Genesis 25:1-34

  • Abulahamu anakwatiranso (1-6)

  • Imfa ya Abulahamu (7-11)

  • Ana a Isimaeli (12-18)

  • Kubadwa kwa Yakobo ndi Esau (19-26)

  • Esau anagulitsa ukulu wake (27-34)

25  Tsopano Abulahamu anatenganso mkazi wina, dzina lake Ketura.  Patapita nthawi, mkaziyo anamuberekera Zimirani, Yokesani, Medani, Midiyani,+ Isibaki ndi Shuwa.+  Yokesani anabereka Sheba ndi Dedani. Ana a Dedani anali Asurimu, Letusimu ndi Leumimu.  Ana a Midiyani anali Efa, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida. Onsewa anali ana aamuna a Ketura.  Pambuyo pake, Abulahamu anapatsa Isaki zonse zimene anali nazo.+  Koma Abulahamu anapereka mphatso kwa ana amene adzakazi ake anamuberekera. Kenako, iye adakali ndi moyo, anatumiza anawo Kumʼmawa, kutali ndi mwana wake Isaki.+  Abulahamu anakhala ndi moyo zaka 175.  Kenako Abulahamu anamwalira ali wokalamba, atakhala ndi moyo wabwino, wautali komanso atakhutira ndi moyo wake ndipo anaikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ake.*  Ana ake, Isaki ndi Isimaeli, anamuika mʼmanda, mʼphanga la Makipela, pamalo a Efuroni mwana wa Zohari Mheti, pafupi ndi Mamure.+ 10  Malo amenewa ndi omwe Abulahamu anagula kwa ana a Heti. Abulahamu anaikidwa kumeneko ndipo nʼkomwenso Sara mkazi wake anaikidwa.+ 11  Abulahamu atamwalira, Mulungu anapitiriza kudalitsa Isaki+ mwana wake. Isakiyo ankakhala pafupi ndi Beere-lahai-roi.+ 12  Iyi ndi mbiri ya Isimaeli+ mwana wa Abulahamu, amene Hagara+ wa ku Iguputo, kapolo wa Sara anaberekera Abulahamu. 13  Mayina a ana a Isimaeli, malinga ndi mabanja awo ndi awa: Nebayoti,+ mwana woyamba wa Isimaeli, Kedara,+ Adibeele, Mibisamu,+ 14  Misima, Duma, Maasa, 15  Hadadi, Tema, Yeturi, Nafisi ndi Kedema. 16  Amenewa ndi ana a Isimaeli, mayina awo ndi amenewa potengera midzi yawo komanso misasa yawo.* Anali atsogoleri okwanira 12 malinga ndi mafuko awo.+ 17  Isimaeli anakhala ndi moyo zaka 137. Kenako anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ake. 18  Mbadwa zake zinayamba kukhala ku Havila+ pafupi ndi Shura+ moyandikana ndi Iguputo, mpaka ku Asuri. Iwo anakhala pafupi ndi abale awo onse.*+ 19  Mbiri ya Isaki mwana wa Abulahamu+ ndi iyi. Abulahamu anabereka Isaki. 20  Isaki anali ndi zaka 40 pamene anakwatira Rabeka, mwana wa Betuele+ wa Chiaramu, wa ku Padani-aramu, amene anali mchemwali wake wa Labani wa Chiaramu. 21  Isaki ankachonderera Yehova mosalekeza zokhudza mkazi wake, chifukwa anali wosabereka. Choncho Yehova anamva pemphero lake, ndipo Rabeka mkazi wakeyo anakhala woyembekezera. 22  Ndiyeno ana amene anali mʼmimba mwake anayamba kulimbana,+ moti iye anati: “Ngati umu ndi mmene ndivutikire, kuli bwino ndingofa.” Choncho anafunsa Yehova kuti adziwe chifukwa chake. 23  Yehova anamuyankha kuti: “Mʼmimba mwako muli mitundu iwiri ya anthu+ ndipo mitundu iwiri imene idzatuluke mʼmimba mwako idzakhala kosiyana.+ Mtundu wina udzakhala wamphamvu kuposa mtundu winawo,+ ndipo wamkulu adzatumikira wamngʼono.”+ 24  Nthawi yoti Rabeka abereke inakwana, ndipo mʼmimba mwake munali ana amapasa. 25  Woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati wavala chovala chaubweya.+ Choncho anamupatsa dzina lakuti Esau.*+ 26  Pambuyo pake, mʼbale wake anabadwa, ndipo dzanja lake linali litagwira chidendene cha Esau.+ Choncho Isaki anapatsa mwanayo dzina lakuti Yakobo.*+ Pamene Rabeka ankabereka anawa nʼkuti Isaki ali ndi zaka 60. 27  Anyamatawa atakula, Esau anakhala mlenje waluso,+ munthu wokonda kuyenda mʼtchire. Koma Yakobo ankakonda kukhala mʼmatenti+ ndipo anali munthu wosalakwa. 28  Isaki ankakonda kwambiri Esau chifukwa ankamuphera nyama, koma Rabeka ankakonda kwambiri Yakobo.+ 29  Tsiku lina Yakobo akuphika mphodza, Esau anafika kuchokera kutchire, ndipo anali atatopa. 30  Ndiyeno Esau anapempha Yakobo kuti: “Chonde, fulumira ndigawireko pangʼono mphodza zofiira zimene ukuphikazo,* ndatopatu ine!”* Nʼchifukwa chake anamupatsa dzina lakuti Edomu.*+ 31  Poyankha Yakobo ananena kuti: “Choyamba, undigulitse ukulu wako monga woyamba kubadwa.”+ 32  Ndiye Esau anati: “Ine pano ndikufuna kufa ndi njala, ndiye ukuluwo uli ndi ntchito yanji kwa ine?” 33  Ndiyeno Yakobo anati: “Uyambe kaye walumbira!” Ndipo iye analumbiradi kwa Yakobo nʼkumugulitsa ukulu wake monga woyamba kubadwa.+ 34  Atatero Yakobo anapatsa Esau mkate ndi mphodza, ndipo iye anadya nʼkumwa. Kenako, ananyamuka nʼkumapita. Umu ndi mmene Esau anasonyezera kuti ankaona kuti ukulu wake unali wopanda phindu.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo anagona limodzi ndi makolo ake.”
Kapena kuti, “misasa yawo yokhala ndi mpanda.”
Mabaibulo ena amati, “Ankachitira nkhanza abale awo onse.”
Kutanthauza kuti, “Wacheya.”
Kutanthauza kuti, “Wogwira Chidendene; Wochenjerera Ena.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chofiiracho, icho chofiiracho.”
Kapena kuti, “ndili ndi njalatu ine.”
Kutanthauza, “Wofiira.”