Genesis 10:1-32

  • Mitundu ya anthu (1-32)

    • Mbadwa za Yafeti  (2-5)

    • Mbadwa za Hamu (6-20)

      • Nimurodi anatsutsana ndi Yehova (8-12)

    • Mbadwa za Semu (21-31)

10  Iyi ndi mbiri ya ana a Nowa, omwe ndi Semu,+ Hamu ndi Yafeti. Iwowa anabereka ana pambuyo pa Chigumula.+  Ana a Yafeti anali Gomeri,+ Magogi,+ Madai, Yavani, Tubala,+ Meseki+ ndi Tirasi.+  Ana a Gomeri anali Asikenazi,+ Rifati ndi Togarima.+  Ana a Yavani anali Elisha,+ Tarisi,+ Kitimu+ ndi Dodanimu.  Mwa anthu amenewa, munachokera anthu okhala mʼzilumba amene anafalikira mʼzilumbazo malinga ndi zilankhulo zawo, mabanja awo ndi mitundu yawo.  Ana a Hamu anali Kusi, Miziraimu,+ Puti+ ndi Kanani.+  Ana a Kusi anali Seba,+ Havila, Sabita, Raama+ ndi Sabiteka. Ana a Raama anali Sheba ndi Dedani.  Kusi anabereka Nimurodi, amene anali woyamba kukhala wamphamvu padziko lapansi.  Iye anakhala mlenje wamphamvu wotsutsa Yehova. Nʼchifukwa chake pali mawu akuti: “Monga Nimurodi mlenje wamphamvu wotsutsa Yehova.” 10  Ufumu wake unayambira ku* Babele,+ Ereke,+ Akadi mpaka ku Kaline mʼdziko la Sinara.+ 11  Atachoka mʼdzikolo analowera ku Asuri+ ndipo anamangako Nineve,+ Rehoboti-iri, Kala, 12  komanso Resene pakati pa Nineve ndi Kala. Umenewu ndi mzinda waukulu.* 13  Miziraimu anabereka Ludimu,+ Anamimu, Lehabimu, Nafituhimu,+ 14  Patirusimu,+ Kasiluhimu (Afilisiti+ anachokera mwa iyeyu) ndiponso Kafitorimu.+ 15  Kanani anabereka Sidoni,+ mwana wake woyamba, kenako anabereka Heti.+ 16  Analinso kholo la Ayebusi,+ Aamori,+ Agirigasi, 17  Ahivi,+ Aariki, Asini, 18  Aarivadi,+ Azemari ndi Ahamati,+ ndipo pambuyo pake, mabanja a Akanani anabalalikana. 19  Choncho malire a dziko la Akanani anachokera ku Sidoni mpaka ku Gerari+ kufupi ndi Gaza,+ nʼkukafika ku Sodomu ndi Gomora+ mpakanso ku Adima ndi Zeboyimu,+ kufupi ndi Lasa. 20  Amenewa ndi omwe anali ana a Hamu malinga ndi mabanja awo ndi zilankhulo zawo, mayiko awo komanso mitundu yawo. 21  Nayenso Semu anabereka ana ndipo anakhala kholo la ana onse a Ebere.+ Semu anali mngʼono wake wa Yafeti, amene anali wamkulu pa onse.* 22  Ana a Semu anali Elamu,+ Ashuri,+ Aripakisadi,+ Ludi ndi Aramu.+ 23  Ana a Aramu anali Uzi, Huli, Geteri ndi Masi. 24  Aripakisadi anabereka Shela+ ndipo Shela anabereka Ebere. 25  Ebere anabereka ana awiri. Wina dzina lake anali Pelegi,*+ chifukwa mʼmasiku ake dziko lapansi linagawanika.* Mʼbale wakeyo dzina lake anali Yokitani.+ 26  Yokitani anabereka Alamodadi, Selefi, Hazaramaveti, Yera,+ 27  Hadoramu, Uzali, Dikila, 28  Obali, Abimaele, Sheba, 29  Ofiri,+ Havila ndi Yobabi. Onsewa anali ana a Yokitani. 30  Dziko limene ankakhala linayambira ku Mesa mpaka ku Sefara, dera lamapiri la Kumʼmawa. 31  Amenewa ndi ana a Semu malinga ndi mabanja awo ndi zilankhulo zawo komanso malinga ndi mayiko awo ndi mitundu yawo.+ 32  Mabanja a ana a Nowa ndi amenewa malinga ndi mibadwo yawo komanso mitundu yawo. Kuchokera mwa anthu amenewa, mitundu inafalikira padziko lapansi pambuyo pa Chigumula.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Mizinda yoyambirira ya ufumu wake inali.”
Zikuoneka kuti mizinda ya Nineve, Rehoboti-iri, Kala komanso Resene, yonse pamodzi ankaiona kuti ndi mzinda umodzi waukulu.
Mawu a Chiheberi amasonyeza kuti nʼkutheka kuti Semu ndi amene anali wamkulu kwa Yafeti.
Dzina lakuti “Pelegi” limatanthauza “Kugawika.”
Kapena kuti, “anthu okhala padziko lapansi anagawanika.”