Genesis 46:1-34

  • Yakobo ndi banja lake anasamukira ku Iguputo (1-7)

  • Mayina a anthu amene anasamukira ku Iguputo (8-27)

  • Yosefe anakumana ndi Yakobo ku Goseni (28-34)

46  Choncho Isiraeli anatenga banja lake komanso zinthu zonse zimene anali nazo nʼkunyamuka. Atafika ku Beere-seba+ anapereka nsembe kwa Mulungu wa bambo ake Isaki.+  Ndiyeno Mulungu analankhula ndi Isiraeli mʼmasomphenya usiku kuti: “Yakobo, Yakobo!” Ndipo Yakobo anayankha kuti: “Ine mbuyanga!”  Mulungu anamuuza kuti: “Ine ndine Mulungu woona, Mulungu wa bambo ako.+ Usaope kupita ku Iguputo, chifukwa kumeneko ndidzakupangitsa kukhala mtundu waukulu.+  Ineyo ndipita nawe ku Iguputo, ndiponso ine ndi amene ndidzabwere nawe mʼdziko lino kuchokera kumeneko.+ Ndipo Yosefe ndi amene adzakutseke maso pa imfa yako.”+  Kenako Yakobo ananyamuka ku Beere-sebako. Ana a Isiraeliwo anatenga Yakobo bambo awo, limodzi ndi ana awo komanso akazi awo. Anawatengera mʼngolo zimene Farao anatumiza.  Anatenganso ziweto zawo zonse ndi katundu wawo yense amene anapeza mʼdziko la Kanani. Kenako Yakobo ndi ana ake onse anafika ku Iguputo.  Anafika limodzi ndi ana ake aamuna ndi aakazi limodzinso ndi zidzukulu zake. Anafika ndi banja lake lonse.  Awa ndi mayina a ana a Isiraeli, kapena kuti ana a Yakobo, omwe anapita nawo ku Iguputo:+ Mwana woyamba wa Yakobo anali Rubeni.+  Ana a Rubeni anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karami.+ 10  Ana a Simiyoni+ anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shauli+ mwana wa mkazi wa Chikanani. 11  Ana a Levi+ anali Gerisoni, Kohati ndi Merari.+ 12  Ana a Yuda+ anali Ere, Onani, Shela,+ Perezi+ ndi Zera.+ Koma Ere ndi Onani anafera kudziko la Kanani.+ Ana a Perezi anali Hezironi ndi Hamuli.+ 13  Ana a Isakara anali Tola, Puva, Yabi ndi Simironi.+ 14  Ana a Zebuloni+ anali Seredi, Eloni ndi Yahaleeli.+ 15  Amenewa ndi ana a Leya, amene anaberekera Yakobo ku Padani-aramu, kuphatikizapo Dina+ mwana wamkazi wa Yakobo. Ana onse aamuna ndi aakazi komanso zidzukulu zake analipo 33. 16  Ana a Gadi+ anali Zifioni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli.+ 17  Ana a Aseri+ anali Imuna, Isiva, Isivi ndi Beriya ndipo mchemwali wawo anali Sera. Ana a Beriya anali Hiberi ndi Malikieli.+ 18  Amenewa ndi ana a Zilipa,+ yemwe Labani anamupereka kwa mwana wake wamkazi Leya. Iye anaberekera Yakobo ana amenewa. Onse pamodzi analipo 16. 19  Ana a Rakele, mkazi wa Yakobo, anali Yosefe+ ndi Benjamini.+ 20  Yosefe anabereka Manase+ ndi Efuraimu+ ku Iguputo. Anabereka anawa ndi mkazi wake Asenati+ mwana wa Potifera, wansembe wa mzinda wa Oni.* 21  Ana a Benjamini+ anali Bela, Bekeri, Asibeli, Gera,+ Namani, Ehi, Rosi, Mupimu, Hupimu+ ndi Aridi.+ 22  Amenewa ndi ana amene Rakele anaberekera Yakobo. Onse pamodzi analipo 14. 23  Mwana wa* Dani+ anali Husimu.+ 24  Ana a Nafitali+ anali Yahazeeli, Guni, Yezera ndi Silemu.+ 25  Amenewa ndi ana a Biliha, yemwe Labani anamupereka kwa mwana wake wamkazi Rakele. Iye anaberekera Yakobo ana amenewa. Onse pamodzi analipo 7. 26  Mbadwa zonse za Yakobo zimene anapita nazo ku Iguputo zinalipo 66,+ osawerengera akazi a ana ake. 27  Ana amene Yosefe anabereka ku Iguputo analipo awiri. Anthu onse amʼnyumba ya Yakobo amene anali nawo ku Iguputo analipo 70.+ 28  Yakobo anatumiza Yuda+ kuti atsogole kupita kwa Yosefe kukamudziwitsa kuti akubwera ku Goseni. Iwo atafika ku Goseni,+ 29  Yosefe anauza anthu kuti amukonzere galeta lake, kenako ananyamuka kuti akakumane ndi Isiraeli bambo ake ku Goseni. Atangofika kwa bambo akewo, nthawi yomweyo anawakumbatira nʼkulira kwa kanthawi.* 30  Kenako Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Tsopano ndingathe kufa mwamtendere. Ndaona nkhope yako ndipo ndadziwa kuti udakali moyo.” 31  Ndiyeno Yosefe anauza abale ake ndi amʼnyumba ya bambo ake kuti: “Ndipite kwa Farao+ ndikamudziwitse kuti, ‘Abale anga ndi amʼnyumba ya bambo anga amene anali mʼdziko la Kanani, abwera kuno kwa ine.+ 32  Anthuwa ndi abusa+ ndipo amaweta ziweto.+ Abwera ndi nkhosa, ngʼombe ndi zinthu zonse zimene ali nazo.’+ 33  Farao akakuitanani nʼkukufunsani kuti, ‘Kodi mumagwira ntchito yanji?’ 34  Inu mukayankhe kuti: ‘Akapolo anufe takhala tikuweta ziweto kuyambira tili ana kufikira lero, ifeyo ndi makolo athu omwe.’+ Mukayankhe choncho kuti mukhale ku Goseni+ kuno, chifukwa aliyense woweta nkhosa Aiguputo amanyansidwa naye.”+

Mawu a M'munsi

Amene ndi Heliyopolisi.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana a.” Nʼkutheka kuti panali ana ena aamuna amene mayina awo sanatchulidwe.
Kapena kuti, “nʼkulira mobwerezabwereza.”