Genesis 21:1-34

  • Kubadwa kwa Isaki (1-7)

  • Isimaeli ankaseka Isaki (8, 9)

  • Hagara ndi Isimaeli anathamangitsidwa (10-21)

  • Pangano la Abulahamu ndi Abimeleki (22-34)

21  Yehova anakumbukira Sara monga mmene ananenera, ndipo Yehova anachitira Sara mogwirizana ndi zimene analonjeza.+  Choncho Sara anakhala woyembekezera+ ndipo anaberekera Abulahamu mwana, Abulahamuyo atakalamba. Izi zinachitika ndendende pa nthawi imene Mulungu analonjeza Abulahamu.+  Abulahamu anapatsa mwana amene Sara anamuberekerayo dzina lakuti Isaki.+  Isaki atakwanitsa masiku 8, Abulahamu anachita mdulidwe wa mwana wakeyo, monga mmene Mulungu anamulamulira.+  Abulahamu anali ndi zaka 100 pamene mwana wake Isaki anabadwa.  Ndiyeno Sara anati: “Mulungu wandipatsa chifukwa chosangalalira. Tsopano aliyense akamva zimenezi asangalala nane limodzi.”*  Anapitiriza kunena kuti: “Ndi ndani akanauza Abulahamu kuti, ‘Sara adzayamwitsa mwanaʼ? Koma taonani, ndamuberekera mwana Abulahamu atakalamba.”  Ndiyeno mwanayo atakula anamusiyitsa kuyamwa. Pa tsiku limene Isaki anamusiyitsa kuyamwalo, Abulahamu anakonza phwando lalikulu.  Koma Sara ankaona mwana amene Hagara+ wa ku Iguputo anaberekera Abulahamu akuseka Isaki.+ 10  Choncho Sara anauza Abulahamu kuti: “Thamangitsani kapolo wamkaziyu pamodzi ndi mwana wakeyu pano, chifukwa mwana wa kapolo ameneyu sadzakhala wolandira cholowa pamodzi ndi mwana wanga Isaki.”+ 11  Koma zimene Sara ananenazi zokhudza Isimaeli, zinamuipira kwambiri Abulahamu.+ 12  Kenako Mulungu anauza Abulahamu kuti: “Usaipidwe ndi zimene Sara akukuuza zokhudza mnyamatayo ndiponso kapolo wakoyo. Mumvere,* chifukwa mbadwa* zimene ndinakulonjeza zidzachokera mwa Isaki.+ 13  Kunena za mwana wa kapoloyu,+ nayenso ndidzamupangitsa kukhala mtundu,+ chifukwa iyenso ndi mwana wako.” 14  Ndiyeno Abulahamu anadzuka mʼmawa kwambiri nʼkutenga mkate ndi thumba lachikopa la madzi, ndipo anaziika paphewa pa Hagara. Atatero anamuuza kuti azipita limodzi ndi mwana wakeyo.+ Choncho Hagarayo ananyamuka nʼkumangoyendayenda mʼchipululu cha Beere-seba.+ 15  Potsirizira pake, madzi anamuthera mʼthumba lachikopa lija, ndipo iye anangomusiya mnyamata uja pachitsamba. 16  Ndiyeno iye anapita chapatali nʼkukakhala pansi payekhayekha pamtunda woti muvi woponya ndi uta ukhoza kufika. Anachita zimenezi chifukwa mumtima mwake anati: “Sindikufuna kuona mwana wanga akufa.” Choncho anakakhala pansi chapatali nʼkuyamba kulira mokweza. 17  Kenako Mulungu anamva mawu a mnyamatayo,+ ndipo mngelo wa Mulungu analankhula ndi Hagara kuchokera kumwamba kuti:+ “Kodi watani Hagara? Usaope, Mulungu wamva mawu a mnyamatayo pomwe wagonapo. 18  Nyamuka! Dzutsa mnyamatayo, ndipo umugwire kuti azitha kuyenda chifukwa ndidzamupangitsa kukhala mtundu waukulu.”+ 19  Ndiyeno Mulungu anamutsegula maso Hagara, moti anaona chitsime cha madzi. Choncho anapita pachitsimecho nʼkutungira madziwo mʼthumba lachikopa lija, kenako anapatsa mnyamatayo kuti amwe. 20  Pamene Isimaeli+ ankakula, Mulungu anakhalabe naye. Mnyamata ameneyu ankakhala mʼchipululu ndipo anakhala katswiri woponya muvi pogwiritsa ntchito uta. 21  Iye anayamba kukhala mʼchipululu cha Parana,+ ndipo amayi ake anakamutengera mkazi kudziko la Iguputo. 22  Pa nthawi imeneyo, Abimeleki limodzi ndi Fikolo mkulu wa gulu lake lankhondo, anauza Abulahamu kuti: “Mulungu ali ndi iwe pa zonse zomwe ukuchita.+ 23  Choncho panopa lumbira pamaso pa Mulungu kuti udzakhala wokhulupirika kwa ine, kwa ana anga ndi kwa mbadwa zanga. Ndiponso kuti udzasonyeza chikondi chokhulupirika ngati chimene ine ndakusonyeza. Lumbira kuti udzasonyeza chikondi chimenechi kwa ineyo ndi anthu amʼdziko limene ukukhala.”+ 24  Abulahamu anayankha kuti: “Ndikulumbira.” 25  Koma Abulahamu anadandaulira Abimeleki za chitsime cha madzi chimene antchito a Abimeleki analanda mwachiwawa.+ 26  Abimeleki anayankha kuti: “Sindikudziwa amene anachita zimenezi, ndipo ngakhale iwe sunandiuze za nkhaniyi. Inetu sindinamve za nkhani imeneyi, moti ndikuimvera pompano.” 27  Ndiye Abulahamu anatenga nkhosa ndi ngʼombe nʼkuzipereka kwa Abimeleki. Ndipo awiriwo anachita pangano. 28  Kenako Abulahamu anapatula ana a nkhosa aakazi 7 pa gululo nʼkuwaika paokha. 29  Ndiyeno Abimeleki anafunsa Abulahamu kuti: “Nʼchifukwa chiyani ana a nkhosa aakazi 7 amenewa wawaika paokha?” 30  Poyankha Abulahamu anati: “Mulandire ana a nkhosa aakazi 7 amene ndikukupatsaniwa, kuti akhale umboni wakuti ndinakumba chitsimechi ndine.” 31  Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Beere-seba,*+ chifukwa chakuti onse awiri analumbira pamalopo. 32  Choncho iwo anachita pangano+ pa Beere-sebapo, kenako Abimeleki limodzi ndi Fikolo mkulu wa asilikali ake, anabwerera kudziko la Afilisiti.+ 33  Zitatero, Abulahamu anadzala mtengo wa bwemba pa Beere-seba, ndipo kumeneko anaitanira pa dzina la Yehova,+ Mulungu yemwe adzakhalepo mpaka kalekale.+ 34  Ndipo Abulahamu anakhala* mʼdziko la Afilisiti kwa nthawi yaitali.*+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “aseka limodzi ndi ine.” Mabaibulo ena amati, “andiseka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mvera mawu ake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Nʼkutheka kuti dzinali limatanthauza “Chitsime cha Lumbiro” kapena “Chitsime cha 7.”
Kapena kuti, “anakhala monga mlendo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku ambiri.”