Genesis 41:1-57

  • Yosefe anamasulira maloto a Farao (1-36)

  • Yosefe anapatsidwa udindo ndi Farao (37-46a)

  • Yosefe ankayangʼanira ntchito yogawa chakudya (46b-57)

41  Patatha zaka ziwiri zathunthu, Farao analota+ ataimirira mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo.  Iye anaona ngʼombe 7 zikutuluka mumtsinje wa Nailo. Ngʼombezo zinali zooneka bwino komanso zonenepa, ndipo zinkadya udzu wamʼmbali mwa mtsinjewo.+  Pambuyo pake anaonanso ngʼombe zina 7 zikutuluka mumtsinje wa Nailowo. Zimenezi zinali zonyansa ndi zowonda, ndipo zinaima pambali pa zonenepazo mʼmbali mwa mtsinjewo.  Ndiye ngʼombe zonyansa ndi zowondazo zinayamba kudya ngʼombe 7 zooneka bwino ndi zonenepa zija. Kenako Farao anadzidzimuka.  Ndiyeno Farao anagonanso nʼkulota maloto ena. Mʼmalotowa anaona ngala za tirigu 7 zikutuluka paphesi limodzi. Ngalazo zinali zokhwima ndi zazikulu bwino.+  Pambuyo pake anaonanso ngala zina 7 zikutuluka. Ngalazo zinali zonyala komanso zowauka ndi mphepo yakumʼmawa.  Ngala zonyalazo zinayamba kumeza ngala 7 zokhwima ndi zazikulu bwinozo. Kenako Farao anadzidzimuka ndipo anazindikira kuti anali maloto.  Mʼmawa kutacha, Farao anavutika kwambiri maganizo. Choncho anaitanitsa ansembe onse amatsenga ndi amuna anzeru onse a mu Iguputo, nʼkuwafotokozera malotowo. Koma palibe amene anatha kumumasulira Farao maloto akewo.  Kenako mkulu wa operekera zakumwa uja anauza Farao kuti: “Lero ndiulule machimo anga. 10  Inuyo Farao munatikwiyira kwambiri ife atumiki anu. Ineyo ndi mkulu wa ophika mkate munatitsekera mʼndende yakunyumba kwa mkulu wa asilikali olondera mfumu.+ 11  Kundendeko tonse awiri tinalota maloto usiku umodzi. Aliyense analota maloto ndipo malotowo anali ndi matanthauzo osiyana.+ 12  Tinalinso ndi mnyamata wina wa Chiheberi kumeneko. Iyeyo anali wantchito wa mkulu wa asilikali olondera mfumu.+ Titamufotokozera maloto athu,+ anatimasulira matanthauzo ake. Aliyense anamumasulira mogwirizana ndi maloto amene analota. 13  Zimene anamasulira nʼzomwedi zinachitika. Ineyo ndinabwezeretsedwa pa ntchito, koma mnzangayo anapachikidwa.”+ 14  Choncho Farao anatuma anthu kukatenga Yosefe+ kundendeko,* ndipo anabwera naye mofulumira.+ Yosefe anameta bwinobwino, kenako anasintha zovala nʼkukaonekera pamaso pa Farao. 15  Ndiyeno Farao anauza Yosefe kuti: “Ine ndalota maloto, ndipo palibe munthu amene wakwanitsa kuwamasulira. Koma ndamva kuti iweyo ukamva maloto umatha kumasulira.”+ 16  Yosefe anayankha Farao kuti: “Mulungu ndi amene anene nkhani yabwino yokhudza inu Farao, osati ine.”+ 17  Farao anafotokozera Yosefe kuti: “Ndinalota nditaima mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo. 18  Ndiyeno ndinaona ngʼombe 7 zonenepa ndi zooneka bwino zikutuluka mumtsinje wa Nailo, ndipo zinayamba kudya udzu wa mʼmbali mwa mtsinjewo.+ 19  Pambuyo pake ndinaonanso ngʼombe zina 7 zikutuluka mumtsinjewo. Ngʼombe zimenezi zinali zonyansa ndi zowonda. Sindinaonepo ngʼombe zonyansa ngati zimenezo mʼdziko lonse la Iguputo. 20  Ngʼombe zowonda ndi zonyansazo zinayamba kudya ngʼombe 7 zonenepa zija. 21  Koma ngakhale zinadya zinzakezo, palibe akanadziwa chifukwa ngʼombezo zimaonekabe zowonda ngati poyamba. Kenako ndinadzidzimuka. 22  Ndiyeno ndinalotanso maloto ena. Ndinalota ngala 7 za tirigu, zokhwima ndi zooneka bwino, zikutuluka paphesi limodzi.+ 23  Pambuyo pake ndinaonanso ngala zina 7 zikutuluka ndipo zinali zonyala komanso zowauka ndi mphepo yakumʼmawa. 24  Ndiyeno ngala zonyalazo zinayamba kumeza ngala 7 zooneka bwinozo. Ndinafotokozera malotowa ansembe amatsenga,+ koma palibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kumasulira.”+ 25  Pamenepo Yosefe anauza Farao kuti: “Maloto anu awiriwa tanthauzo lake ndi limodzi. Mulungu woona wakudziwitsani inu Farao zimene adzachite.+ 26  Ngʼombe 7 zonenepazo zikuimira zaka 7. Komanso ngala 7 zooneka bwinozo zikuimira zaka 7. Malotowa tanthauzo lake ndi limodzi. 27  Ngʼombe 7 zowonda ndi zonyansazo, zimene zinatuluka pambuyo pa zoyamba zija, zikuimira zaka 7. Komanso ngala 7 zopanda kanthu ndiponso zowauka ndi mphepo yakumʼmawa, zidzakhala zaka 7 za njala. 28  Choncho, monga ndakuuzirani inu Farao, Mulungu woona wakuonetsani zimene adzachite. 29  Kukubwera zaka 7 zimene kudzakhala chakudya chochuluka mʼdziko lonse la Iguputo. 30  Koma pambuyo pa zaka zimenezo, padzabwera zaka 7 za njala. Chakudya chonse chochuluka cha mʼdziko la Iguputo chija chidzaiwalika, ndipo njalayo idzawononga dziko lonse.+ 31  Sizidzadziwika kuti mʼdzikoli pa nthawi ina munali chakudya chambiri, chifukwa njalayo idzakhala yoopsa kwambiri. 32  Inu Farao mwalota kawiri malotowa chifukwa Mulungu woona watsimikiza mtima kuchita zimenezi, ndipo Mulungu woona azichita posachedwapa. 33  Choncho inu Farao mufufuze munthu wozindikira ndi wanzeru, ndipo mumuike kuti akhale woyangʼanira dziko la Iguputo. 34  Inu Farao muike anthu oyangʼanira mʼdziko lino, ndipo muzitenga gawo limodzi mwa magawo 5 a chakudya cha dziko la Iguputo pa zaka 7 zimene kudzakhale zokolola zochuluka.+ 35  Mʼzaka zimene kudzakhale chakudya chambiri, oyangʼanirawo azidzasonkhanitsa tirigu yense nʼkumusunga bwino mʼmizinda ndipo adzakhale wa inu Farao.+ 36  Chakudya chimenecho chidzakhala chakudya cha dzikoli pa zaka 7 zimene mʼdziko la Iguputo mudzakhale njala, kuti anthu ndi ziweto asadzafe ndi njalayo.”+ 37  Zimene Yosefe ananena zinasangalatsa Farao ndi antchito ake onse. 38  Ndiyeno Farao anafunsa antchito ake kuti: “Kodi pangapezekenso munthu wina ngati uyu, amene ali ndi mzimu wa Mulungu?” 39  Kenako Farao anauza Yosefe kuti: “Popeza kuti Mulungu wakudziwitsa zonsezi, palibenso munthu wina wozindikira ndi wanzeru ngati iwe. 40  Iweyo ukhala woyangʼanira nyumba yanga, ndipo anthu anga onse azimvera chilichonse chimene iweyo ungawauze.+ Koma ine ndekha ndikhala wamkulu kwa iwe chifukwa ndine mfumu.” 41  Farao anauzanso Yosefe kuti: “Tsopano ndikukuika kukhala woyangʼanira dziko lonse la Iguputo.”+ 42  Atatero, Farao anavula mphete yake yachifumu kudzanja lake nʼkuveka Yosefe. Anamuvekanso zovala zokongola komanso tcheni chagolide mʼkhosi mwake. 43  Ndiponso anamukweza pagaleta lina la Farao,* ndipo anthu ankafuula patsogolo pake kuti, “A·vrékh!”* Choncho Farao anamupatsa udindo woyangʼanira dziko lonse la Iguputo. 44  Farao anauzanso Yosefe kuti: “Farao ndine, koma popanda chilolezo chako, palibe wina aliyense amene angachite* chilichonse mʼdziko lonse la Iguputo.”+ 45  Kenako Farao anapatsa Yosefe dzina lakuti Zafenati-panea.* Anamʼpatsanso mkazi dzina lake Asenati+ yemwe anali mwana wa Potifera, wansembe wa mzinda wa Oni.* Ndipo Yosefe anayamba kuyangʼanira* dziko la Iguputo.+ 46  Yosefe anali ndi zaka 30+ pamene anayamba kutumikira* Farao, mfumu ya Iguputo. Kenako anachoka pamaso pa Farao nʼkuyamba kuyendera dziko lonse la Iguputo. 47  Pa zaka zonse 7 zimene dzikolo linabereka chakudya chochuluka, mʼdzikolo munali chakudya chamwanaalirenji. 48  Pa zaka 7 zimenezo, Yosefe anasonkhanitsa chakudya chonse chimene anakolola mʼdziko lonse la Iguputo nʼkuchisunga mʼmizinda. Mumzinda uliwonse, ankasunga chakudya chochokera mʼminda yozungulira mzindawo. 49  Yosefe anapitiriza kusunga tirigu, mpaka anachuluka kwambiri ngati mchenga wakunyanja moti anasiya kumuyeza chifukwa sakanathanso kumuyeza chifukwa anali wambiri. 50  Chaka choyamba cha njala chisanafike, Yosefe anakhala ndi ana aamuna awiri,+ amene anamʼberekera mkazi wake Asenati, mwana wa Potifera, wansembe wa mzinda wa Oni. 51  Mwana woyambayo, Yosefe anamupatsa dzina lakuti Manase*+ chifukwa anati, “Mulungu wandiiwalitsa mavuto anga onse ndi nyumba yonse ya bambo anga.” 52  Wachiwiriyo anamupatsa dzina lakuti Efuraimu*+ chifukwa anati, “Mulungu wandipatsa ana mʼdziko la masautso anga.”+ 53  Kenako zaka 7 zimene mʼdziko la Iguputo munali chakudya chochuluka zinatha.+ 54  Ndipo zaka 7 za njala zinayamba, mogwirizana ndi zimene Yosefe ananena.+ Njalayo inali mʼmayiko onse, koma dziko lonse la Iguputo linali ndi chakudya.+ 55  Kenako njala ija inafika mʼdziko lonse la Iguputo, ndipo anthu anayamba kulirira Farao kuti awapatse chakudya.+ Koma Farao anauza Aiguputo onse kuti: “Pitani kwa Yosefe, ndipo mukachite chilichonse chimene akakuuzeni.”+ 56  Njala ija inapitirizabe padziko lonse lapansi.+ Zitatero, Yosefe anayamba kutsegula nkhokwe zonse zimene zinali pakati pawo nʼkuyamba kugulitsa chakudya kwa Aiguputo,+ chifukwa njalayo inali itafika poipa kwambiri mʼdziko la Iguputo. 57  Komanso, anthu padziko lonse lapansi anayamba kubwera ku Iguputo kudzagula chakudya kwa Yosefe, chifukwa njalayo inali itafika poipa kwambiri padziko lonse lapansi.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼchitsimemo; mʼdzenjemo.”
Galeta limeneli linali la munthu amene anali wachiwiri kwa Farao.
Zikuoneka kuti mawuwa ndi ouza anthu kuti apereke ulemu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene anganyamule dzanja lake kapena phazi lake.”
Zikuoneka kuti mʼChiheberi, dzinali limatanthauza “Woulula Zinthu Zobisika.”
Amene ndi Heliyopolisi.
Kapena kuti, “kuyendera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pamene anaima pamaso pa.”
Kutanthauza, “Wochititsa Kuiwala; Woiwalitsa.”
Kutanthauza, “Kubereka Kawiri.”