Ezekieli 8:1-18

  • Ezekieli anapititsidwa ku Yerusalemu mʼmasomphenya (1-4)

  • Anaona zinthu zonyansa mʼkachisi (5-18)

    • Azimayi ankalilira mulungu wotchedwa Tamuzi (14)

    • Amuna ankalambira dzuwa (16)

8  Mʼchaka cha 6, mʼmwezi wa 6, pa tsiku la 5 la mweziwo dzanja la Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, linandikhudza. Pa nthawiyo ndinali nditakhala mʼnyumba mwanga ndipo akuluakulu a Yuda anali atakhala pamaso panga.  Nditayangʼana ndinaona chinachake chooneka ngati moto. Ndipo moto unkayaka kuchokera pachimene chinkaoneka ngati chiuno chake kupita mʼmunsi.+ Kuchokera mʼchiuno mwake kupita mʼmwamba, maonekedwe ake anali owala ngati siliva wosakanikirana ndi golide.+  Kenako iye anatambasula chinachake chooneka ngati dzanja ndipo anagwira tsitsi lakumutu kwanga nʼkundinyamula. Ndiyeno mzimu unandinyamulira mʼmalere pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba, nʼkundipititsa ku Yerusalemu mʼmasomphenya ochokera kwa Mulungu. Mzimuwo unandifikitsa pakhomo la geti la bwalo lamkati+ loyangʼana kumpoto pamene panali fano loimira nsanje, limene limachititsa nsanje.+  Kumeneko ndinaonako ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli,+ wofanana ndi umene ndinaona kuchigwa uja.+  Kenako iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kweza maso ako uyangʼane kumpoto.” Choncho ndinakweza maso anga nʼkuyangʼana kumpoto, ndipo ndinaona kuti kumpoto kwa geti la guwa lansembe kunali fano loimira nsanje lija pakhomo la getilo.  Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zinthu zoipa komanso zonyansa kwambiri zimene anthu a nyumba ya Isiraeli akuchita kuno,+ zimene zikupangitsa kuti nditalikirane ndi malo anga opatulika?+ Koma uonanso zinthu zina zoipa zomwe ndi zonyansa kwambiri kuposa zimenezi.”  Kenako anandipititsa pakhomo lolowera mʼbwalo ndipo nditayangʼana ndinaona bowo pakhoma.  Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, tabowola khomalo.” Ine ndinabowoladi khomalo ndipo ndinaona khomo.  Iye anandiuza kuti: “Lowa uone zinthu zoipa ndi zonyansa zimene anthu akuchita kuno.” 10  Choncho ndinalowa ndipo nditayangʼana ndinaona zithunzi za zinthu zosiyanasiyana zokwawa, nyama zonyansa+ komanso mafano onse onyansa* a Aisiraeli.+ Zithunzizo zinajambulidwa pamakoma onse mochita kugoba. 11  Ndipo akuluakulu 70 a nyumba ya Isiraeli anali ataimirira patsogolo pa mafanowo. Pakati pawo panalinso Yaazaniya mwana wa Safani.+ Aliyense ananyamula chiwaya chofukizira nsembe mʼmanja mwake ndipo utsi wonunkhira wa zofukizazo unkakwera mʼmwamba.+ 12  Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Isiraeli akuchita mumdima? Kodi waona zimene aliyense wa iwo akuchita mʼzipinda zake zamkati mmene muli mafano ake? Iwo akunena kuti, ‘Yehova sakutiona. Yehova wachokamo mʼdziko muno.’”+ 13  Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Uonanso zinthu zina zoipa komanso zonyansa kwambiri zimene akuchita.” 14  Choncho anandipititsa pakhomo la geti la nyumba ya Yehova limene linali mbali yakumpoto ndipo kumeneko ndinaona azimayi atakhala pansi nʼkumalirira mulungu wotchedwa Tamuzi. 15  Iye anandiuzanso kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zimenezi? Uonanso zinthu zina zoipa zomwe ndi zonyansa kwambiri kuposa zimenezi.”+ 16  Choncho anandipititsa kubwalo lamkati la nyumba ya Yehova.+ Ndiyeno ndinaona kuti pakhomo lolowera mʼkachisi wa Yehova, pakati pa khonde ndi guwa lansembe, panali amuna pafupifupi 25 atafulatira kachisi wa Yehova ndipo nkhope zawo zinali zitayangʼana kumʼmawa. Iwo ankagwadira dzuwa limene linali kumʼmawa.+ 17  Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimenezi? Kodi ndi chinthu chachingʼono kuti anthu a nyumba ya Yuda azichita zinthu zonyansazi? Kodi ndi chinthu chachingʼono kuti adzaze dzikoli ndi chiwawa+ nʼkupitiriza kundikwiyitsa? Anthuwatu akulozetsa nthambi* pamphuno panga. 18  Choncho ineyo ndidzawalanga nditakwiya kwambiri. Diso langa silidzawamvera chisoni ndipo sindidzawachitira chifundo.+ Ngakhale iwo adzandilirire mofuula, ine sindidzamva.”+

Mawu a M'munsi

Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Zikuoneka kuti nthambi imeneyi ankaigwiritsa ntchito polambira mafano.