Genesis 44:1-34

  • Kapu yasiliva ya Yosefe inapezeka mʼthumba la Benjamini (1-17)

  • Yuda anapempha kuti akhale kapolo mʼmalo mwa Benjamini (18-34)

44  Kenako Yosefe analamula woyangʼanira nyumba yake uja kuti: “Udzazitse chakudya mʼmatumba a anthuwa chimene angakwanitse kunyamula. Aliyense umubwezere ndalama zake ndipo uziike pakamwa pa thumba lake.+  Koma uike kapu yanga yasiliva ija pakamwa pa thumba la wamngʼonoyo limodzi ndi ndalama zake zogulira tirigu.” Choncho woyangʼanira nyumba yakeyo anachita zimene Yosefe anamuuzazo.  Mʼmawa kutacha, abale ake a Yosefe aja anawalola kuti azipita pamodzi ndi abulu awo.  Iwo asanapite patali kuchokera mumzindawo, Yosefe anauza woyangʼanira nyumba yake kuti: “Nyamuka, athamangire anthu aja. Ukawapeza uwafunse kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mwabwezera zoipa pa zabwino?  Nʼchifukwa chiyani mwaba kapu yomwera mbuye wanga, imenenso amaombezera pofuna kudziwa zinthu? Mwachita chinthu choipa kwambiri.’”  Choncho munthu uja atawapeza, anawafunsa zimenezo.  Koma iwo anamuyankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukulankhula choncho mbuyathu? Nʼzosatheka kuti akapolo anufe tichite zinthu ngati zimenezo.  Pajatu ndalama zimene tinazipeza pakamwa pa matumba athu kudziko la Kanani tinazibweza kwa inu.+ Ndiye zingatheke bwanji kuti tibe siliva ndi golide mʼnyumba ya mbuye wanu?  Amene apezeke ndi kapuyo mwa akapolo anufe aphedwe, ndipo enafe tikhale akapolo anu mbuyathu.” 10  Ndiyeno iye anati: “Chabwino, zichitike mmene mwaneneramo. Amene ati apezeke nayo akhala kapolo wanga, koma enanu mukhala opanda mlandu.” 11  Zitatero, aliyense anatsitsa pansi thumba lake mwamsanga nʼkulimasula. 12  Munthu uja anafufuza mosamala mʼmatumba awo, kuyambira la wamkulu kumalizira ndi la wamngʼono. Pamapeto pake, kapuyo inapezeka mʼthumba la Benjamini.+ 13  Zitatero, iwo anangʼamba zovala zawo. Kenako aliyense anakwezanso thumba lake pabulu wake nʼkubwerera kumzinda kuja. 14  Yuda+ ndi abale ake atalowa mʼnyumba ya Yosefe, anamupeza adakali mʼnyumbamo, ndipo iwo anagwada nʼkumuweramira mpaka nkhope zawo pansi.+ 15  Yosefe anati: “Ndiye chiyani mwachitachi? Kodi inu simukudziwa kuti munthu ngati ine ndingathe kudziwa zinthu poombeza maula?”+ 16  Ndiyeno Yuda anayankha kuti: “Kodi tinganene chiyani kwa inu mbuyathu? Tilankhule kuti chiyani? Titani kuti muone kuti sitinalakwe? Pamenepa Mulungu woona ndi amene wapeza cholakwa mwa ife akapolo anu.+ Basi, titengeni ndife akapolo anu mbuyathu, ifeyo limodzi ndi amene mwamʼpeza ndi kapuyo.” 17  Koma Yosefe anati: “Sindingachite zimenezo! Amene wapezeka ndi kapu yangayo ndi amene akhale kapolo wanga.+ Enanu mupite kwa bambo anu mwamtendere.” 18  Tsopano Yuda anayandikira kwa Yosefe nʼkunena kuti: “Chonde mbuyanga, ndikukupemphani. Ndiloleni kapolo wanune kuti ndinene mawu amodzi okha. Chonde musandipsere mtima, chifukwa inu muli ngati Farao yemwe.+ 19  Pajatu inu mbuyanga munatifunsa akapolo anufe kuti: ‘Kodi muli ndi bambo kapena mʼbale wanu wina?’ 20  Ife tinakuyankhani mbuyanga kuti, ‘Bambo tili nawo koma ndi okalamba. Ali ndi mwana amene anabereka atakalamba, yemwe ndi wamngʼono kwa tonsefe.+ Mʼbale wake wa mimba imodzi anamwalira,+ moti anatsala yekha+ ndipo bambo amamukonda kwambiri.’ 21  Kenako inu munatiuza ife akapolo anu kuti, ‘Mukabwere naye kuno kuti ndidzamuone.’+ 22  Koma ife tinakuuzani inu mbuyanga kuti, ‘Mwanayo sangachoke kwa bambo ake. Atati achoke, ndithu bambo akewo akhoza kufa.’+ 23  Ndiyeno munatiuza ife akapolo anu kuti, ‘Musadzabwerenso kwa ine* pokhapokha ngati mʼbale wanuyo mutabwera naye.’+ 24  Choncho ife tinapita kwa kapolo wanu, bambo athu, ndipo tinawauza zimene munanena mbuyanga. 25  Patapita nthawi bambo athu anatiuza kuti, ‘Pitaninso mukatigulireko kachakudya pangʼono.’+ 26  Koma ife tinati, ‘Sitingathe kupitanso. Ngati mungatilole kutenga mngʼono wathuyu tipitako, chifukwa sitingathe kukaonananso ndi munthuyo pokhapokha ngati mngʼono wathuyu titapita naye.’+ 27  Ndiyeno kapolo wanu bambo athuwo anatiuza kuti, ‘Inuyo mukudziwa bwino kuti mkazi wanga anandiberekera ana awiri okha.+ 28  Koma mmodzi wa awiriwo anandisiya, ndipo ndinafuula kuti: “Mayo ine! Wakhadzulidwa ndithu mwana wanga!”+ moti sindinamuonenso mpaka lero. 29  Ndiye ngati uyunso mungapite naye, ngozi yoopsa nʼkumuchitikira panjira nʼkufa, ndithu mudzatsitsira ku Manda*+ imvi zanga chifukwa cha chisoni.’+ 30  Bambo amamʼkonda kwambiri mwanayu ngati mmene amakondera moyo wawo. Choncho ndikakangofika kwa kapolo wanu bambo anga ndilibe mwanayu, 31  iwo nʼkuona kuti mwanayu palibe, basi akafa. Ndithu, akapolo anufe tidzatsitsira ku Manda* imvi za kapolo wanu bambo athu chifukwa cha chisoni. 32  Ine kapolo wanu ndinalonjeza bambo anga kuti moyo wa mwanayu udzakhala mʼmanja mwanga. Ndinalonjeza kuti, ‘Ndikadzalephera kubwera naye kwa inu, ndidzakhale wochimwa kwa inu bambo anga moyo wanga wonse.’+ 33  Ndiye chonde mbuyanga, tengani ineyo ndikhale kapolo wanu mʼmalo mwa mwanayu, kuti iye apite ndi abale akewa. 34  Ndingathe bwanji kupita kwa bambo anga ndilibe mwanayu? Ayi, sindikufuna kukaona bambo anga akuzunzika.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Musadzaonenso nkhope yanga.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.