Genesis 35:1-29

  • Yakobo anachotsa milungu yachilendo (1-4)

  • Yakobo anabwerera ku Beteli (5-15)

  • Kubadwa kwa Benjamini; imfa ya Rakele (16-20)

  • Ana 12 a Isiraeli (21-26)

  • Imfa ya Isaki (27-29)

35  Zitatero, Mulungu anauza Yakobo kuti: “Nyamuka, pita ku Beteli+ ukakhale kumeneko. Ukandimangire guwa lansembe. Ndine Mulungu woona, amene anaonekera kwa iwe pamene unkathawa mchimwene wako Esau.”+  Ndiyeno Yakobo anauza anthu a mʼbanja lake ndi onse amene anali naye kuti: “Chotsani milungu yachilendo imene ili pakati panu.+ Dziyeretseni ndipo sinthani zovala zanu.  Mukatero, tinyamuke tipite ku Beteli. Kumeneko ndikamangira guwa lansembe Mulungu woona, amene anandiyankha pa tsiku la kusautsika kwanga, ndipo wakhala nane kulikonse kumene ndapita.”+  Choncho anthuwo anapereka kwa Yakobo milungu yachilendo yonse imene anali nayo, ndi ndolo zimene anavala mʼmakutu. Kenako Yakobo anakwirira* zinthuzo pansi pa mtengo waukulu umene unali pafupi ndi ku Sekemu.  Atanyamuka, Mulungu anachititsa kuti anthu amʼmizinda yowazungulira agwidwe ndi mantha, moti sanatsatire ana a Yakobo kuti amenyane nawo.  Kenako Yakobo anafika ku Luzi,+ komwe ndi ku Beteli, mʼdziko la Kanani. Iye anafika kumeneko limodzi ndi anthu onse amene anali naye.  Anamanga guwa lansembe kumeneko nʼkutchula malowo kuti Eli-beteli.* Malowo anawapatsa dzinali chifukwa Mulungu woona anaonekera kwa iye kumeneko pamene ankathawa mʼbale wake.+  Pambuyo pake Debora,+ mlezi* wa Rabeka anamwalira, ndipo anamuika ku Beteli mʼmunsi mwa phiri, pansi pa mtengo waukulu. Choncho mtengowo anautchula kuti Aloni-bakuti.*  Mulungu anaonekeranso kwa Yakobo pamene ankabwerera kwawo kuchokera ku Padani-aramu, ndipo anamudalitsa. 10  Mulungu anamuuza kuti: “Dzina lako ndi Yakobo.+ Kuyambira lero, dzina lako silikhalanso Yakobo, koma likhala Isiraeli.” Choncho anayamba kumutchula kuti Isiraeli.+ 11  Mulungu anamuuzanso kuti: “Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse.+ Ubereke ndipo ukhale ndi ana ambiri. Mitundu ndi mafuko ambiri adzatuluka mwa iwe,+ ndipo zina mwa mbadwa zako zidzakhala* mafumu.+ 12  Dziko limene ndinalipereka kwa Abulahamu ndi Isaki, ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbadwa* zako.”+ 13  Kenako Mulungu anachoka pamalo amene ankalankhula ndi Yakobo. 14  Zitatero, Yakobo anaimika mwala wachikumbutso pamalo amene ankalankhula nayepo, kenako pamwalawo anathirapo nsembe yachakumwa ndi mafuta.+ 15  Ndiyeno Yakobo anatchulanso malo amene Mulungu analankhula nayewo kuti Beteli.+ 16  Kenako anachoka ku Beteliko. Kutatsala mtunda wautali kuti afike ku Efurata, nthawi yoti Rakele abereke inakwana, koma poberekapo anavutika kwambiri. 17  Pamene ankavutika kwambiri kuti abereke, mzamba* anamuuza kuti: “Usaope, chifukwa ubereka mwana wina wamwamuna.”+ 18  Pa nthawi imene moyo wake unkachoka (chifukwa anali akumwalira), anapereka dzina kwa mwanayo lakuti Beni-oni.* Koma bambo ake anamupatsa dzina lakuti Benjamini.*+ 19  Choncho Rakele anamwalira, ndipo anamuika mʼmanda mʼmbali mwa njira yopita ku Efurata, komwe ndi ku Betelehemu.+ 20  Yakobo anaika mwala pamandapo. Mwala umenewo ulipobe mpaka lero pamanda a Rakele. 21  Kenako Isiraeli ananyamuka nʼkukamanga tenti yake patsogolo pa nsanja ya Ederi. 22  Nthawi ina Isiraeli akukhala mʼdziko limenelo, Rubeni anagona ndi Biliha mkazi wamngʼono* wa bambo ake, ndipo Isiraeli anamva zimene zinachitikazo.+ Yakobo anali ndi ana aamuna 12. 23  Ana aamuna amene Leya anaberekera Yakobo anali Rubeni+ mwana wake woyamba, kenako Simiyoni, Levi, Yuda, Isakara ndi Zebuloni. 24  Ana amene Rakele anaberekera Yakobo anali Yosefe ndi Benjamini. 25  Ana amene Biliha kapolo wa Rakele anaberekera Yakobo anali Dani ndi Nafitali. 26  Ana amene Zilipa kapolo wa Leya anaberekera Yakobo anali Gadi ndi Aseri. Ana aamuna amene Yakobo anabereka ku Padani-aramu ndi amenewa. 27  Pamapeto pake Yakobo anafika kwa bambo ake Isaki ku Mamure,+ mʼdera la Kiriyati-ariba, komwe ndi ku Heburoni. Uku nʼkumenenso Abulahamu ndi Isaki anakhalako monga alendo.+ 28  Isaki anakhala ndi moyo zaka 180.+ 29  Kenako Isaki anamwalira, ndipo anaikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ake.* Anamwalira atakhala ndi moyo wautali komanso atakhutira ndi masiku a moyo wake ndipo ana ake, Esau ndi Yakobo, anamuika mʼmanda.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anabisa.”
Kutanthauza, “Mulungu wa ku Beteli.”
Mlezi ndi wantchito wamkazi amene amalera mwana.
Kutanthauza, “Mtengo Waukulu Wolirirapo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana amene adzatuluke mʼchiuno mwako adzakhala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
“Mzamba” ndi munthu amene amathandiza amayi pobereka. Ena amamutchula kuti “namwino.”
Kutanthauza, “Mwana wa Chisoni Changa.”
Kutanthauza, “Mwana wa Dzanja Langa Lamanja.”
“Mkazi wamngʼono” ameneyu anali kapolo wa Rakele.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anagona limodzi ndi makolo ake.”