Ezekieli 47:1-23
47 Kenako anandipititsanso kukhomo lolowera mʼkachisi+ ndipo kumeneko ndinaona madzi akutuluka pansi pakhomo la kachisi+ nʼkumalowera chakumʼmawa, chifukwa kachisiyo anayangʼana kumʼmawa. Madziwo ankatuluka pansi kuchokera kumbali yakumanja kwa kachisiyo, kumʼmwera kwa guwa lansembe.
2 Ndiyeno ananditulutsa kudzera pageti lakumpoto+ ndipo anandipititsa kunja nʼkuzungulira kukafika kugeti lakunja limene linayangʼana kumʼmawa.+ Kumeneko ndinaonako madzi akuyenda kuchokera kumbali yakumanja kwa getilo.
3 Munthu uja anapita mbali yakumʼmawa atatenga chingwe choyezera mʼmanja mwake.+ Kenako anayeza mtsinjewo mikono* 1,000 kuchokera pakanyumba kapageti, ndipo anandiuza kuti ndiwoloke mtsinjewo. Madzi ake anali olekeza mʼmapazi.
4 Kenako anayezanso mtsinjewo mikono ina 1,000 ndipo anandiuza kuti ndiwoloke. Madzi ake anali olekeza mʼmawondo.
Anayezanso mtsinjewo mikono ina 1,000 nʼkundiuza kuti ndiwoloke ndipo madzi ake anali olekeza mʼchiuno.
5 Atayezanso mtsinjewo mikono ina 1,000, mtsinjewo unakula kwambiri moti sindinathe kuwoloka chifukwa chakuti madzi ake anali ozama kwambiri moti munthu amafunika kusambira. Unali mtsinje waukulu woti munthu sakanatha kuwoloka.
6 Ndiyeno anandifunsa kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimenezi?”
Kenako munthu uja ananditulutsa mʼmadzimo nʼkupita nane mʼmphepete mwa mtsinjewo.
7 Nditatuluka mʼmadzimo ndinaona kuti mʼmphepete mwa mtsinjewo munali mitengo yambirimbiri mbali zonse.+
8 Ndiyeno anandiuza kuti: “Madzi awa akupita kuchigawo cha kumʼmawa ndipo adutsa ku Araba*+ nʼkukafika kunyanja. Madziwa akakafika kunyanjako,+ akachititsa kuti madzi amʼnyanjamo akhale abwino.
9 Kulikonse kumene madziwo apita,* zamoyo zamʼmadzi za mtundu uliwonse zidzakhala ndi moyo. Nsomba zidzachuluka chifukwa madzi amenewa adzafika kunyanja. Madzi amʼnyanja adzakhala abwino ndipo kulikonse kumene mtsinjewo ukupita, chilichonse chidzakhala ndi moyo.
10 Asodzi adzaima mʼmbali mwa nyanjayo kuchokera ku Eni-gedi+ mpaka ku Eni-egilaimu, kumene kudzakhale malo oyanikapo makoka. Kudzakhala nsomba zambirimbiri zamitundu yosiyanasiyana ngati nsomba za ku Nyanja Yaikulu.*+
11 Madzi amʼzithaphwi ndi mʼmadambo amʼmphepete mwa nyanjayo sadzasintha nʼkukhala abwino. Madzi amenewo adzakhalabe amchere.+
12 Kumbali zonse zamʼmphepete mwa mtsinjewo mudzamera mitengo yosiyanasiyana ya zipatso. Masamba ake sadzafota ndipo zipatso zake sizidzatha. Mwezi uliwonse mitengoyo izidzabereka zipatso chifukwa chakuti madzi ake akuchokera kumalo opatulika.+ Zipatso zake zidzakhala chakudya ndipo masamba ake adzakhala mankhwala.”+
13 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Limeneli ndi dera limene mudzagawire mafuko 12 a Isiraeli ngati cholowa chawo ndipo zigawo ziwiri zidzakhale za mbadwa za Yosefe.+
14 Mudzatenge dzikoli kuti likhale cholowa chanu ndipo aliyense adzalandire gawo lofanana ndi la mnzake. Ine ndinalumbira kuti ndidzapereka dziko limeneli kwa makolo anu+ ndipo tsopano ndikulipereka kwa inu kuti likhale cholowa chanu.
15 Malire a dzikoli kumbali yakumpoto ndi awa: Akuyambira ku Nyanja Yaikulu kudzera njira ya ku Heteloni+ nʼkumalowera ku Zedadi,+
16 ku Hamati,+ ku Berota,+ ku Siburaimu, amene ali pakati pa dera la Damasiko ndi dera la Hamati, mpaka kukafika ku Hazere-hatikoni kufupi ndi malire a Haurani.+
17 Choncho malirewo adzayambire kunyanja mpaka ku Hazara-enoni,+ kumene ndi kumalire akumpoto kwa Damasiko komanso kumalire a Hamati.+ Amenewa ndi malire akumpoto.
18 Malire a mbali yakumʼmawa ali pakati pa Haurani ndi Damasiko, kudutsa mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodano pakati pa Giliyadi+ ndi dziko la Isiraeli. Mudzayeze mtunda wochokera kumalirewo kukafika kunyanja yakumʼmawa.* Amenewa ndi malire akumʼmawa.
19 Malire a mbali yakumʼmwera, adzayambire ku Tamara kukafika kumadzi a Meribati-kadesi,+ kenako akafike kuchigwa cha Iguputo mpaka ku Nyanja Yaikulu.+ Amenewa ndi malire akumʼmwera.
20 Kumbali yakumadzulo malire anu ndi Nyanja Yaikulu, kuchokera mʼmalire a mbali yakumʼmwera mpaka kukafika malo amene ayangʼanizana ndi Lebo-hamati.*+ Amenewa ndi malire akumadzulo.
21 Inu mugawane dzikoli pakati pa mafuko onse 12 a Isiraeli.
22 Mugawane dzikoli kuti likhale cholowa chanu ndi cha alendo omwe akukhala pakati panu, amene abereka ana pa nthawi imene amakhala nanu. Kwa inu, alendowo akhale ngati nzika za Isiraeli. Iwo alandire cholowa pamodzi ndi inu pakati pa mafuko a Isiraeli.
23 Mlendo aliyense muzimupatsa cholowa mʼdera la fuko limene akukhala,” akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.