Ezekieli 45:1-25

  • Chopereka chopatulika komanso mzinda (1-6)

  • Malo amene mtsogoleri ankalandira (7, 8)

  • Atsogoleri azichita zinthu moona mtima (9-12)

  • Zinthu zimene anthu ankapereka komanso zimene mtsogoleri ankayenera kuchita (13-25)

45  “‘Mukamagawana dzikoli kuti likhale cholowa chanu,+ mudzatenge malo ena nʼkuwapereka kwa Yehova monga gawo loyera.+ Malowo adzakhale mikono 25,000* mulitali ndi mikono 10,000 mulifupi.+ Malo onsewo* adzakhale gawo loyera.  Mkati mwa gawo loyeralo mudzakhale malo ofanana mbali zonse kuti adzakhale malo oyera. Malowa adzakhale mikono 500 mbali zonse*+ ndipo kumbali iliyonse kudzakhale malo odyetserako ziweto okwana mikono 50.+  Kuchokera pamalo amenewa, udzayeze malo okwana mikono 25,000 mulitali ndi mikono 10,000 mulifupi. Mʼmalo amenewa mudzakhale malo opatulika amene ndi malo oyera koposa.  Malo amenewa adzakhale gawo lopatulika la ansembe mʼdzikoli,+ omwe ndi atumiki apamalo opatulika, amene amayandikira kwa Yehova nʼkumamutumikira.+ Malo amenewa adzakhala oti adzamangepo nyumba zawo komanso adzakhala malo opatulika omangapo kachisi.  Kudzakhale malo okwana mikono 25,000 mulitali ndi mikono 10,000 mʼlifupi.+ Malo amenewa adzakhale a Alevi, omwe ndi atumiki apakachisi. Aleviwo adzakhale ndi zipinda 20 zoti azidzadyeramo chakudya.+  Mudzapereke malo okwana mikono 25,000 mulitali (mofanana ndi chopereka chopatulika) ndi mikono 5,000 mulifupi+ kuti adzakhale malo a mzinda. Malo amenewa adzakhale a anthu a nyumba yonse ya Isiraeli.  Malo a mtsogoleri wa anthu adzakhale kumbali zonse za chopereka chopatulika komanso za malo amene aperekedwa kuti akhale a mzinda. Adzayandikane ndi chopereka chopatulika komanso malo a mzindawo. Malo a mtsogoleriwo adzakhale kumadzulo ndi kumʼmawa. Mulitali mwake kuchokera kumalire akumadzulo kukafika kumalire akumʼmawa adzakhale ofanana ndi kutalika kwa gawo la fuko la Isiraeli limene layandikana nawo.+  Malo amenewa adzakhale cholowa cha mtsogoleriyo mu Isiraeli. Atsogoleri anga sadzazunzanso anthu anga+ ndipo adzagawa dzikoli kwa anthu a nyumba ya Isiraeli mogwirizana ndi mafuko awo.’+  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndatopa nanu inu atsogoleri a Isiraeli! Siyani ziwawa ndi kupondereza anthu anga ndipo muzichita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+ Lekani kulanda zinthu za anthu anga,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 10  ‘Muzigwiritsa ntchito masikelo olondola, muyezo wa efa* wolondola ndi mitsuko* yoyezera yolondola.+ 11  Muyezo wa efa komanso wa mtsuko woyezera uzikhala wosasinthasintha. Muyezo wa mtsuko uzikhala wokwana gawo limodzi la magawo 10 a homeri* ndipo muyezo wa efa uzikhala wokwana gawo limodzi la magawo 10 a homeri. Muyezo wa homeri ukhale muyezo wa nthawi zonse. 12  Sekeli*+ imodzi izikwana magera* 20. Muziphatikiza masekeli 20, masekeli 25 ndi masekeli 15 kuti ukhale muyezo wanu umodzi wa mane.* 13  Muzipereka zinthu izi kuti chikhale chopereka chanu: Pa tirigu wanu wokwana homeri, muzipereka gawo limodzi mwa magawo 6 a muyezo wa efa. Ndipo pa balere wanu wokwana homeri muzipereka gawo limodzi mwa magawo 6 a muyezo wa efa. 14  Poyeza mafuta oti muzipereka, muzigwiritsa ntchito mtsuko woyezera. Mtsuko woyezera ndi wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa kori.* Mitsuko 10 ndi yokwana homeri chifukwa mitsuko 10 imakwana homeri imodzi. 15  Pa ziweto zonse mu Isiraeli, muzipereka nkhosa imodzi kuchokera pa nkhosa 200 zilizonse. Muzidzagwiritsa ntchito zinthu zonsezi popereka nsembe zambewu,+ nsembe zopsereza zathunthu+ ndi nsembe zamgwirizano+ pofuna kuphimba machimo a anthu,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 16  ‘Anthu onse amʼdzikoli azidzapereka zopereka zimenezi+ kwa mtsogoleri mu Isiraeli. 17  Koma mtsogoleri ndi amene adzakhale ndi udindo woyangʼanira nsembe zopsereza zathunthu,+ nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa. Iye azidzayangʼanira nsembezo pa nthawi ya zikondwerero,+ pa masiku amene mwezi watsopano waoneka, pa masiku a Sabata+ ndi pa nthawi ya zikondwerero zonse za nyumba ya Isiraeli.+ Mtsogoleriyo ndi amene azidzapereka kwa ansembe nsembe yamachimo, nsembe yambewu, nsembe yopsereza yathunthu ndi nsembe zamgwirizano kuti aphimbe machimo a nyumba ya Isiraeli.’ 18  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Mʼmwezi woyamba, pa tsiku loyamba la mweziwo, uzitenga ngʼombe yamphongo yaingʼono yopanda chilema kuchokera pagulu la ziweto, ndipo uziyeretsa kachisi ku machimo.+ 19  Wansembe azitenga ena mwa magazi a nsembe yamachimo nʼkuwapaka pafelemu la kachisi,+ mʼmakona 4 a chigawo chachitatu cha guwa lansembe komanso pafelemu la kanyumba kapageti ka bwalo lamkati. 20  Muzichita zimenezi pa tsiku la 7 la mweziwo chifukwa cha munthu aliyense amene wachimwa mwangozi kapena mosadziwa+ ndipo muziyeretsa kachisi ku machimo.+ 21  Mʼmwezi woyamba, pa tsiku la 14 la mweziwo, muzichita chikondwerero cha Pasika.+ Kwa masiku 7 muzidya mikate yopanda zofufumitsa.+ 22  Pa tsiku limeneli, mtsogoleri azipereka kwa ansembe ngʼombe yaingʼono yamphongo kuti ikhale nsembe yamachimo ake komanso a anthu onse amʼdzikoli.+ 23  Kwa masiku 7 a chikondwererocho, iye azipereka kwa ansembe nyama zoti ziperekedwe kwa Yehova ngati nsembe yopsereza yathunthu. Azipereka ngʼombe 7 zazingʼono zamphongo ndi nkhosa 7 zamphongo. Nyama zimenezi zizikhala zopanda chilema ndipo azizipereka tsiku lililonse kwa masiku 7 amenewo.+ Aziperekanso mbuzi yamphongo tsiku lililonse kuti ikhale nsembe yamachimo. 24  Popereka ngʼombe iliyonse yaingʼono yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo umodzi wa efa. Popereka nkhosa iliyonse yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo umodzi wa efa. Pa muyezo uliwonse wa efa azipereka mafuta okwana muyezo umodzi wa hini.* 25  Mʼmwezi wa 7, kuyambira pa tsiku la 15 la mweziwo, kwa masiku 7 pa nthawi ya chikondwerero,+ mtsogoleri azipereka kwa wansembe zinthu zofanana ndi zimenezi. Azipereka zinthu zimenezi kuti zikhale nsembe yamachimo, nsembe zopsereza zathunthu, nsembe yambewu ndiponso mafuta.’”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Malo onse amkati mwa malire ake.”
Imeneyi ndi mikono yaitali. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbali iyi 500, mbali inayo 500.”
Muyezo wa efa ndi wofanana ndi malita 22. Onani Zakumapeto B14.
Mtsuko umodzi unkakwana malita 22. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “mina.” Onani Zakumapeto B14.