Genesis 43:1-34
43 Tsopano njala ija inakula kwambiri mʼdzikomo.+
2 Tirigu amene anabweretsa kuchokera ku Iguputo+ uja atatha, bambo awo anawauza kuti: “Pitaninso mukatigulireko kachakudya pangʼono.”
3 Koma Yuda anauza bambo ake kuti: “Munthu ujatu anatichenjeza momveka bwino kuti, ‘Musadzabwerenso kwa ine* pokhapokha mʼbale wanuyo mutabwera naye.’+
4 Mukalola kuti mʼbale wathuyu timutenge, tipita ku Iguputo kuti tikakugulireni chakudya.
5 Koma ngati simutilola kupita naye, sitipitako, chifukwa munthu uja anatiuza kuti, ‘Musadzabwerenso kwa ine pokhapokha mʼbale wanuyo mutabwera naye.’”+
6 Ndiyeno Isiraeliyo+ anafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwandiputira mavuto pomuuza munthuyo kuti muli ndi mʼbale wanu wina?”
7 Koma iwo anayankha kuti: “Munthuyo anachita kufunsa zokhudza ife ndi banja lathu kuti, ‘Kodi bambo anu adakali ndi moyo? Kodi muli ndi mʼbale wanu wina?’ Ndipo ife tinamuuza zoona.+ Nanga tikanadziwa bwanji zoti anena kuti, ‘Mukabwere naye kuno mʼbale wanuyoʼ?”+
8 Kenako Yuda anauza Isiraeli bambo ake kuti: “Ndiloleni ndimutenge mnyamatayu+ kuti tinyamuke tizipita kuti tikhalebe ndi moyo tisafe,+ inuyo ndi ife, limodzi ndi ana athuwa.+
9 Moyo wa mnyamatayu ukhale mʼmanja mwanga.*+ Ngati chinachake chitamuchitikira mudzandilange. Ndikadzapanda kubwera naye ndi kumʼpereka kwa inu, ndidzakhale wochimwa kwa inu moyo wanga wonse.
10 Ndipotu tikanapanda kuzengereza, bwenzi pano titapita nʼkubwerako maulendo awiri.”
11 Ndiyeno bambo awo Isiraeli anawauza kuti: “Ngati ndi choncho, chitani izi: Tengani zinthu zamtengo wapatali zamʼdziko lino mʼmatumba anu, mukamʼpatse munthuyo monga mphatso.+ Tengani mafuta a basamu+ pangʼono, uchi pangʼono, labidanamu, khungwa la utomoni wonunkhira,+ mtedza wa pisitasho ndi zipatso za amondi.
12 Mutengenso ndalama kuchulukitsa kawiri zoyamba zija. Komanso mutenge ndalama zimene anakubwezerani zija, zomwe munazipeza pakamwa pa matumba anu,+ mukazibweze. Mwina anangosokoneza.
13 Mutenge mʼbale wanuyu ndipo mupitenso kwa munthuyo.
14 Mulungu Wamphamvuyonse apangitse munthuyo kukuchitirani chifundo, kuti akamasule mʼbale wanu uja, ndipo mukabwere naye limodzi ndi Benjamini. Koma ngati ndingataye ana angawa, chabwino, zikhale choncho!”+
15 Ndiyeno amunawo anatenga mphatso zija, ndalama kuchulukitsa kawiri ndiponso Benjamini, nʼkunyamuka kupita ku Iguputo. Kumeneko anakaonananso ndi Yosefe.+
16 Yosefe atangoona Benjamini ali ndi abale akewo, anauza mwamuna amene ankayangʼanira nyumba yake kuti: “Pita nawo kunyumba anthuwa ndipo ukaphe nyama ndi kukonza chakudya, chifukwa anthuwa adya ndi ine masana ano.”
17 Nthawi yomweyo mwamuna uja anachita zimene Yosefe ananena.+ Anatenga anthu aja nʼkupita nawo kunyumba kwa Yosefe.
18 Koma amunawo atapita nawo kunyumba kwa Yosefe, anachita mantha ndipo anati: “Atibweretsa kuno chifukwa cha ndalama zimene anatibwezera mʼmatumba athu pa ulendo woyamba uja. Anthu amenewa atiukira nʼkutigwira kuti tikhale akapolo ndipo atilanda abulu athu!”+
19 Choncho iwo anapita kwa munthu woyangʼanira nyumba ya Yosefe uja nʼkulankhula naye pakhomo lolowera mʼnyumbamo.
20 Iwo anati: “Pepani mbuyathu! Ifetu tinabwera kuno kudzagula chakudya ulendo woyamba.+
21 Koma pobwerera, titafika pamalo oti tigone, tinamasula matumba athu ndipo tinangoona kuti ndalama za aliyense zili pakamwa pa thumba lake, zonse mogwirizana ndi kulemera kwake.+ Choncho tabwera nazo kuti tizibweze tokha.
22 Tabwera ndi ndalama zina zogulira chakudya. Koma sitikudziwa kuti ndi ndani amene anatiikira ndalama mʼmatumba athu.”+
23 Pamenepo mwamunayo anati: “Musachite mantha, simunalakwe chilichonse. Mulungu wanu, Mulungu wa bambo anu ndi amene anaika chumacho mʼmatumba mwanu. Ndalama zanu ndinalandira kale.” Atatero mwamunayo anamasula Simiyoni nʼkumupititsa kwa iwo.+
24 Kenako munthuyo analowetsa amunawo mʼnyumba ya Yosefe. Anawapatsa madzi kuti asambe mapazi awo nʼkuwapatsanso chakudya choti adyetse abulu awo.
25 Amunawo anakonzeratu mphatso+ zimene anabwera nazo zija kuti apatse Yosefe masanawo, popeza anali atamva kuti adya nawo limodzi chakudya kumeneko.+
26 Ndiyeno Yosefe atafika nʼkulowa mʼnyumbamo, iwo anapereka mphatsozo kwa iye. Ndipo anamugwadira nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+
27 Kenako Yosefe anawafunsa za moyo wawo. Anawafunsanso kuti: “Kodi bambo anu okalamba amene munkanena aja ali bwanji? Kodi adakali ndi moyo?”+
28 Iwo anayankha kuti: “Kapolo wanu bambo athu ali bwino. Adakali ndi moyo.” Atatero anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+
29 Yosefe atakweza maso ake nʼkuona mngʼono wake Benjamini, mʼbale wake wa mimba imodzi,+ anati: “Kodi uyu ndi mngʼono wanu amene munkanena uja?”+ Ananenanso kuti: “Mulungu akukomere mtima mwana wanga.”
30 Ndiyeno Yosefe anachokapo mofulumira chifukwa anagwidwa chifundo ataona mʼbale wakeyo. Anafunafuna malo oti akalirireko, ndiye analowa mʼchipinda chimene munalibe anthu nʼkugwetsa misozi.+
31 Kenako, anasamba kumaso nʼkutuluka ndipo anadzilimbitsa nʼkunena kuti: “Ikani chakudya.”
32 Iwo anamuikira Yosefe chakudya payekha. Abale akewo anawaikiranso paokha. Nawonso Aiguputo amene ankadya mʼnyumba mwake anawaikira paokha. Aiguputo sankadya limodzi ndi Aheberi, chifukwa chinali chinthu chonyansa kwa iwo.+
33 Abale akewo anawauza kuti akhale pansi pamaso pake, kuyambira wamkulu kwambiri*+ mpaka wamngʼono kwambiri. Iwo ankangoyangʼanana modabwa.
34 Yosefe ankatapa chakudya patebulo pake nʼkumapatsa operekera chakudya kuti aziwonjezera pachakudya cha abale akewo. Koma chakudya chimene ankapatsa Benjamini ankachichulukitsa maulendo 5 kuposa cha ena onsewo.+ Choncho iwo anapitiriza kudya ndi kumwa naye limodzi mosangalala mpaka kukhuta.