Genesis 11:1-32

  • Nsanja ya Babele (1-4)

  • Yehova anasokoneza chilankhulo (5-9)

  • Kuchokera pa Semu kudzafika pa Abulamu (10-32)

    • Banja la Tera (27)

    • Abulamu anachoka ku Uri (31)

11  Tsopano dziko lonse lapansi linali ndi chilankhulo chimodzi ndipo anthu ankagwiritsa ntchito mawu ofanana. 2  Pamene anthuwo ankalowera chakumʼmawa, anapeza chigwa mʼdera la Sinara+ ndipo anayamba kukhala kumeneko. 3  Kenako anauzana kuti: “Tiyeni tiumbe njerwa tiziotche.” Atatero, anayamba kumanga ndi njerwa mʼmalo mwa miyala, nʼkumagwiritsa ntchito phula ngati matope omangira. 4  Ndiyeno anati: “Tiyeni timange mzinda wathuwathu, ndipo nsanja yake ikafike mʼmwamba mwenimweni. Tikatero tidzipangira dzina loti titchuke nalo, ndipo sitimwazikana padziko lonse lapansi.”+ 5  Kenako Yehova anapita kukaona mzinda ndi nsanja imene ana a anthu anamanga. 6  Ndiyeno Yehova anati: “Taonani! Izi nʼzimene anthuwa ayamba kuchita, popeza ndi amodzi ndipo onse ali ndi chilankhulo chimodzi.+ Mmene zililimu, angathe kuchita chilichonse chimene akuganiza. 7  Tiyeni+ tipite komweko nʼkukasokoneza chilankhulo chawo* kuti asamamvane polankhula.” 8  Choncho Yehova anawabalalitsa pamalopo moti anafalikira padziko lonse lapansi.+ Pangʼono ndi pangʼono iwo anasiya kumanga mzindawo. 9  Mzindawo unatchedwa Babele,*+ chifukwa kumeneko Yehova anasokoneza chilankhulo cha anthu onse, ndipo Yehova anabalalitsira anthuwo padziko lonse lapansi. 10  Iyi ndi mbiri ya Semu.+ Semu anali ndi zaka 100 pamene anabereka Aripakisadi,+ patatha zaka ziwiri chigumula chitachitika. 11  Atabereka Aripakisadi, Semu anakhalabe ndi moyo zaka zina 500. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi.+ 12  Aripakisadi ali ndi zaka 35, anabereka Shela.+ 13  Atabereka Shela, Aripakisadi anakhalabe ndi moyo zaka zina 403. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi. 14  Shela ali ndi zaka 30, anabereka Ebere.+ 15  Atabereka Ebere, Shela anakhalabe ndi moyo zaka zina 403. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi. 16  Ebere ali ndi zaka 34, anabereka Pelegi.+ 17  Atabereka Pelegi, Ebere anakhalabe ndi moyo zaka zina 430. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi. 18  Pelegi ali ndi zaka 30, anabereka Reu.+ 19  Atabereka Reu, Pelegi anakhalabe ndi moyo zaka zina 209. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi. 20  Reu ali ndi zaka 32, anabereka Serugi. 21  Atabereka Serugi, Reu anakhalabe ndi moyo zaka zina 207. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi. 22  Serugi ali ndi zaka 30, anabereka Nahori. 23  Atabereka Nahori, Serugi anakhalabe ndi moyo zaka zina 200. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi. 24  Nahori ali ndi zaka 29, anabereka Tera.+ 25  Atabereka Tera, Nahori anakhalabe ndi moyo zaka zina 119. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi. 26  Tera anakhala ndi moyo zaka 70, kenako anabereka Abulamu,+ Nahori+ ndi Harana. 27  Mbiri ya Tera ndi iyi. Tera anabereka Abulamu, Nahori ndi Harana. Harana anabereka Loti.+ 28  Pambuyo pake, Harana anamwalira mumzinda wa Uri+ womwe ndi wa Akasidi,+ kumene anabadwira. Anamwalira bambo ake Tera ali ndi moyo. 29  Abulamu ndi Nahori anakwatira. Mkazi wa Abulamu anali Sarai,+ pamene mkazi wa Nahori anali Milika,+ mwana wa Harana. Harana analinso bambo ake a Yisika. 30  Koma Sarai anali wosabereka,+ ndipo analibe mwana. 31  Kenako Tera anatenga mwana wake Abulamu, mdzukulu+ wake Loti mwana wa Harana ndi Sarai mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abulamu, nʼkuchoka mumzinda wa Uri womwe ndi wa Akasidi kupita kudziko la Kanani.+ Patapita nthawi anafika ku Harana+ ndipo anayamba kukhala kumeneko. 32  Choncho Tera anakhala ndi moyo zaka 205. Kenako anamwalira ku Harana.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Tiyeni titsikire kumeneko ndi kukasokoneza chilankhulo chawo.”
Kutanthauza kuti, “Chisokonezo.”