Genesis 36:1-43

  • Mbadwa za Esau (1-30)

  • Mafumu a ku Edomu (31-43)

36  Mbiri ya Esau, kapena kuti Edomu,+ ndi iyi:  Esau anakwatira ana aakazi a ku Kanani. Anakwatira Ada,+ mwana wamkazi wa Eloni, Muhiti.+ Anakwatiranso Oholibama,+ yemwe anali mwana wamkazi wa Ana komanso anali mdzukulu wa Zibeoni, Mhivi.  Anakwatiranso Basemati,+ yemwe anali mwana wamkazi wa Isimaeli komanso anali mchemwali wake wa Nebayoti.+  Ada anaberekera Esau mwana dzina lake Elifazi, ndipo Basemati anamuberekera Reueli.  Ana amene Oholibama anaberekera Esau anali Yeusi, Yalamu ndi Kora.+ Amenewa anali ana a Esau amene anabereka mʼdziko la Kanani.  Pambuyo pake, Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi komanso ena onse amʼnyumba yake, ziweto zake zonse ndi chuma chake chonse chimene anachipeza+ mʼdziko la Kanani nʼkupita kudziko lina, kutali ndi Yakobo mchimwene wake.+  Iye anachoka chifukwa chuma chawo chinali chitachuluka kwambiri, moti sakanathanso kukhala limodzi. Mʼdziko limene ankakhalalo* malo anali ochepa chifukwa ziweto zawo zinali zambiri.  Choncho Esau anakakhazikika kudera lamapiri ku Seiri.+ Dzina lina la Esau linali Edomu.+  Imeneyi ndi mibadwo ya Esau, kholo la Aedomu, amene ankakhala kudera lamapiri la Seiri.+ 10  Mayina a ana a Esau ndi awa: Elifazi, mwana wamwamuna amene Ada mkazi wake wa Esau anabereka, komanso Reueli, mwana wamwamuna amene Basemati mkazi wake wa Esau anabereka.+ 11  Ana a Elifazi anali Temani,+ Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi.+ 12  Timina anali mkazi wamngʼono wa Elifazi mwana wa Esau. Patapita nthawi, Timina anaberekera Elifazi mwana wamwamuna dzina lake Amaleki.+ Ana a Ada mkazi wa Esau anali amenewa. 13  Ana a Reueli anali awa: Nahati, Zera, Shama ndi Miza. Ana a Basemati+ mkazi wa Esau anali amenewa. 14  Oholibama, mkazi wake wa Esau, anaberekera Esau ana aamuna awa: Yeusi, Yalamu ndi Kora. Oholibamayu anali mwana wa Ana komanso mdzukulu wa Zibeoni. 15  Mafumu a mafuko a ana a Esau ndi awa:+ Ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau anali: Mfumu Temani, Mfumu Omari, Mfumu Zefo, Mfumu Kenazi,+ 16  Mfumu Kora, Mfumu Gatamu ndi Mfumu Amaleki. Awa ndi amene anali mafumu akubanja la Elifazi+ mʼdziko la Edomu. Amenewa ndi ana a Ada. 17  Ana a Reueli, mwana wamwamuna wa Esau ndi awa: Mfumu Nahati, Mfumu Zera, Mfumu Shama ndi Mfumu Miza. Amenewa ndi amene anali mafumu akubanja la Reueli mʼdziko la Edomu.+ Amenewa anali ana a Basemati mkazi wa Esau. 18  Potsiriza, ana a Oholibama mkazi wa Esau ndi awa: Mfumu Yeusi, Mfumu Yalamu ndi Mfumu Kora. Amenewa ndi amene anali mafumu akubanja la Oholibama mkazi wa Esau, amenenso anali mwana wa Ana. 19  Amenewa anali ana a Esau kapena kuti Edomu+ ndi mafumu awo. 20  Ana a Seiri Mhori, nzika za dzikolo+ ndi awa: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana,+ 21  Disoni, Ezeri ndi Disani.+ Amenewa anali ana a Seiri, mafumu a fuko la Ahori, mʼdziko la Edomu. 22  Ana a Lotani anali Hori ndi Hemamu, ndipo Lotani anali ndi mchemwali wake dzina lake Timina.+ 23  Ana a Sobala anali Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu. 24  Ana a Zibeoni+ anali Aya ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi otentha mʼchipululu pa nthawi imene ankadyetsa abulu a Zibeoni bambo ake. 25  Ana anabereka ana awa: Disoni ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana. 26  Ana a Disoni anali Hemadani, Esibani, Itirani ndi Kerana.+ 27  Ana a Ezeri anali Bilihani, Zavani ndi Ekani. 28  Ana a Disani anali Uzi ndi Arani.+ 29  Mafumu a fuko la Ahori ndi awa: Mfumu Lotani, Mfumu Sobala, Mfumu Zibeoni, Mfumu Ana, 30  Mfumu Disoni, Mfumu Ezeri ndi Mfumu Disani.+ Amenewa ndi amene anali mafumu a fuko la Ahori mogwirizana ndi ufumu wawo mʼdziko la Seiri. 31  Mafumu amene analamulira dziko la Edomu,+ Aisiraeli* asanayambe kulamulidwa ndi mfumu ina iliyonse,+ ndi awa: 32  Bela mwana wa Beori analamulira Edomu, ndipo dzina la mzinda wake linali Dinihaba. 33  Bela atamwalira, Yobabi mwana wa Zera wa ku Bozira, anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 34  Yobabi atamwalira, Husamu wa ku Temani, anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 35  Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi amene anagonjetsa Amidiyani+ mʼdera la Mowabu, anayamba kulamulira mʼmalo mwake, ndipo dzina la mzinda wake linali Aviti. 36  Hadadi atamwalira, Samila wa ku Masereka anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 37  Samila atamwalira, Shauli wamumzinda wa Rehoboti, womwe unali mʼmbali mwa Mtsinje,* anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 38  Shauli atamwalira, Baala-hanani mwana wa Akibori, anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 39  Baala-hanani mwana wa Akibori atamwalira, Hadari anayamba kulamulira mʼmalo mwake, ndipo dzina la mzinda wake linali Pau. Mkazi wake dzina lake anali Mehetabele, mwana wa Matiredi. Matiredi anali mwana wamkazi wa Mezahabu. 40  Mayina a mafumu a Esau mogwirizana ndi mabanja awo komanso madera awo ndi awa: Mfumu Timina, Mfumu Aliva, Mfumu Yeteti,+ 41  Mfumu Oholibama, Mfumu Ela, Mfumu Pinoni, 42  Mfumu Kenazi, Mfumu Temani, Mfumu Mibezari, 43  Mfumu Magidieli ndi Mfumu Iramu. Amenewa ndi amene anali mafumu a Edomu mogwirizana ndi madera awo mʼdziko lawo.+ Mibadwo ya Esau, kholo la Aedomu+ ndi imeneyi.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ankakhalamo monga alendo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Isiraeli.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.