amenewa ndi malangizo amene akuyenera kutsatiridwa popanga guwa lansembe kuti aziperekerapo nsembe zopsereza zathunthu ndi kuwazapo magazi.+ 19  Ana a Zadoki, omwe ndi Alevi ansembe,+ amene amayandikira kwa ine nʼkumanditumikira, uwapatse ngʼombe yaingʼono yamphongo kuchokera pagulu la ziweto kuti ikhale nsembe yamachimo,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 20  ‘Utenge magazi akewo pangʼono nʼkuwapaka panyanga 4 za guwa lansembe komanso mʼmakona 4 a chigawo chachitatu cha guwalo. Uwapakenso pakakhoma konse kozungulira chigawo chachitatucho kuti uyeretse guwa lansembelo ku machimo ndiponso kuti uliperekere nsembe yophimba machimo.+ 21  Kenako utenge ngʼombe yaingʼono yamphongo ya nsembe yamachimo kuti ansembe akaipsereze pamalo apadera apakachisi, kunja kwa malo opatulika.+ 22  Pa tsiku lachiwiri, udzapereke mbuzi yamphongo yopanda chilema kuti ikhale nsembe yamachimo. Ansembewo adzayeretse guwa lansembelo ku machimo ngati mmene analiyeretsera ku machimo popereka ngʼombe yaingʼono yamphongo. 23  Ukamaliza kuyeretsa guwalo ku machimo, udzabweretse ngʼombe yaingʼono yamphongo yopanda chilema ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema kuchokera pagulu la ziweto. 24  Udzazibweretse kwa Yehova ndipo ansembe adzaziwaze mchere+ nʼkuzipereka kwa Yehova monga nsembe yopsereza yathunthu. 25  Tsiku lililonse, kwa masiku 7, uzipereka mbuzi yamphongo monga nsembe yamachimo+ komanso ngʼombe yaingʼono yamphongo ndi nkhosa yamphongo. Nyama zimenezi zizichokera pagulu la ziweto ndipo zizikhala zopanda chilema.* 26  Kwa masiku 7, aphimbe machimo a guwa la nsembe ndipo aliyeretse nʼkuyamba kuligwiritsa ntchito. 27  Masiku 7 amenewo akatha, kuyambira tsiku la 8+ kupita mʼtsogolo, ansembe azidzakuperekerani nsembe* zopsereza zathunthu ndi nsembe zamgwirizano paguwali, ndipo ine ndidzasangalala nanu,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “anapita.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼnyumba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ayeze kamangidwe ka kachisiyu.”
Imeneyi ndi mikono yaitali. Onani Zakumapeto B14.
Umenewu ndi muyezo umene ukuchokera pansonga ya chala chamanthu cha dzanja lanu kukafika pansonga ya chala chachingʼono, mutatambasula zala. Muyezo umenewu ndi wokwana masentimita 22.2. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “zopanda vuto lililonse.”
Kutanthauza kuti azidzaperekera anthuwo nsembe.