Genesis 47:1-31

  • Yakobo anakumana ndi Farao (1-12)

  • Yosefe anagwira ntchito yoyangʼanira mwanzeru (13-26)

  • Isiraeli anakhazikika ku Goseni (27-31)

47  Choncho Yosefe anapita kwa Farao nʼkukamuuza kuti:+ “Bambo anga ndi abale anga abwera kuchokera ku Kanani. Abwera ndi nkhosa zawo, ngʼombe zawo ndi zonse zimene ali nazo, ndipo afikira ku Goseni.”+ 2  Pa abale akewo, Yosefe anatengapo 5 nʼkukamuonetsa Farao.+ 3  Farao anafunsa abale ake a Yosefe aja kuti: “Kodi mumagwira ntchito yanji?” Iwo anayankha Farao kuti: “Akapolo anufe timaweta nkhosa ngati mmene ankachitira makolo athu.”+ 4  Kenako anauza Farao kuti: “Tabwera kuno kudzakhala monga alendo,+ chifukwa akapolo anufe tilibe chakudya chopatsa ziwetozi, popeza njala yafika poipa kwambiri ku Kanani.+ Ndiye chonde, tiloleni ife akapolo anu tikhale ku Goseni.”+ 5  Zitatero Farao anauza Yosefe kuti: “Bambo ako ndi abale akowa abwera kuno kwa iwe. 6  Dziko la Iguputo lili mʼmanja mwako, choncho uwapatse malo abwino kwambiri.+ Uwauze kuti akhale ku Goseni, ndipo ngati ukudziwapo amuna olimbikira ntchito, uwaike kuti akhale oyangʼanira ziweto zanga.” 7  Kenako Yosefe anabweretsa bambo ake Yakobo nʼkuwasonyeza kwa Farao, ndipo Yakobo anadalitsa Farao. 8  Ndiyeno Farao anafunsa Yakobo kuti: “Kodi muli ndi zaka zingati?” 9  Yakobo anayankha Farao kuti: “Ndili ndi zaka 130 ndipo pa zaka zimenezi ndakhala ndikuyendayenda* mʼmalo osiyanasiyana. Ndakhala ndi moyo zaka zowerengeka komanso zosautsa,+ ndipo si zambiri poyerekezera ndi zaka zimene makolo anga akhala akuyendayenda mʼmalo osiyanasiyana.”+ 10  Atatero, Yakobo anadalitsa Farao nʼkuchoka pamaso pake. 11  Choncho Yosefe anauza bambo ake ndi abale akewo kuti azikhala ku Iguputo. Anawapatsa malo abwino kwambiri adzikolo ku Ramese*+ monga mmene Farao analamulira. 12  Kumeneko, Yosefe ankapatsa chakudya bambo ake, abale ake ndi banja lonse la bambo ake, mogwirizana ndi kuchuluka kwa ana awo. 13  Chakudya chinatheratu mʼdziko lonselo ndipo njala inafika poipa kwambiri. Anthu onse a ku Iguputo ndi a ku Kanani anali ofooka chifukwa cha njalayo.+ 14  Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse zimene zinali mʼdziko la Iguputo ndi la Kanani, zomwe anthu ankagulira chakudya.+ Iye ankatenga ndalamazo nʼkuzipititsa kunyumba kwa Farao. 15  Pamapeto pake, ndalama zonse zamʼdziko la Iguputo ndi dziko la Kanani zinatha. Choncho anthu onse a ku Iguputo anayamba kufika kwa Yosefe nʼkunena kuti: “Tipatseni chakudya! Kodi tikufereni mukuona chifukwa choti ndalama zatithera?” 16  Ndiye Yosefe anati: “Ngati ndalama zakutherani, bweretsani ziweto zanu tidzasinthane ndi chakudya.” 17  Choncho anthuwo anayamba kubweretsa ziweto zawo kwa Yosefe. Yosefeyo ankawapatsa chakudya posinthanitsa ndi mahatchi awo, nkhosa, ngʼombe ndi abulu. Mʼchaka chonsecho, Yosefe ankawapatsa chakudya posinthanitsa ndi ziweto zawo. 18  Chakacho chitatha, anthu anayamba kupita kwa iye chaka chotsatira. Iwo ankanena kuti: “Tisakubisireni mbuyathu, ndalama zathu ndi ziweto zonse zatha chifukwa tinazipereka kwa inu. Tilibenso chilichonse choti tikupatseni kupatulapo matupi athuwa komanso minda yathu. 19  Tiferenji ife inu mukuona, ndipo minda yathu ikhalirenji yogonera? Mutigule limodzi ndi minda yathu potipatsa chakudya kuti tikhale akapolo a Farao. Mutipatse tirigu kuti tikhale ndi moyo tisafe, komanso kuti minda yathu isagonere.” 20  Choncho Yosefe anagulira Farao minda yonse ya Aiguputo, chifukwa munthu aliyense wa mu Iguputo anagulitsa munda wake. Anachita zimenezi chifukwa njala inali itafika poopsa, moti minda yonse inakhala ya Farao. 21  Kenako Yosefe anasamutsira anthuwo mʼmizinda, kuchokera kumalire a dziko la Iguputo mpaka kumalire ena.+ 22  Malo a ansembe okha ndi amene sanawagule,+ chifukwa chakudya chimene ansembe ankadya chinkachokera kwa Farao. Nʼchifukwa chake ansembewo sanagulitse malo awo. 23  Ndiyeno Yosefe anauza anthuwo kuti: “Onani, ndakugulani inu lero limodzi ndi minda yanu kuti mukhale a Farao. Tengani mbewu iyi, mukadzale mʼmindamo. 24  Nthawi yokolola ikakwana, muzipereka kwa Farao gawo limodzi mwa magawo 5 a zokololazo.+ Magawo 4 otsalawo muzigwiritsa ntchito monga mbewu yodzala mʼmindamo, chakudya chanu ndi cha anthu amʼnyumba zanu komanso cha ana anu.” 25  Iwo anayankha kuti: “Mwapulumutsa miyoyo yathu.+ Mwatikomera mtima mbuyathu, ndipo tidzakhala akapolo a Farao.”+ 26  Choncho Yosefe anakhazikitsa lamulo limene lilipobe mpaka lero lakuti, Farao azilandira gawo limodzi mwa magawo 5 a zokolola za minda yonse ya mu Iguputo. Koma malo a ansembe okha sanakhale a Farao.+ 27  Aisiraeliwo anakhazikika mʼdziko la Iguputo, mʼdera la Goseni.+ Kumeneko anaberekana nʼkuchulukana kwambiri.+ 28  Ndipo Yakobo anakhalabe ndi moyo mʼdziko la Iguputo kwa zaka 17. Choncho Yakobo anakhala ndi moyo zaka 147.+ 29  Tsopano nthawi yakuti Isiraeli amwalire inayandikira.+ Ndiye anaitana mwana wake Yosefe nʼkumuuza kuti: “Ngati ungandikomere mtima, ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga. Ulumbire kuti udzandisonyeza chikondi chokhulupirika komanso kuti udzakhala wokhulupirika kwa ine. Chonde, usadzandiike mʼmanda ku Iguputo kuno.+ 30  Ndikadzamwalira,* udzandinyamule kuchoka ku Iguputo kuno nʼkukandiika mʼmanda a makolo anga.”+ Yosefe anayankha kuti: “Ndidzachitadi mogwirizana ndi zimene mwanena.” 31  Ndiyeno Yakobo anati: “Lumbira kwa ine.” Yosefe analumbira kwa iye.+ Zitatero Isiraeli anawerama nʼkutsamira kumutu kwa bedi lake.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ndakhala ngati mlendo.”
Zikuoneka kuti Ramese chinali chigawo cha mʼdera la Goseni kapena linali dzina lina la Goseni.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndikadzagona ndi makolo anga.”