Genesis 32:1-32

  • Angelo anakumana ndi Yakobo (1, 2)

  • Yakobo anakonzekera kukumana ndi Esau (3-23)

  • Yakobo analimbana ndi mngelo (24-32)

    • Yakobo anasinthidwa dzina kukhala Isiraeli (28)

32  Kenako Yakobo ananyamuka, koma ali mʼnjira angelo a Mulungu anakumana naye.  Yakobo atangowaona anati: “Ilitu ndi gulu la Mulungu!” Choncho malowo anawatchula kuti Mahanaimu.*  Ndiyeno Yakobo anatuma anthu kuti apite kwa mchimwene wake Esau, kudziko la Seiri,+ mʼdera la Edomu.+  Anawauza kuti: “Mbuyanga Esau mukamuuze kuti, ‘Kapolo wanu Yakobo wanena kuti: “Ndakhala ndi Labani* kwa nthawi yaitali.+  Pano ndili ndi ngʼombe, abulu, nkhosa komanso antchito aamuna ndi aakazi.+ Ndatumiza uthengawu kwa inu mbuyanga kuti mundikomere mtima.”’”  Anthuwo atabwerako, anauza Yakobo kuti: “Takumana naye mchimwene wanu Esau, ndipo akubwera limodzi ndi amuna 400 kudzakumana nanu.”+  Atamva zimenezi, Yakobo anachita mantha ndi kuda nkhawa kwambiri.+ Choncho anagawa mʼmagulu awiri anthu amene anali nawo, nkhosa, mbuzi, ngʼombe ndi ngamila.  Kenako anati: “Ngati Esau angaukire gulu limodzi, gulu linalo lingathe kuthawa.”  Atatero, Yakobo anati: “Mulungu wa kholo langa Abulahamu, Mulungu wa bambo anga Isaki, inu Yehova munandiuza kuti, ‘Bwerera kudziko lakwanu kwa abale ako, ndipo ndidzakusamalira.’+ 10  Ine ndine wosayenerera chikondi chokhulupirika komanso kukoma mtima konseku, kumene mwandisonyeza ine mtumiki wanu.+ Ndinawoloka Yorodano ndilibe kanthu, koma ndodo yokha, ndipo pano ndili ndi magulu awiriwa.+ 11  Chonde ndipulumutseni+ mʼdzanja la mchimwene wanga, Esau. Ndikuchita naye mantha kuti akafika, akhoza kundivulaza+ komanso kuvulaza akaziwa limodzi ndi ana awo. 12  Pajatu munanena kuti: ‘Ndithu ndidzakusamalira, ndipo ndidzachulukitsa mbadwa* zako ngati mchenga wakunyanja, womwe ndi wosawerengeka.’”+ 13  Tsiku limenelo Yakobo anagona pamalopo. Kenako anatenga zinthu zina pa chuma chake kuti akapatse mchimwene wake Esau ngati mphatso.+ 14  Anatenga mbuzi zazikazi 200, mbuzi zamphongo 20, nkhosa zazikazi 200, nkhosa zamphongo 20, 15  ngamila zoyamwitsa 30 ndi ana a ngamilazo, ngʼombe zazikazi 40, ngʼombe zamphongo 10, abulu aakazi 20 ndi abulu amphongo 10.+ 16  Kenako anapatsa anyamata ake magulu a ziwetozo, gulu lililonse palokha nʼkuwauza kuti: “Tsogolani muwoloke mtsinje, ndipo muzisiya mpata pakati pa gulu lililonse la ziweto.” 17  Anauzanso mnyamata woyamba kuti: “Ngati mchimwene wanga Esau angakumane nawe nʼkukufunsa kuti, ‘Kodi mbuye wako ndi ndani? Ndipo ukupita kuti? Nanga ziweto zimene uli nazozi nʼzandani?’ 18  Ukayankhe kuti, ‘Mbuyanga ndi Yakobo kapolo wanu. Ziwetozi ndi mphatso imene iye watumiza kwa inu mbuyanga Esau.+ Iyeyo ali mʼmbuyo mwathumu.’” 19  Anauzanso mnyamata wachiwiri ndi wachitatu komanso ena onse amene anawapatsira ziwetozo kuti atsogole nazo, kuti: “Zimene ndanenazi mukauze Esau mukakakumana naye. 20  Mukamuuzenso kuti, ‘Ndiponso kapolo wanu Yakobo ali mʼmbuyo mwathumu.’” Popeza mumtima mwake anati: “Ngati angasangalale ndi mphatso imene ndatumizayi,+ ndiye kuti ndikakumana naye akhoza kundilandira bwino.” 21  Choncho atumiki akewo anatsogola ndi mphatsoyo, koma iye anagona pamsasapo usikuwo. 22  Usiku umenewo, iye anadzuka nʼkutenga akazi ake awiri aja,+ akapolo ake awiri aakazi aja+ ndi ana ake aamuna 11 nʼkuwoloka mtsinje wa Yaboki.+ 23  Atawawolotsa mtsinjewo,* anawolotsanso zonse zimene anali nazo. 24  Pomaliza, Yakobo anatsala yekhayekha. Kenako munthu winawake anayamba kulimbana naye mpaka mʼbandakucha.+ 25  Munthuyo ataona kuti Yakobo sakugonja, anamugwira pamalo amene fupa la ntchafu limalumikizana ndi chiuno ndipo polumikizanapo panaguluka mmene ankalimbana naye.+ 26  Atatero anauza Yakobo kuti: “Ndisiye ndizipita, chifukwa kukucha tsopano.” Koma Yakobo anayankha kuti: “Sindikusiya mpaka utandidalitsa.”+ 27  Ndiyeno munthuyo anamufunsa kuti: “Dzina lako ndi ndani?” Iye anayankha kuti: “Yakobo.” 28  Kenako munthuyo anati: “Dzina lako silikhalanso Yakobo, koma Isiraeli,*+ chifukwa walimbana ndi Mulungu+ komanso anthu, ndipo potsirizira pake wapambana.” 29  Nayenso Yakobo anamuuza kuti: “Iwenso undiuze dzina lako.” Koma iye anati: “Nʼchifukwa chiyani ukufuna kudziwa dzina langa?”+ Atatero, anamudalitsa pamalo amenewo. 30  Choncho Yakobo anatchula malowo dzina lakuti Penieli,*+ chifukwa iye anati, “Ndaonana ndi Mulungu pamasomʼpamaso, komabe ndapulumuka.”+ 31  Dzuwa linali litatuluka pamene Yakobo ankachoka ku Penueli,* koma ankayenda motsimphina.+ 32  Nʼchifukwa chake mpaka pano, ana a Isiraeli sadya mtsempha wa pamalo amene fupa la ntchafu limalumikizana ndi chiuno, chifukwa ndi umene munthu uja anagwira polimbana ndi Yakobo.

Mawu a M'munsi

Kutanthauza, “Magulu Awiri.”
Kapena kuti, “Ndakhala ndi Labani ngati mlendo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Kapena kuti, “chigwacho; khwawalo.”
Kutanthauza, “Wolimbana ndi Mulungu” kapena “Mulungu Walimbana Naye.”
Kutanthauza, “Nkhope ya Mulungu.”
Kapena kuti, “Penieli.”