Genesis 37:1-36

  • Maloto a Yosefe (1-11)

  • Yosefe ndi abale ake ansanje (12-24)

  • Yosefe anagulitsidwa ku ukapolo (25-36)

37  Yakobo anapitiriza kukhala mʼdziko la Kanani, kumene bambo ake anakhalako ngati mlendo.+  Iyi ndi mbiri ya Yakobo. Yosefe+ ali ndi zaka 17, anapita kokadyetsa nkhosa+ limodzi ndi ana a Biliha+ ndi ana a Zilipa,+ omwe anali akazi a bambo ake. Ndiyeno Yosefe anakauza bambo ake zoipa zimene abale akewo ankachita.  Isiraeli ankamukonda kwambiri Yosefe kuposa ana ake onse,+ chifukwa anali mwana amene anamʼbereka atakalamba. Choncho anamusoketsera mkanjo wokongola.  Abale ake ataona kuti bambo awo ankakonda kwambiri Yosefe kuposa abale ake onse, anayamba kudana naye, moti sankalankhula naye mwamtendere.  Kenako Yosefe analota maloto ndipo anauza abale ake+ moti iwo anapeza chifukwa china chowapangitsa kuti azidana naye.  Iye anawauza kuti: “Tamvetserani maloto amene ine ndinalota.  Ndinalota tikumanga mitolo ya tirigu pakati pa munda. Mtolo wanga unadzuka nʼkuima chilili. Mitolo yanunso inadzuka nʼkuzungulira mtolo wanga ndipo inayamba kuuweramira.”+  Abale akewo anamufunsa kuti: “Kodi zoona iweyo ukuganiza kuti ungadzakhale mfumu yathu nʼkumatilamulira?”+ Choncho maloto amenewa komanso zimene ananena zinapangitsa kuti abale akewo apeze chifukwa chinanso choti azidana naye.  Tsiku linanso analota maloto ena, ndipo anauza abale akewo kuti: “Leronso ndinalota maloto ena. Ndinalota dzuwa ndi mwezi ndiponso nyenyezi zokwana 11 zikundigwadira.”+ 10  Kenako anafotokozeranso bambo ake ndi abale ake malotowo. Koma bambo ake anamʼdzudzula kuti: “Kodi maloto akowa akutanthauza chiyani? Kodi zoona ineyo ndi mayi akowa, komanso abale akowa tidzagwada pansi pamaso pa iwe?” 11  Abale akewo anamuchitira nsanje,+ koma bambo ake anasunga mawuwo mumtima. 12  Ndiyeno abale ake aja anapita kokadyetsa ziweto za bambo awo kufupi ndi ku Sekemu.+ 13  Kenako Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Kodi abale ako sakudyetsa ziweto pafupi ndi ku Sekemu? Tabwera ndikutume kwa iwo.” Iye anati: “Chabwino bambo.” 14  Ndiyeno Isiraeli anati: “Pita ukaone ngati abale ako ali bwino. Ukaonenso ngati ziweto zili bwino ndipo udzandiuze.” Choncho anamuuza kuti anyamuke kuchigwa cha Heburoni+ ndipo ananyamuka nʼkulowera ku Sekemu. 15  Kenako Yosefe akungoyendayenda kutchireko, munthu wina anakumana naye. Ndiyeno munthuyo anamufunsa kuti: “Kodi ukufufuza chiyani?” 16  Iye anayankha kuti: “Ndikufufuza abale anga. Tandiuzani chonde, kodi iwo akudyetsera kuti ziweto?” 17  Munthuyo anati: “Amenewo achoka kuno chifukwa ndinawamva akunena kuti, ‘Tiyeni tipite ku Dotani.’” Choncho Yosefe anawalondola abale akewo mpaka anakawapeza ku Dotani. 18  Abale akewo anamuonera patali akubwera, koma asanafike anayamba kukonza chiwembu kuti amuphe. 19  Ndiye anayamba kukambirana kuti: “Tamuonani wolota uja.+ Uyo akubwera apoyo! 20  Tiyeni timuphe nʼkumuponya muchitsime chopanda madzi, ndipo tikanene kuti chilombo cholusa chamudya. Tidzaone kuti chidzachitike nʼchiyani ndi maloto ake aja.” 21  Rubeni+ atamva zimenezo anayesa kumupulumutsa. Iye anati: “Ayi, tisamuphe.”+ 22  Rubeni anawauza kuti: “Musakhetse magazi.+ Muponyeni mʼchitsime chopanda madzichi kutchire kuno, koma musamuvulaze.”+ Cholinga chake chinali chakuti amupulumutse kwa iwo nʼkumubwezera kwa bambo ake. 23  Choncho Yosefe atangofika kwa abale akewo, anamuvula mkanjo wake wokongola uja, womwe anavala.+ 24  Atatero, anamutenga nʼkumuponya mʼchitsime chomwe pa nthawiyo chinali chopanda madzi. 25  Ndiyeno abale akewo anakhala pansi kuti adye chakudya. Koma atayangʼana, anaona gulu la Aisimaeli+ amene ankachokera ku Giliyadi. Ngamila zawo zinali zitanyamula zinthu zonunkhira monga labidanamu, basamu komanso makungwa a utomoni wonunkhira.+ Iwo anali pa ulendo wopita ku Iguputo. 26  Yuda atawaona, anauza abale ake kuti: “Tipindulapo chiyani tikapha mʼbale wathu ndi kubisa imfa yake?+ 27  Tiyeni timugulitse+ kwa Aisimaeliwa, tisamuvulaze. Ndipotu ndi mʼbale wathu ameneyu, magazi amodzi.”* Choncho iwo anamvera zimene mʼbale wawoyo ananena. 28  Pamene amalonda a Chimidiyani+ aja ankadutsa, abale a Yosefe anamutulutsa mʼchitsimemo nʼkumugulitsa kwa Aisimaeliwo. Anamugulitsa ndalama zasiliva 20,+ ndipo amalondawo anapita naye ku Iguputo. 29  Rubeni atabwerera kuchitsime kuja nʼkupeza kuti Yosefe mulibe mʼchitsimemo, anangʼamba zovala zake. 30  Atabwerera kwa abale ake aja, anafuula kuti: “Mwana ujatu kulibe! Mayo ine, nditani ine?” 31  Ndiyeno iwo anapha mbuzi yamphongo nʼkutenga mkanjo wa Yosefe uja nʼkuuviika mʼmagazi a mbuziyo. 32  Kenako, iwo anatumiza mkanjo uja kwa bambo awo ndipo bambowo anauzidwa kuti: “Tapeza mkanjo uwu. Chonde, uonetsetseni kuti muone ngati uli mkanjo wa mwana wanu kapena ayi.”+ 33  Bambowo anayangʼanitsitsa mkanjowo nʼkufuula kuti: “Mayo ine! Mkanjowu ndi wa mwana wanga! Chilombo cholusa chamudya mwana wanga. Wakhadzulidwa ndithu mwana wanga Yosefe!” 34  Atatero Yakobo anangʼamba zovala zake nʼkuvala chiguduli mʼchiuno mwake, ndipo anamulira mwana wake masiku ambiri. 35  Ana ake onse aamuna ndi aakazi ankapita kukamutonthoza, koma iye ankakana kutonthozedwa. Ankanena kuti: “Ayi! Ndidzalira mpaka kutsikira ku Manda*+ kumene kuli mwana wanga.” Ndipo bambo akewo anapitiriza kumulira. 36  Amidiyani aja anakamugulitsa Yosefe ku Iguputo kwa Potifara. Potifara anali nduna yapanyumba ya Farao,+ ndiponso anali mkulu wa asilikali olondera mfumu.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “thupi limodzi.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.