Genesis 50:1-26

  • Yosefe anaika mʼmanda Yakobo ku Kanani (1-14)

  • Yosefe anatsimikizira abale ake kuti anawakhululukira (15-21)

  • Masiku akumapeto kwa moyo wa Yosefe ndi imfa yake (22-26)

    • Lamulo la Yosefe lokhudza mafupa ake (25)

50  Choncho Yosefe anakumbatira bambo ake+ ndipo analira kwambiri nʼkuwakisa.*  Kenako Yosefe analamula atumiki ake omwe anali madokotala, kuti akonze mtembo wa bambo ake ndi mankhwala kuti usawonongeke.+ Choncho madokotalawo anakonza mtembo wa Isiraeli.  Anatenga masiku 40 akukonza thupi lake, chifukwa kukonza mtembo kunkatenga masiku ochuluka choncho. Aiguputowo anapitiriza kumulira Isiraeli kwa masiku 70.  Masiku olira maliro a Yakobo atatha, Yosefe anauza nduna* za Farao kuti: “Ngati mungandikomere mtima, chonde mukandiperekere uthenga uwu kwa Farao:  ‘Bambo anga anandilumbiritsa+ kuti: “Inetu ndikufa.+ Ukandiike mʼmanda amene ndinakonza+ mʼphanga kudziko la Kanani.”+ Ndiye chonde, ndiloleni ndipite ndikaike bambo anga, pambuyo pake ndikabweranso.’”  Farao anayankha kuti: “Pita ukaike bambo ako mogwirizana ndi mmene anakulumbiritsira.”+  Choncho Yosefe anapita kukaika bambo ake. Atumiki onse a Farao, akuluakulu+ amʼnyumba yake ndi akuluakulu onse amʼdziko la Iguputo anamuperekeza.  Anthu onse amʼnyumba ya Yosefe, abale ake, ndi anthu amʼnyumba ya bambo ake, anapita naye limodzi.+ Ku Goseni kunangotsala ana awo aangʼono, nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe zawo.  Anatenganso magaleta+ ndi anthu okwera mahatchi, moti gululo linali lalikulu kwambiri. 10  Kenako anafika pamalo opunthira mbewu a Atadi mʼchigawo cha Yorodano. Kumeneko, anthuwo analira mokweza kwambiri, ndipo Yosefe analira maliro a bambo ake kwa masiku 7. 11  Akanani amene ankakhala mʼdzikolo anaona anthuwo akulira pamalo opunthira mbewu a Atadi, ndipo anati: “Aiguputowa ali pa chisoni chachikulu kwambiri!” Nʼchifukwa chake malowo anawatchula kuti Abele-miziraimu,* ndipo ali mʼchigawo cha Yorodano. 12  Choncho ana a Yakobowo anamuchitira zonse zimene iye anawalamula.+ 13  Ana akewo anamunyamula nʼkupita naye kudziko la Kanani ndipo anakamuika mʼphanga mʼmunda wa Makipela, umene uli moyangʼanizana ndi munda wa Mamure. Mundawo ndi umene Abulahamu anagula kwa Efuroni, Muhiti, kuti akhale manda.+ 14  Yosefe ataika bambo ake mʼmanda, anabwerera ku Iguputo limodzi ndi abale ake ndi onse amene anamuperekeza pokaika bambo akewo. 15  Abale ake a Yosefe ataona kuti bambo awo amwalira, ananena kuti: “Mwina Yosefe anatisungira chidani, ndipo atibwezera zoipa zonse zimene tinamuchitira.”+ 16  Choncho iwo anatumiza uthenga kwa Yosefe wakuti: “Bambo anu asanamwalire anatisiyira mawu. Anatiuza kuti: 17  ‘Mukamuuze Yosefe kuti: “Mwana wanga, zimene abale ako anakuchitira si zabwino. Koma ndikukupempha kuti uwakhululukire zonse zimene anakuchitira.”’ Ndiye chonde, tikhululukireni ife akapolo a Mulungu wa bambo anu.” Atamuuza zimenezi, Yosefe analira kwambiri. 18  Kenako abale akewonso anafika nʼkudzigwetsa pansi pamaso pake, ndipo ananena kuti: “Tikudzipereka kwa inu ngati akapolo anu.”+ 19  Yosefe anawauza kuti: “Musaope. Kodi ine ndatenga malo a Mulungu? 20  Ngakhale kuti munali ndi cholinga chondichitira zoipa,+ Mulungu anali ndi cholinga chabwino, kuti apulumutse miyoyo ya anthu ambiri ngati mmene akuchitira panomu.+ 21  Ndiye musachite mantha. Ine ndipitiriza kukupatsani chakudya limodzi ndi ana anu.”+ Choncho anawalimbikitsa komanso kuwatsimikizira zimenezi. 22  Yosefe anapitiriza kukhala ku Iguputo limodzi ndi anthu amʼnyumba ya bambo ake, ndipo Yosefe anakhala ndi moyo zaka 110. 23  Yosefe anakhalabe ndi moyo mpaka kuona ana a Efuraimu+ amʼbadwo wachitatu. Anaonanso ana a Makiri+ mwana wa Manase. Onsewo anabadwira pamawondo a Yosefe.* 24  Potsirizira pake, Yosefe anauza abale ake kuti: “Ine ndikufa, koma Mulungu adzakuthandizani+ ndipo adzakutulutsani ndithu mʼdziko lino. Adzakupititsani kudziko limene analumbira kuti adzalipereka kwa Abulahamu, kwa Isaki ndi kwa Yakobo.”+ 25  Tsopano Yosefe analumbiritsa ana a Isiraeliwo kuti: “Ndithu Mulungu adzakuthandizani. Choncho mudzatenge mafupa anga pochoka kuno.”+ 26  Yosefe anamwalira ali ndi zaka 110. Thupi lake analikonza ndi mankhwala kuti lisawonongeke,+ ndipo analiika mʼbokosi ku Iguputo.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “nʼkuwapsompsona.”
Kapena kuti, “anthu amʼnyumba ya Farao.”
Kutanthauza, “Kulira Maliro kwa Aiguputo.”
Kutanthauza kuti, ankawaona ngati ana ake ndipo ankawakonda mwapadera.