Ezekieli 48:1-35
48 “Magawo amene mafuko adzalandire potsatira mayina awo, kuyambira kumalire akumpoto ndi awa: Gawo la fuko la Dani+ likhale mʼmbali mwa msewu wa ku Heteloni wopita ku Lebo-hamati*+ mpaka kukafika ku Hazara-enani, kumalire akumpoto a Damasiko kufupi ndi Hamati.+ Gawolo liyambire kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo.
2 Gawo la fuko la Aseri+ lichite malire ndi gawo la fuko la Dani, kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo.
3 Gawo la fuko la Nafitali+ lichite malire ndi gawo la fuko la Aseri, kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo.
4 Gawo la fuko la Manase+ lichite malire ndi gawo la fuko la Nafitali, kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo.
5 Gawo la fuko la Efuraimu lichite malire ndi gawo la fuko la Manase,+ kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo.
6 Gawo la fuko la Rubeni lichite malire ndi gawo la fuko la Efuraimu,+ kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo.
7 Gawo la fuko la Yuda lichite malire ndi gawo la fuko la Rubeni,+ kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo.
8 Mupereke gawo lina kuti likhale chopereka chanu. Gawolo lichite malire ndi gawo la fuko la Yuda kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo ndipo likhale mikono 25,000* mulifupi.+ Mulitali mwake lifanane ndi magawo a mafuko aja kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo. Malo opatulika akhale pakati pa gawo limeneli.
9 Gawo loti mupereke kwa Yehova monga chopereka chanu likhale mikono 25,000 mulitali ndi mikono 10,000 mulifupi.
10 Gawo limeneli likhale chopereka chopatulika cha ansembe.+ Mbali yakumpoto, gawoli likhale mikono 25,000. Mbali yakumadzulo likhale mikono 10,000. Mbali yakumʼmawa likhale mikono 10,000 ndipo mbali yakumʼmwera likhale mikono 25,000. Malo opatulika a Yehova adzakhala pakati pa gawo limeneli.
11 Gawo limeneli likhale la ansembe opatulika, ana a Zadoki,+ amene ankanditumikira ndipo sanandisiye pamene Aisiraeli ndi Alevi anandisiya.+
12 Ansembewo akhale ndi gawo lawo kuchokera pa gawo limene mwapereka kuti likhale gawo lopatulika koposa, ndipo lichite malire ndi gawo la Alevi.
13 Alevi akhale ndi gawo pafupi ndi gawo la ansembe. Mulitali mwake likhale mikono 25,000 ndipo mulifupi likhale mikono 10,000. (Malo onsewo akhale aatali mikono 25,000 ndipo mulifupi mwake akhale okwana mikono 10,000.)
14 Aleviwo asamagulitse, kusinthanitsa kapena kupereka kwa munthu wa fuko lina mbali iliyonse ya malo abwino kwambiriwo, chifukwa malo amenewo ndi opatulika kwa Yehova.
15 Malo otsala okwana mikono 5,000 mulifupi ndi mikono 25,000 mulitali, akhale malo a mzinda oti munthu aliyense angagwiritse ntchito.+ Malo amenewa akhale oti anthu azimangako nyumba komanso kudyetserako ziweto. Mzinda ukhale pakati pa malowa.+
16 Miyezo ya mzindawo ndi iyi: Mbali yakumpoto ikhale mikono 4,500. Mbali yakumʼmwera ikhale mikono 4,500. Mbali yakumʼmawa ikhale mikono 4,500, ndipo mbali yakumadzulo ikhalenso mikono 4,500.
17 Malo odyetserako ziweto a mzindawo akhale mikono 250 mbali yakumpoto, mikono 250 mbali yakumʼmwera, mikono 250 mbali yakumʼmawa komanso mikono 250 mbali yakumadzulo.
18 Malo otsala akhale aatali mofanana ndi malo omwe ndi chopereka chopatulika.+ Akhale mikono 10,000 kumʼmawa ndiponso mikono 10,000 kumadzulo. Malo amenewo achite malire ndi malo omwe ndi chopereka chopatulika. Zokolola zapamalowo zizikhala chakudya cha amene akugwira ntchito mumzindawo.
19 Anthu ochokera mʼmafuko onse a Isiraeli amene akugwira ntchito mumzinda ndi omwe azidzalima malo amenewa.+
20 Malo onse oti aperekedwe akhale mikono 25,000 mbali zonse 4. Mupereke malo amenewa kuti akhale chopereka chopatulika ndiponso malo a mzinda.
21 Malo amene atsala kumbali zonse za chopereka chopatulika ndiponso ya malo a mzinda akhale a mtsogoleri wa anthu.+ Malowa adzachita malire ndi malo omwe ndi chopereka, amene akukwana mikono 25,000 kumʼmawa ndi kumadzulo. Malowo achite malire ndi malo amene anaperekedwa aja ndipo akhale a mtsogoleri wa anthu. Malo omwe ndi chopereka chopatulika komanso malo opatulika a kachisi aja akhale pakati pa malo a mtsogoleriwa.
22 Malo a Alevi komanso malo a mzinda akhale pakati pa malo a mtsogoleri. Malo a mtsogoleriwo achite malire ndi gawo la fuko la Yuda+ komanso gawo la fuko la Benjamini.
23 Pa mafuko ena otsalawo, gawo la fuko la Benjamini liyambire kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo.+
24 Gawo la fuko la Simiyoni lichite malire ndi gawo la fuko la Benjamini,+ kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo.
25 Gawo la fuko la Isakara+ lichite malire ndi gawo la fuko la Simiyoni, kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo.
26 Gawo la fuko la Zebuloni lichite malire ndi gawo la fuko la Isakara,+ kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo.+
27 Gawo la fuko la Gadi lichite malire ndi gawo la fuko la Zebuloni,+ kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo.
28 Malire akumʼmwera a dzikolo akhale malire a gawo la fuko la Gadi ndipo achokere ku Tamara+ kukafika kumadzi a Meribati-kadesi,+ kuchigwa cha Iguputo+ mpaka ku Nyanja Yaikulu.*
29 Limeneli ndi dziko lomwe mukuyenera kugawa kwa mafuko onse a Isiraeli kuti likhale cholowa chawo+ ndipo magawo awo akhale amenewa,”+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
30 “Makomo otulukira mumzinda akhale motere: Kumbali yakumpoto mzindawo ukhale mikono 4,500.+
31 Mayina a mageti a mzindawo akhale ofanana ndi mayina a mafuko a Isiraeli. Mbali yakumpoto kukhale mageti atatu. Geti limodzi likhale ndi dzina lakuti Rubeni, geti lina Yuda ndipo lina Levi.
32 Kumbali yakumʼmawa mzindawo ukhale mikono 4,500 ndipo kukhale mageti atatu awa: Geti limodzi likhale ndi dzina lakuti Yosefe, geti lina Benjamini ndipo lina Dani.
33 Kumbali yakumʼmwera mzindawo ukhale mikono 4,500 ndipo kukhale mageti atatu awa: Geti limodzi likhale ndi dzina lakuti Simiyoni, geti lina Isakara ndipo lina Zebuloni.
34 Kumbali yakumadzulo mzindawo ukhale mikono 4,500 ndipo kukhale mageti awa: Geti limodzi likhale ndi dzina lakuti Gadi, geti lina Aseri ndipo geti lina Nafitali.
35 Kuzungulira mzindawo pakhale mtunda wokwana mikono 18,000. Kuyambira tsiku limenelo, dzina la mzindawo lidzakhala lakuti, Yehova Ali Kumeneko.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “wopita polowera ku Hamati.”
^ Imeneyi ndi mikono yaitali. Onani Zakumapeto B14.
^ Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.