Genesis 29:1-35

  • Yakobo anakumana ndi Rakele (1-14)

  • Yakobo anakonda Rakele (15-20)

  • Yakobo anakwatira Leya ndi Rakele (21-29)

  • Ana 4 aamuna a Yakobo amene Leya anamuberekera: Rubeni, Simiyoni, Levi ndi Yuda (30-35)

29  Kenako Yakobo anapitiriza ulendo wake wopita kudziko la anthu a Kumʼmawa.  Atafika pamalo enaake anaona chitsime, ndipo panali magulu atatu a nkhosa zitagona pansi, chifukwa mʼpamene anthu ankakonda kumwetserapo ziweto. Pachitsimepo panali potseka ndi mwala waukulu.  Nkhosa zonse zikafika pamalopo, abusa ankagubuduza mwala kuuchotsa pachitsimepo nʼkutunga madzi kuti nkhosazo zimwe. Akamaliza, ankabwezeretsa mwalawo pachitsimepo.  Ndiyeno Yakobo anawafunsa kuti: “Abale anga, kodi mwachokera kuti?” Iwo anayankha kuti: “Tachokera ku Harana.”+  Anawafunsanso kuti: “Kodi Labani+ mdzukulu wa Nahori+ mumamudziwa?” Iwo anati: “Eya timamudziwa.”  Kenako anawafunsa kuti: “Kodi ali bwino?” Iwo anayankha kuti: “Ali bwino. Komanso mwana wake Rakele,+ ndi uyo akubwera ndi nkhosa apoyo.”  Kenako Yakobo anawauza kuti: “Inotu si nthawi yosonkhanitsa ziweto, ndi masanatu ano. Zimwetseni madzi, kenako mupite nazo kubusa.”  Iwo anayankha kuti: “Sitiloledwa kuchita zimenezo mpaka magulu onse a nkhosa atafika. Zikatero timachotsa mwala wa pachitsimewu nʼkumwetsa nkhosa zathu.”  Akulankhula nawo choncho, Rakele anafika ndi nkhosa za bambo ake, chifukwa anali mʼbusa wamkazi. 10  Yakobo ataona Rakele mwana wa Labani, mchimwene wa mayi ake, ndiponso nkhosa za Labaniyo, nthawi yomweyo anapita pachitsime paja nʼkugubuduza mwalawo kuuchotsa pachitsimepo. Atatero anatungira madzi nkhosa za Labani, mchimwene wa mayi ake. 11  Ndiyeno Yakobo anakisa* Rakele, nʼkulira mofuula uku akugwetsa misozi. 12  Kenako anayamba kuuza Rakele kuti iye ndi wachibale wa bambo ake, ndiponso kuti ndi mwana wa Rabeka. Atamva zimenezi, Rakele anathamanga kukauza bambo ake. 13  Labani+ atangomva za Yakobo, mwana wa mchemwali wake, anathamanga kukakumana naye. Atafika, anamʼkumbatira ndi kumukisa nʼkupita naye kunyumba kwake. Ndipo Yakobo anafotokozera Labani zonse zimene zinamuchitikira. 14  Ndiyeno Labani anamuuza kuti: “Iwe ndiwedi mʼbale wanga weniweni.”* Choncho anakhala naye mwezi wathunthu. 15  Kenako Labani anafunsa Yakobo kuti: “Kodi ukufuna undigwirire ntchito yaulere chifukwa chakuti ndiwe wachibale wanga?+ Ndiuze, kodi ndidzakulipire chiyani?”+ 16  Labani anali ndi ana aakazi awiri, wamkulu dzina lake anali Leya, wamngʼono anali Rakele.+ 17  Leya anali ndi maso osaoneka bwino, pamene Rakele anali mtsikana wooneka bwino komanso wokongola kwambiri. 18  Koma Yakobo anakonda Rakele, ndiye anati: “Ndine wokonzeka kukugwirirani ntchito zaka 7, kuti mudzandipatse Rakele mwana wanu wamngʼonoyu.”+ 19  Labani anati: “Ndi bwino kuti Rakeleyu ndikupatse iweyo, kusiyana nʼkuti ndimupereke kwa munthu wina. Upitirize kukhala ndi ine.” 20  Yakobo anagwira ntchito zaka 7 kuti atenge Rakele.+ Koma zakazo anangoziona ngati masiku ochepa chabe, chifukwa anamʼkonda kwambiri mtsikanayo. 21  Kenako Yakobo anauza Labani kuti: “Ndipatseni mkazi wanga, chifukwa masiku anga akwana, kuti ndimukwatire.”* 22  Atatero Labani anasonkhanitsa anthu onse akumeneko nʼkuchita phwando. 23  Koma kutada, Labani anaganiza zotenga Leya mwana wake nʼkupita naye kwa Yakobo, kuti akagone naye. 24  Labani anaperekanso Zilipa kapolo wake kwa mwana wake Leya, kuti akhale kapolo wake.+ 25  Kutacha mʼmawa, Yakobo anadabwa kuona kuti ali ndi Leya. Ataona zimenezi anafunsa Labani kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwandichitira zimenezi? Ine ndakugwirirani ntchito kuti mundipatse Rakele. Nanga nʼchifukwa chiyani mwandipusitsa chonchi?”+ 26  Labani anayankha kuti: “Mogwirizana ndi mwambo wathu, nʼzosaloleka kukwatitsa wamngʼono mkulu wake asanakwatiwe. 27  Usangalale ndi mkaziyu mlungu wonse wokondwerera ukwati wake. Kenako ndidzakupatsa mkazi winayu, komabe udzandigwirira ntchito zaka zina 7.”+ 28  Choncho Yakobo anasangalaladi ndi Leya mlungu wonse wokondwerera ukwati wake. Kenako Labani anamupatsa mwana wake Rakele kuti akhale mkazi wake. 29  Labani anaperekanso kapolo wake Biliha+ kwa mwana wake Rakele kuti akhale kapolo wake.+ 30  Ndiyeno Yakobo anagonanso ndi Rakele ndipo anamʼkonda kwambiri kuposa Leya, moti anagwiriranso ntchito Labani zaka zina 7.+ 31  Yehova ataona kuti Leya sankakondedwa kwenikweni,* anamʼpatsa mphamvu zobereka,*+ koma Rakele anali wosabereka.+ 32  Choncho Leya anakhala woyembekezera ndipo anabereka mwana wamwamuna. Mwanayo anamupatsa dzina lakuti Rubeni,*+ ndipo anati: “Chifukwa Yehova waona kusautsika kwanga,+ ndipo tsopano mwamuna wanga ayamba kundikonda.” 33  Leya anakhalanso woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna, ndipo anati: “Yehova wandipatsa mwana wina chifukwa wamva kudandaula kwanga kuti sindikukondedwa kwenikweni.” Choncho mwanayo anamupatsa dzina lakuti Simiyoni.*+ 34  Anakhalanso woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna, ndipo anati: “Apa tsopano mwamuna wanga andikonda basi, chifukwa ndamuberekera ana aamuna atatu.” Choncho mwanayo anamupatsa dzina lakuti Levi.*+ 35  Anakhalanso woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna, ndipo anati: “Tsopano nditamanda Yehova.” Choncho Leya anamupatsa mwanayo dzina lakuti Yuda.*+ Atabereka mwana ameneyu, anasiya kaye kubereka.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anapsompsona.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “fupa langa ndi mnofu wanga.”
Kapena kuti, “kuti ndigone naye.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ankadedwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anatsegula mimba yake.”
Kutanthauza, “Onani, ndi Mwana Wamwamuna!”
Kutanthauza, “Wandimvera.”
Kutanthauza, “Kuphatikizana; Kulumikizana.”
Kutanthauza, “Kutamandidwa; Wotamandika.”