Genesis 12:1-20

  • Abulamu anachoka ku Harana kupita ku Kanani (1-9)

    • Lonjezo la Mulungu kwa Abulamu (7)

  • Abulamu ndi Sarai ku Iguputo (10-20)

12  Yehova anauza Abulamu kuti: “Samuka mʼdziko lako ndi kuchoka pakati pa abale ako ndipo usiye nyumba ya bambo ako. Upite kudziko limene ndidzakuonetse.+  Ndidzakupangitsa kuti ukhale mtundu waukulu. Ndidzakudalitsa ndipo ndidzapangitsa kuti dzina lako litchuke. Komanso anthu ena adzadalitsidwa chifukwa cha iwe.+  Odalitsa iwe ndidzawadalitsa, ndipo wotemberera iwe ndidzamutemberera.+ Mabanja onse apadziko lapansi adzadalitsidwa* kudzera mwa iwe.”+  Choncho Abulamu ananyamuka monga mmene Yehova anamuuzira, ndipo Loti ananyamuka naye limodzi. Pamene ankachoka ku Harana, Abulamu anali ndi zaka 75.+  Abulamu anatenga mkazi wake Sarai,+ Loti mwana wa mʼbale+ wake ndi chuma chawo chonse+ komanso akapolo awo onse amene anapeza kudziko la Harana. Iwo ananyamuka ulendo wopita kudziko la Kanani.+ Atafika ku Kanani,  Abulamu anadutsa mʼdzikolo mpaka kukafika ku Sekemu,+ pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya ku More.+ Pa nthawiyo nʼkuti Akanani akukhala mʼdzikomo.  Ndiyeno Yehova anaonekera kwa Abulamu nʼkumuuza kuti: “Ndidzapereka dziko ili+ kwa mbadwa* zako.”+ Choncho Abulamu anamanga guwa lansembe pamalo amene Yehova anaonekera kwa iye.  Patapita nthawi, anasamuka pamalopo nʼkupita kudera lamapiri, kumʼmawa kwa Beteli.+ Kumeneko iye anamanga tenti yake. Beteli anali kumadzulo kwake ndipo Ai+ anali kumʼmawa kwake. Kenako anamangira Yehova guwa lansembe+ nʼkuyamba kuitana pa dzina la Yehova.+  Pambuyo pake Abulamu anasamutsa tenti yake kumeneko. Kuyambira pa nthawi imeneyi, iye ankangokhalira kumanga ndi kusamutsa msasa, kulowera ku Negebu.+ 10  Tsopano mʼdzikolo munali njala, ndipo Abulamu ananyamuka kupita ku Iguputo kukakhala kumeneko kwa kanthawi,*+ chifukwa njalayo inafika poipa kwambiri mʼdzikolo.+ 11  Atatsala pangʼono kulowa mʼdziko la Iguputo anauza mkazi wake Sarai kuti: “Ndikudziwa kuti ndiwe mkazi wokongola.+ 12  Choncho Aiguputo akakuona, mosakayikira anena kuti, ‘Ameneyu ndi mkazi wake.’ Ndipo andipha koma iweyo akusiya wamoyo. 13  Ndiye chonde, unene kuti ndiwe mchemwali wanga kuti zindiyendere bwino. Ukatero upulumutsa moyo wanga.”+ 14  Choncho Abulamu atangolowa mu Iguputo, Aiguputo anaonadi kuti mkaziyo ndi wokongola kwambiri. 15  Nawonso akalonga a Farao anamuona ndipo anakauza Farao kuti mkaziyo ndi wokongola. Choncho mkaziyo anatengedwa nʼkupita naye kunyumba kwa Farao. 16  Farao anamusamalira bwino Abulamu chifukwa cha mkazi wake, moti anamupatsa nkhosa, ngʼombe, abulu aamuna ndi aakazi, antchito aamuna ndi aakazi komanso ngamila.+ 17  Ndiyeno Yehova anagwetsera Farao ndi onse amʼbanja lake miliri yoopsa chifukwa cha Sarai, mkazi wa Abulamu.+ 18  Choncho Farao ataona zimenezi anaitana Abulamu nʼkumufunsa kuti: “Nʼchiyani wachitachi? Nʼchifukwa chiyani sunandiuze kuti ndi mkazi wako? 19  Nʼchifukwa chiyani unanena kuti, ‘Ndi mchemwali wanga,’+ moti ndinatsala pangʼono kumutenga kukhala mkazi wanga? Eko mkazi wako. Mutenge uzipita!” 20  Choncho Farao analamula anyamata ake kuti aperekeze Abulamu ndi mkazi wake, limodzi ndi zonse zimene anali nazo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “adzapeza madalitso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Kapena kuti, “kukakhala kumeneko ngati mlendo.”