Ezekieli 6:1-14
6 Yehova anandiuzanso kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, yangʼana kumapiri a Isiraeli ndipo ulosere zinthu zimene zidzawachitikire.
3 Uwauze kuti, ‘Inu mapiri a Isiraeli, mvetserani zimene akunena Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa: Izi nʼzimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, akunena kwa mapiri, zitunda, mitsinje ndi zigwa: “Ine ndidzakubweretserani lupanga ndipo ndidzawononga malo anu okwezeka.
4 Maguwa anu ansembe adzagumulidwa, maguwa anu ofukizirapo zonunkhira adzaphwanyidwa+ ndipo mitembo ya anthu anu amene adzaphedwe ndidzaiponyera pamaso pa mafano anu onyansa.*+
5 Mitembo ya Aisiraeli ndidzaiponyera pamaso pa mafano awo onyansa, ndipo mafupa anu ndidzawamwaza kuzungulira maguwa anu ansembe.+
6 Mʼmalo onse amene mukukhala, mizinda idzawonongedwa.+ Malo okwezeka adzagumulidwa ndipo adzakhala mabwinja.+ Maguwa anu ansembe adzagumulidwa nʼkuphwanyidwa. Mafano anu onyansa adzawonongedwa, maguwa anu ofukizirapo zonunkhira adzagwetsedwa ndipo ntchito za manja anu zidzawonongedwa.
7 Anthu amene aphedwa adzagwa pakati panu,+ ndipo inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+
8 Koma ndidzachititsa kuti pakhale anthu ena opulumuka, chifukwa ena a inu simudzaphedwa ndi lupanga pakati pa anthu a mitundu ina mukadzabalalikira mʼmayiko osiyanasiyana.+
9 Anthu amene adzapulumuke adzandikumbukira pakati pa anthu amitundu ina amene anawagwira ukapolo.+ Adzazindikira kuti zinandipweteka kwambiri mumtima chifukwa cha mtima wawo wosakhulupirika* womwe unachititsa kuti andipandukire+ komanso maso awo amene amalakalaka mafano awo onyansa.+ Iwo adzachita manyazi komanso kuipidwa chifukwa cha zinthu zonse zoipa ndi zonyansa zimene anachita.+
10 Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova komanso kuti zimene ndinanena kuti ndidzawabweretsera tsoka limeneli, sizinali nkhambakamwa chabe.”’+
11 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ombani mʼmanja mowawidwa mtima ndipo pondani pansi posonyeza kuti muli ndi chisoni chachikulu. Mulire chifukwa cha zoipa zonse komanso zonyansa zimene Aisiraeli anachita chifukwa iwo adzaphedwa ndi lupanga, njala ndi mliri.+
12 Yemwe ali kutali adzaphedwa ndi mliri. Yemwe ali pafupi adzaphedwa ndi lupanga. Yemwe wapulumuka zinthu zimenezi adzafa ndi njala, ndipo ndidzawasonyeza mkwiyo wanga wonse.+
13 Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova,+ mitembo ya anthu awo ikadzakhala pakati pa mafano awo onyansa, kuzungulira maguwa awo onse ansembe,+ paphiri lililonse lalitali, pansonga zonse za mapiri, pansi pa mtengo uliwonse waukulu wamasamba obiriwira, ndiponso pansi pa nthambi za mitengo ikuluikulu pamene ankaperekerapo nsembe zonunkhira kuti asangalatse mafano awo onse onyansa.+
14 Ndidzatambasula dzanja langa nʼkuwalanga ndipo dziko lawo ndidzalisandutsa bwinja. Malo awo onse amene amakhala adzasanduka bwinja loipa kwambiri kuposa chipululu chimene chili pafupi ndi Dibula. Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”