Genesis 13:1-18

  • Abulamu anabwerera ku Kanani (1-4)

  • Abulamu anasiyana ndi Loti (5-13)

  • Mulungu anabwereza lonjezo lake kwa Abulamu (14-18)

13  Choncho Abulamu anachoka ku Iguputo nʼkulowera ku Negebu.+ Iye anachoka limodzi ndi mkazi wake ndi zonse zimene anali nazo komanso Loti.  Abulamu anali ndi chuma chambiri. Anali ndi ziweto, siliva ndi golide.+  Abulamu atachoka ku Negebu, ankamanga misasa malo osiyanasiyana nʼkumasamuka mpaka anakafika ku Beteli, kumene kunali tenti yake poyamba, pakati pa Beteli ndi Ai.+  Kumeneko nʼkumene anamangako guwa lansembe poyamba paja. Atafika kumeneko Abulamu anaitanira pa dzina la Yehova.  Nayenso Loti, amene ankayenda limodzi ndi Abulamu, anali ndi nkhosa, ngʼombe komanso matenti.  Chifukwa choti katundu wawo anachuluka kwambiri, malo anawachepera moti sakanathanso kukhala limodzi.  Zimenezi zinapangitsa kuti pabuke mkangano pakati pa abusa a Abulamu ndi abusa a Loti. (Pa nthawiyo nʼkuti Akanani ndi Aperezi akukhala mʼdzikomo.)+  Choncho Abulamu anauza Loti+ kuti: “Chonde, pasakhale mkangano uliwonse pakati pa ine ndi iwe, komanso pakati pa abusa anga ndi abusa ako, pajatu ndife pachibale.  Tiye tisiyane. Ukhoza kusankha mbali iliyonse ya dzikoli. Iwe ukapita kumanzere, ine ndipita kumanja, koma ukapita kumanja, ine ndipita kumanzere.” 10  Choncho Loti anakweza maso ake nʼkuona chigawo chonse cha Yorodano+ mpaka kukafika ku Zowari,+ ndipo anaona kuti chinali ndi madzi ambiri. (Pa nthawiyi nʼkuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora.) Chinali ngati munda wa Yehova+ komanso ngati dziko la Iguputo. 11  Kenako Loti anasankha chigawo chonse cha Yorodano, ndipo anasamutsira msasa wake kumʼmawa. Choncho iwo anasiyana. 12  Abulamu anapitiriza kukhala mʼdziko la Kanani, koma Loti anakakhala pakati pa mizinda yamʼchigawocho.+ Kenako anakamanga tenti yake pafupi ndi Sodomu. 13  Koma anthu a ku Sodomu anali oipa ndiponso ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova.+ 14  Abulamu atasiyana ndi Loti, Yehova anamuuza kuti: “Takweza maso ako kuchokera pamene ulipo. Uyangʼane kumpoto ndi kumʼmwera, komanso kumʼmawa ndi kumadzulo. 15  Dziko lonse limene ukulionali, ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbadwa zako,* kuti likhale lanu mpaka kalekale.+ 16  Ndidzachulukitsa mbadwa zako* ngati mchenga wapadziko lapansi. Choncho ngati munthu angathe kuwerenga mchengawo, ndiye kuti mbadwa zako* zidzatha kuwerengedwa.+ 17  Nyamuka, uyendere dziko lonselo, mʼlitali ndi mʼlifupi mwake, chifukwa ndidzalipereka kwa iwe.” 18  Choncho Abulamu anapitiriza kukhala mʼmatenti. Patapita nthawi, anakakhala pakati pa mitengo ikuluikulu ya ku Mamure,+ ku Heburoni.+ Kumeneko, anamangira Yehova guwa lansembe.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zako.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zako.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zako.”