Genesis 34:1-31

  • Dina anagwiriridwa (1-12)

  • Ana a Yakobo anachita zinthu mwachinyengo (13-31)

34  Dina, mwana wamkazi amene Leya anaberekera Yakobo,+ ankakonda kukacheza ndi* atsikana a mumzindawo.+  Ndiyeno Sekemu mwana wamwamuna wa Hamori Mhivi,+ mmodzi wa atsogoleri amumzindawu ataona mtsikanayu, anamutenga nʼkumugwiririra.  Atatero, anayamba kulakalaka kwambiri Dina mwana wa Yakobo, ndipo anamukonda kwambiri mtsikanayu, moti ankalankhula naye momunyengerera.  Potsirizira pake, Sekemu anauza bambo ake Hamori+ kuti: “Mukanditengere mtsikana ameneyu kuti akhale mkazi wanga.”  Yakobo anamva kuti Sekemu wagwiririra mwana wake Dina. Pa nthawiyo nʼkuti ana ake aamuna ali koweta ziweto zake. Choncho Yakobo sananene kanthu kudikira kuti ana akewo abwere.  Kenako Hamori bambo ake a Sekemu, anapita kwa Yakobo kukakambirana naye.  Koma ana a Yakobo atamva za nkhaniyi, nthawi yomweyo anabwerako koweta ziweto kuja. Nkhaniyi inawapweteketsa mtima kwambiri ndipo anakwiya koopsa, chifukwa Sekemu anachitira Isiraeli chinthu chochititsa manyazi kwambiri pogona ndi mwana wa Yakobo.+ Zimenezi zinali zosayenera kuchitika ngakhale pangʼono.+  Ndiyeno Hamori anawauza kuti: “Mwana wanga Sekemu wamukonda mtsikana wanuyu ndi mtima wonse. Chonde, mupatseni kuti akhale mkazi wake.  Tiyeni tichite mgwirizano kuti tizikwatirana. Muzitipatsa ana anu aakazi, inunso muzitenga ana athu aakazi.+ 10  Muzikhala kwathu kuno ndipo dzikoli likhalanso lanu. Mukhazikike mumzinda uno ndipo muzichita malonda mwaufulu.” 11  Kenako Sekemu anauza bambo ake a Dina ndi alongo ake kuti: “Ndikomereni mtima, ndikupatsani chilichonse chimene mungafune. 12  Kwezani kwambiri ndalama za malowolo ndi mphatso zoti ndipereke.+ Ndine wokonzeka kupereka chilichonse chimene mungandiuze, bola mundipatse mtsikanayu kuti akhale mkazi wanga.” 13  Koma ana a Yakobo anayankha Sekemu ndi bambo ake Hamori mowapusitsa chifukwa Sekemu anali atagwiririra mchemwali wawo Dina. 14  Iwo anawayankha kuti: “Sitingachite zimenezo. Sitingapereke mchemwali wathu kwa mwamuna wosadulidwa.+ Zimenezo nʼzochititsa manyazi kwa ife. 15  Tikulolani pokhapokha ngati mwamuna aliyense atadulidwa+ kuti mukhale ofanana ndi ife. 16  Mukatero tidzakupatsani ana athu aakazi ndipo ifenso tidzatenga ana anu aakazi. Tizidzakhala limodzi ndipo tidzakhala anthu amodzi. 17  Koma ngati simutsatira zimene tanenazi zakuti mudulidwe, mwana wathu wamkaziyo tikamutenga nʼkubwera naye.” 18  Zimene ananenazi zinasangalatsa Hamori+ ndi mwana wake Sekemu.+ 19  Choncho mnyamatayu sanachedwe kuchita zimene anauzidwazo+ chifukwa anamukonda kwambiri mwana wa Yakobo. Sekemu anali wolemekezeka kwambiri mʼnyumba yonse ya bambo ake. 20  Kenako Hamori ndi mwana wake Sekemu anapita pageti la mzinda wawo nʼkuyamba kulankhula ndi amuna amumzindawo+ kuti: 21  “Anthu awa akufuna kuti tizikhala nawo mwamtendere. Ndiye aloleni akhale mʼdzikoli nʼkumachita malonda, popeza dzikoli ndi lalikulu moti atha kukhalamo. Tikhoza kukwatira ana awo aakazi ndiponso tikhoza kuwapatsa ana athu aakazi.+ 22  Koma pakufunika chinthu chimodzi kuti anthuwa alole kuti azikhala nafe nʼkukhala anthu amodzi ndi ife. Akufuna kuti mwamuna aliyense pakati pathu adulidwe ngati mmene iwowo alili.+ 23  Tikatero, kodi katundu wawo, chuma chawo ndi ziweto zawo zonse sizidzakhala zathu? Ndiye tiyeni tilolere zimene akufunazo kuti azikhala nafe.” 24  Choncho anthu onse otuluka pageti la mzindawo anamvera Hamori ndi mwana wake Sekemu, ndipo amuna onse amumzinda wakewo anadulidwa. 25  Koma pa tsiku lachitatu, anthuwo akumvabe ululu, ana awiri a Yakobo, Simiyoni ndi Levi, alongo ake a Dina,+ aliyense anatenga lupanga lake nʼkukalowa mumzindawo anthuwo asakuyembekezera ndipo anapha mwamuna aliyense.+ 26  Anaphanso Hamori ndi mwana wake Sekemu ndi lupanga. Kenako anatenga Dina mʼnyumba ya Sekemu, nʼkumapita. 27  Ana ena a Yakobo anabwera mumzindawo amuna onse ataphedwa, nʼkutenga katundu yense wamumzindamo. Anatero chifukwa anthuwo anagwiririra mchemwali wawo.+ 28  Anatenga nkhosa zawo, abulu awo ndi ziweto zina komanso chilichonse chimene chinali mumzindawo ndi chimene chinali kunja kwa mzindawo. 29  Anatenganso chuma chawo chonse, ana awo onse angʼonoangʼono ndi akazi awo komanso zonse zimene zinali mʼnyumba zawo nʼkumapita. 30  Yakobo ataona zimenezi anauza Simiyoni ndi Levi+ kuti: “Mwandiputira mavuto aakulu, ndipo mwandidanitsa ndi anthu amʼdziko lino, Akanani ndi Aperezi. Ine ndili ndi anthu ochepa. Iwowa ndithu asonkhana nʼkutiukira ndipo atitha tonse, ine ndi banja langa.” 31  Koma anawo anayankha kuti: “Kodi ndi bwino kuti munthu azitenga mchemwali wathu ngati hule?”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kukaona.”