Ezekieli 9:1-11

  • Anthu 6 opereka chilango komanso munthu amene anali ndi kachikwama konyamuliramo inki ndi zolembera (1-11)

    • Chiweruzo chinayambira pamalo opatulika (6)

9  Kenako iye analankhula mokuwa ine ndikumva, kuti: “Itana anthu amene akuyenera kupereka chilango pamzindawu. Aliyense abwere atanyamula chida chake chowonongera!”  Ndiyeno ndinaona amuna 6 akubwera kuchokera kugeti lakumtunda+ loyangʼana kumpoto, aliyense atanyamula chida chake chowonongera. Pakati pawo panali munthu mmodzi atavala zovala zansalu ndipo mʼchiuno mwake munali kachikwama ka mlembi, konyamuliramo inki ndi zolembera. Anthuwo analowa mkati nʼkuima pambali pa guwa lansembe lakopa.*+  Kenako ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli+ unachoka pamwamba pa akerubi pamene unali ndipo unapita pakhomo la malo opatulika.+ Ndiyeno Mulungu anayamba kulankhula mofuula kwa munthu amene anavala zovala zansalu uja, yemwe mʼchiuno mwake munali kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki ndi zolembera.  Yehova anauza munthu uja kuti: “Uyendeyende mumzinda wonse wa Yerusalemu ndipo ulembe chizindikiro pazipumi za anthu amene akuusa moyo komanso kubuula+ chifukwa cha zonyansa zonse zimene zikuchitika mumzindawu.”+  Ndiyeno iye anauza amuna ena aja ine ndikumva, kuti: “Mʼtsatireni ameneyu. Muyendeyende mumzindamo nʼkumapha anthu. Diso lanu lisamve chisoni ndipo musasonyeze aliyense chifundo.+  Muphe amuna achikulire, anyamata, anamwali, tiana ndi azimayi ndipo pasatsale aliyense.+ Koma musayandikire munthu aliyense amene ali ndi chizindikiro+ ndipo muyambire pamalo anga opatulika.”+ Choncho iwo anayambira kupha akuluakulu amene anali kutsogolo kwa nyumbayo.+  Kenako anawauza kuti: “Ipitsani nyumbayi ndipo mudzaze mabwalo ake ndi mitembo ya anthu ophedwa.+ Pitani!” Choncho iwo anapitadi nʼkukapha anthu mumzindamo.  Pamene amunawo ankapha anthu, ine ndekha ndi amene ndinatsala ndi moyo. Choncho ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi ndipo ndinafuula kuti: “Mayo ine, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Kodi muwononga anthu onse amene anatsala mu Isiraeli pamene mukukhuthulira ukali wanu pa Yerusalemu?”+  Iye anandiyankha kuti: “Zolakwa za nyumba ya Isiraeli ndi Yuda nʼzazikulu kwambiri.+ Dziko lawo ladzaza ndi kukhetsa magazi+ ndipo mumzindamo mwadzaza zinthu zopanda chilungamo.+ Iwo akunena kuti, ‘Yehova wachokamo mʼdziko muno ndipo Yehova sakuona.’+ 10  Koma ine diso langa silimva chisoni ndipo sindiwasonyeza chifundo.+ Ndiwabwezera mogwirizana ndi zochita zawo.” 11  Kenako ndinaona munthu amene anavala zovala zansalu uja, yemwe mʼchiuno mwake munali kachikwama konyamuliramo inki ndi zolembera atabwera, ndipo ananena kuti: “Ndachita zonse zimene munandilamula.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “lamkuwa.”