Genesis 42:1-38

  • Azichimwene ake a Yosefe anapita ku Iguputo (1-4)

  • Yosefe anakumana ndi azichimwene ake ndipo anawayesa (5-25)

  • Azichimwene ake a Yosefe anabwerera kwa Yakobo (26-38)

42  Yakobo atamva kuti ku Iguputo kuli tirigu,+ anafunsa ana ake kuti: “Kodi muzingoyangʼanana?”  Anapitiriza kuti: “Ine ndamva kuti ku Iguputo kuli tirigu. Pitani mukatigulire kuti tikhalebe ndi moyo, tisafe ndi njala.”+  Choncho abale ake a Yosefe 10+ anapita ku Iguputo kuti akagule tirigu.  Koma Yakobo sanalole kuti Benjamini,+ mʼbale wake wa Yosefe, apite limodzi ndi abale akewo chifukwa anati: “Mwina ngozi yoopsa ingamuchitikire nʼkufa.”+  Ndiyeno ana a Isiraeliwo anafika ku Iguputo limodzi ndi anthu ena okagula tirigu, chifukwa mʼdziko la Kanani munali njala.+  Yosefe ndi amene anali wolamulira mʼdzikomo+ ndipo ndi amene ankagulitsa tirigu kwa anthu onse ochokera kumayiko ena onse.+ Choncho abale a Yosefe anafika kwa iye ndipo anagwada nʼkumuweramira mpaka nkhope zawo pansi.+  Yosefe ataona abale akewo, nthawi yomweyo anawazindikira, koma iye anayesetsa kuti asamuzindikire.+ Choncho analankhula nawo mwaukali nʼkuwafunsa kuti: “Mwachokera kuti?” Iwo anayankha kuti: “Tachokera kudziko la Kanani, ndipo tabwera kudzagula chakudya.”+  Ngakhale kuti Yosefe anawazindikira abale akewo, iwo sanamʼzindikire.  Nthawi yomweyo Yosefe anakumbukira maloto ake aja okhudza abale akewo.+ Choncho anawauza kuti: “Inu ndinu akazitape! Mwabwera kuno kudzafufuza malo amene dziko lathu lili lofooka!” 10  Koma iwo anakana kuti: “Ayi mbuyathu, akapolo anufe tabwera kudzagula chakudya. 11  Tonsefe ndife ana a munthu mmodzi, ndipo ndife anthu achilungamo. Akapolo anufe sitichita zaukazitape.” 12  Koma iye anawauza kuti: “Mukunama! Mwabwera kuno kudzafufuza malo ofooka a dziko lathu.” 13  Iwo anati: “Akapolo anufe ndife pachibale ndipo tinalipo 12.+ Ndife ana a munthu mmodzi+ wa ku Kanani. Wamngʼono kwambiri watsala ndi bambo athu,+ koma mmodzi kulibenso.”+ 14  Komabe Yosefe anawauza kuti: “Ndiye kuti zimene ndanena zija ndi zoona kuti, ‘Anthu inu ndi akazitape!’ 15  Ndiye ndikuyesani kuti ndione ngati mukunena zoona: Pali Farao wamoyo, ndithu simuchoka kuno mpaka mngʼono wanuyo atabwera.+ 16  Tumani mmodzi wa inu kuti apite kukatenga mngʼono wanuyo. Enanu ndikutsekerani mʼndende. Ndikufuna ndione ngati mukunena zoona. Ndipo ngati si zoona, pali Farao wamoyo, ndiye kuti ndinu akazitape basi.” 17  Atatero, anawatsekera mʼndende onse pamodzi kwa masiku atatu. 18  Pa tsiku lachitatu, Yosefe anawauza kuti: “Chitani izi kuti mukhale ndi moyo, chifukwa ndimaopa Mulungu. 19  Ngati mulidi achilungamo, mmodzi wa inu atsale mʼndendemu. Ena nonsenu mukhoza kumapita kuti mukapereke tirigu kunyumba zanu chifukwa kuli njala.+ 20  Ndiyeno mukabweretse mngʼono wanuyo kwa ine. Mukatero, ndidzatsimikiza kuti mukunena zoona, moti simudzaphedwa.” Iwo anachitadi zomwezo. 21  Kenako iwo anayamba kukambirana kuti: “Ndithudi, izi zikuchitika chifukwa cha zimene tinachitira mʼbale wathu uja.+ Pajatu tinaona mmene ankamvetsera chisoni pamene ankatichonderera kuti timuchitire chifundo, koma ife sitinamumvere. Nʼchifukwa chaketu takumana ndi tsoka limeneli.” 22  Ndiyeno Rubeni anayankha kuti: “Kodi ine sindinakuuzeni kuti, ‘Mwanayu musamuchitire zoipaʼ?* Koma inu simunamvere.+ Si izi nanga, magazi ake akufunidwatu kwa ife.”+ 23  Iwo sanadziwe kuti Yosefe akumva zimene ankanenazo, chifukwa ankalankhula nawo kudzera mwa womasulira. 24  Ndiyeno Yosefe anapita kwayekha kukalira.+ Kenako anabwerako nʼkuyambiranso kulankhula nawo, ndipo anatenga Simiyoni+ nʼkumumanga iwo akuona.+ 25  Atatero Yosefe analamula anyamata ake kuti awathirire tirigu mʼmatumba awo mpaka kudzaza komanso kuti aliyense amubwezere ndalama zake pomuikira mʼthumba lake. Anawalamulanso kuti awapatse chakudya cha pa ulendo. Anyamatawo anawachitiradi zimenezo. 26  Choncho iwo ananyamulitsa abulu awo tiriguyo nʼkuyamba ulendo wawo. 27  Atafika pamalo oti agone, mmodzi wa iwo anamasula thumba lake kuti atengemo chakudya choti apatse bulu wake. Atamasula, anangoona kuti ndalama zake zili pakamwa pa thumbalo. 28  Iye anauza abale akewo kuti: “Taonani! Ndalama zanga andibwezera, izi zili mʼthumbazi!” Choncho mitima yawo inangoti myuu! ndipo anayamba kunjenjemera nʼkuyamba kufunsana kuti: “Kodi Mulungu akutichitira chiyani ife?” 29  Atafika kwa bambo awo Yakobo mʼdziko la Kanani, anawafotokozera zonse zimene zinawachitikira kuti: 30  “Nduna yaikulu ya dzikolo inalankhula nafe mwaukali,+ chifukwa inationa ngati akazitape okafufuza dzikolo. 31  Koma tinaiuza kuti, ‘Ndife anthu achilungamo, si ife akazitape.+ 32  Ndife ana a bambo mmodzi ndipo tinalipo ana aamuna 12.+ Koma mmodzi kulibenso,+ ndipo wamngʼono ali ndi bambo athu kudziko la Kanani.’+ 33  Ndiye nduna yaikulu ya dzikolo inatiuza kuti, ‘Ngati mulidi achilungamo muchite izi: Mmodzi wa inu atsale ndi ine kuno.+ Koma enanu tengani chakudya, mupite nacho kunyumba zanu chifukwa kuli njala.+ 34  Mukabweretse mʼbale wanu wamngʼonoyo kwa ine kuti ndidzatsimikize kuti si inu akazitape koma anthu achilungamo. Mukatero, ndidzakubwezerani mʼbale wanuyu, ndipo mudzatha kuchita malonda mʼdziko lino.’” 35  Pamene ankakhuthula matumba awo, aliyense anapeza kachikwama ka ndalama zake mʼthumba lake. Iwo limodzi ndi bambo awo ataona ndalamazo, anachita mantha. 36  Yakobo bambo awo anadandaula kuti: “Inetu mwandisandutsa namfedwa!+ Yosefe anapita,+ Simiyoni kulibenso.+ Tsopano mukufuna kutenga Benjamini! Nʼchifukwa chiyani zonsezi zikundichitikira?” 37  Koma Rubeni anauza bambo ake kuti: “Ngati Benjamini sindidzabwera naye kwa inu, mudzaphe ana anga aamuna awiri.+ Mumupereke mʼmanja mwanga, ndipo ndidzamʼbwezera kwa inu.”+ 38  Koma bambowo anati: “Zoti mwana wanga apite nanu, izo ndiye ndakana, chifukwa mʼbale wake anafa, ndipo iye anatsala yekha.+ Ngati ngozi yoopsa itamuchitikira panjira nʼkufa, ndithu mudzatsitsira ku Manda*+ imvi zanga chifukwa cha chisoni.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “musamuchimwire.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.