Ezekieli 46:1-24

  • Nsembe zoperekedwa pazochitika zapadera (1-15)

  • Cholowa chochokera pamalo a mtsogoleri (16-18)

  • Malo amene ankawiritsirapo nsembe (19-24)

46  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Kanyumba kapageti la bwalo lamkati kamene kayangʼana kumʼmawa+ kazikhala kotseka+ kwa masiku 6 ogwira ntchito.+ Koma pa tsiku la Sabata ndi pa tsiku limene mwezi watsopano waoneka kazitsegulidwa.  Mtsogoleri azilowa kuchokera panja kudzera pakhonde la kanyumba kapagetiko+ ndipo aziima pafupi ndi felemu lagetilo. Ndiyeno ansembe azimuperekera nsembe yopsereza yathunthu ndi nsembe zake zamgwirizano. Mtsogoleriyo azigwada nʼkuwerama pakhomo la kanyumba kapageti kenako nʼkutuluka. Koma getilo lisamatsekedwe mpaka madzulo.  Anthu amʼdzikoli azigwadanso nʼkuwerama pamaso pa Yehova pakhomo lolowera mʼkanyumba kameneka pa masiku a Sabata ndi pa masiku amene mwezi watsopano waoneka.+  Nsembe yopsereza yathunthu imene mtsogoleri wa anthu azipereka kwa Yehova pa tsiku la Sabata, izikhala ana a nkhosa amphongo 6 ndi nkhosa yamphongo imodzi. Nyama zonsezi zizikhala zopanda chilema.+  Popereka nkhosa yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo umodzi wa efa.* Popereka ana a nkhosa amphongo aziperekanso nsembe yambewu imene angakwanitse. Pa nsembe iliyonse yambewu yokwana muyezo wa efa azipereka mafuta okwana muyezo wa hini.*+  Pa tsiku limene mwezi watsopano waoneka, azipereka ngʼombe yaingʼono yamphongo yopanda chilema kuchokera pagulu la ziweto. Aziperekanso ana a nkhosa amphongo 6 ndi nkhosa imodzi yamphongo. Nyama zonsezi zizikhala zopanda chilema.+  Popereka ngʼombe yaingʼono yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo umodzi wa efa. Akamapereka nkhosa yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo umodzi wa efa. Popereka ana a nkhosa amphongo aziperekanso nsembe yambewu imene angakwanitse. Pa nsembe iliyonse yambewu yokwana muyezo wa efa, azipereka mafuta okwana muyezo wa hini.  Mtsogoleri wa anthu akamalowa, azidzera mbali yakukhonde ya kanyumba kapageti ndipo akamatuluka azidzeranso komweko.+  Anthu amʼdzikoli akafika pamaso pa Yehova pa nthawi ya zikondwerero,+ anthu amene alowa kudzalambira kudzera pageti la kumpoto+ azidzatulukira pageti lakumʼmwera.+ Amene alowera pageti lakumʼmwera azidzatulukira pageti lakumpoto. Munthu aliyense asadzatulukire pageti limene analowera chifukwa aliyense akuyenera kutulukira pageti limene lili kutsogolo kwake. 10  Anthuwo akamalowa, mtsogoleri amene ali pakati pawo azilowa nawo limodzi, ndipo akamatuluka nayenso azituluka. 11  Mukamachita zikondwerero komanso pa nthawi ya zikondwerero zanu, azipereka ngʼombe yaingʼono yamphongo pamodzi ndi nsembe yambewu yokwana muyezo umodzi wa efa. Aziperekanso nkhosa yamphongo pamodzi ndi nsembe yambewu yokwana muyezo umodzi wa efa. Akamapereka ana a nkhosa amphongo aziperekanso nsembe yambewu imene angakwanitse. Pa nsembe iliyonse yambewu yokwana muyezo wa efa azipereka mafuta okwana muyezo wa hini.+ 12  Ngati mtsogoleri wa anthu akupereka kwa ansembe nsembe yopsereza yathunthu+ kapena nsembe zamgwirizano kuti zikhale nsembe yaufulu yoperekedwa kwa Yehova, azimutsegulira geti lakumʼmawa. Mtsogoleriyo azipereka kwa ansembe nsembe yake yopsereza yathunthu ndi nsembe zake zamgwirizano ngati mmene amachitira pa tsiku la Sabata.+ Akatuluka getilo lizitsekedwa.+ 13  Tsiku lililonse muzipereka kwa Yehova mwana wa nkhosa wamphongo wopanda chilema wosakwanitsa chaka kuti ikhale nsembe yopsereza yathunthu.+ Muzichita zimenezi mʼmawa uliwonse. 14  Mukamapereka mwana wa nkhosayo, muziperekanso nsembe yambewu mʼmawa uliwonse yokwanira gawo limodzi mwa magawo 6 a muyezo wa efa. Muziperekanso mafuta okwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini kuti aziwazidwa mu ufa wosalala monga nsembe yambewu imene iziperekedwa kwa Yehova nthawi zonse. Limeneli ndi lamulo limene lidzakhalepo mpaka kalekale. 15  Mʼmawa uliwonse, iwo azipereka kwa ansembe mwana wa nkhosa wamphongo, nsembe yambewu komanso mafuta, kuti zikhale nsembe yopsereza yathunthu ya nthawi zonse.’ 16  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Mtsogoleri wa anthu akapereka mphatso kwa mwana wake aliyense wamwamuna monga cholowa chake, mphatsoyo idzakhala chuma cha ana akewo. Chimenecho ndi chuma cha anawo ndipo chidzakhala cholowa chawo. 17  Koma akapereka mphatso kwa mmodzi wa antchito ake kuchokera pacholowa chake, mphatsoyo idzakhala ya wantchitoyo mpaka chaka cha ufulu,+ kenako idzabwezedwa kwa mtsogoleriyo. Koma cholowa chimene wapereka kwa ana ake chidzakhala chawo mpaka kalekale. 18  Mtsogoleri wa anthu asamakakamize munthu aliyense kuti achoke pamalo omwe ndi cholowa chake nʼkutenga malowo kuti akhale ake. Ana ake aamuna aziwapatsa cholowa kuchokera pamalo amene ali nawo, kuti pakati pa anthu anga pasapezeke munthu aliyense amene wathamangitsidwa pamalo ake.’” 19  Kenako munthu uja anandilowetsa mkati kudzera pakhomo+ limene lili pafupi ndi geti lopita kunyumba zopatulika* zomwe ansembe ankadyeramo, zimene zinayangʼana kumpoto.+ Kumeneko ndinaona malo kumbuyo, mbali yakumadzulo. 20  Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Awa ndi malo amene ansembe aziwiritsirapo nsembe yakupalamula ndi nsembe yamachimo komanso pamene aziphikirapo nsembe yambewu.+ Aziphikira pamenepa kuti asamatulutse chilichonse kupita nacho kubwalo lakunja nʼkuchititsa kuti anthu akhale oyera.”+ 21  Kenako anandipititsa mʼbwalo lakunja nʼkundidutsitsa mʼmakona 4 a bwalolo ndipo ndinaona kuti pakona iliyonse ya bwalo lakunjalo panali bwalo. 22  Mʼmakona onse 4 a bwalolo munali mabwalo angʼonoangʼono amene anali mikono 40* mulitali ndi mikono 30 mulifupi. Mabwalo 4 onsewo anali aakulu mofanana.* 23  Panali kakhoma kuzungulira mkati monse mwa tinyumba tonse 4 tapakonato. Mʼmunsi mwa timakoma timeneto anamangamo malo oti aziwiritsirapo nsembe. 24  Kenako anandiuza kuti: “Izi ndi nyumba zimene atumiki apakachisi amawiritsiramo nsembe zimene anthu amapereka.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “lopita kuzipinda zopatulika.”
Imeneyi ndi mikono yaitali. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “Onse 4 komanso tinyumba take tapakona tinali ndi muyezo wofanana.”