Genesis 39:1-23

  • Yosefe mʼnyumba ya Potifara (1-6)

  • Yosefe anakana kugona ndi mkazi wa Potifara (7-20)

  • Yosefe anaikidwa mʼndende (21-23)

39  Kenako Aisimaeli+ aja anapita naye Yosefe ku Iguputo+ ndipo anakamugulitsa kwa munthu wina wa ku Iguputo dzina lake Potifara.+ Potifara anali nduna yapanyumba ya Farao, komanso mkulu wa asilikali olondera mfumu. 2  Koma Yehova anali ndi Yosefe,+ moti chilichonse chimene ankachita chinkamuyendera bwino. Ndipo anaikidwa kuti aziyangʼanira nyumba ya munthu wa ku Iguputo uja, amene anali mbuye wake. 3  Mbuye wakeyo anaona kuti Yehova anali ndi mnyamatayo komanso kuti Yehova ankathandiza mnyamatayo kuti chilichonse chimene ankachita chiziyenda bwino. 4  Potifara anapitiriza kumukonda Yosefe ndipo anakhala mtumiki amene ankamudalira. Choncho anamusankha kuti akhale woyangʼanira nyumba yake komanso zinthu zonse zimene anali nazo. 5  Kuyambira pamene Potifara anasankha Yosefe kukhala woyangʼanira nyumba yake ndi zinthu zake zonse, Yehova anapitiriza kudalitsa nyumba ya munthu wa ku Iguputoyo chifukwa cha Yosefe. Yehova anadalitsa zonse zamʼnyumba ya Potifara ndi zakumunda zomwe.+ 6  Kenako Potifara anasiya zinthu zake zonse mʼmanja mwa Yosefe, moti sankadera nkhawa chilichonse kupatulapo kusankha chakudya choti adye. Komanso Yosefe anali wooneka bwino ndiponso wa thupi loumbika bwino. 7  Kenako, mkazi wa mbuye wake anayamba kuyangʼana Yosefe momusirira, moti ankamuuza kuti: “Ugone nane.” 8  Koma Yosefe ankakana ndipo ankauza mkazi wa mbuye wakeyo kuti: “Mbuye wanga sadera nkhawa chilichonse mʼnyumba muno chifukwa cha ine, ndipo chilichonse chimene iye ali nacho wachisiya mʼmanja mwanga. 9  Mʼnyumba muno mulibe woyangʼanira woposa ine, ndipo mbuye wanga anaika chilichonse mʼmanja mwanga kupatulapo inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake. Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi nʼkuchimwira Mulungu?”+ 10  Mkaziyo ankalankhula ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, koma iye sanamvere zoti agone pambali pake kapena kuti agone naye. 11  Tsiku lina Yosefe analowa mʼnyumba kuti akagwire ntchito yake, ndipo mʼnyumbamo munalibe antchito ena. 12  Choncho mkaziyo anagwira malaya a mnyamatayo nʼkumuuza kuti: “Ugone nane basi!” Koma mnyamatayo anangovula malayawo nʼkuwasiya mʼmanja mwa mkaziyo nʼkuthawira panja. 13  Mkaziyo ataona kuti mnyamatayo wasiya malaya ake mʼmanja mwake nʼkuthawira panja, 14  anayamba kufuulira antchito ena amʼnyumbamo, kuti: “Taonani! Anatibweretsera mwamuna wa Chiheberiyu kuti adzatichite chipongwe anthu nʼkutiseka. Iye anabwera kwa ine kuti adzandigwiririre, koma ndinakuwa mwamphamvu. 15  Ndiye ataona kuti ndayamba kukuwa, anasiya malaya ake pambali pangapa nʼkuthawira panja.” 16  Atatero, anasunga malaya a mnyamatayo pambali pake mpaka mwamuna wake atabwera kunyumbako. 17  Mwamuna wake atafika, mkaziyo anamuuzanso mawu omwe aja akuti: “Wantchito wa Chiheberi amene munatibweretsera uja, anabwera kwa ine kuti andichite zachipongwe. 18  Koma ataona kuti ndayamba kukuwa, anasiya malaya ake pambali pangapa nʼkuthawira panja.” 19  Mbuye wa mnyamatayo atamva zimene mkazi wake anamuuza zakuti: “Wantchito wanu anachita zakutizakuti,” anapsa mtima kwambiri. 20  Zitatero, mbuye wake wa Yosefe anamutenga nʼkukamusiya kundende ya akaidi a mfumu kuti akamutsekere, ndipo Yosefe anakhala kumeneko.+ 21  Koma Yehova anapitirizabe kukhala ndi Yosefe nʼkumamusonyeza chikondi chokhulupirika ndipo anachititsa kuti mkulu wa ndende azimukonda.+ 22  Choncho, mkulu wa ndendeyo anasankha Yosefe kuti aziyangʼanira akaidi onse mʼndendemo, ndi chilichonse chimene chinkachitika mmenemo.+ 23  Mkulu wa ndendeyo sankayangʼaniranso chilichonse chimene chinali mʼmanja mwa Yosefe. Zinali choncho chifukwa Yehova anali ndi Yosefe, ndipo Yehova ankamuthandiza kuti chilichonse chimene iye ankachita chiziyenda bwino.+

Mawu a M'munsi