Genesis 9:1-29

  • Malangizo opita kwa anthu onse (1-7)

    • Lamulo lokhudza magazi (4-6)

  • Pangano la utawaleza (8-17)

  • Maulosi okhudza mbadwa za Nowa (18-29)

9  Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nʼkuwauza kuti: “Muberekane, muchuluke ndipo mudzaze dziko lapansi.+  Chamoyo chilichonse chapadziko lapansi, chamoyo chilichonse chouluka mumlengalenga, chilichonse chokwawa padziko lapansi, ndi nsomba zonse zamʼnyanja, zidzapitiriza kukuopani. Tsopano ndapereka zonsezi mʼmanja mwanu.*+  Mukhoza kudya chamoyo chilichonse choyenda padziko lapansi.+ Monga mmene ndinakupatsirani zomera zonse kuti zikhale chakudya chanu, ndikukupatsaninso zonsezi.+  Koma musadye+ nyama limodzi ndi magazi ake,+ chifukwa magaziwo ndi moyo wake.  Kuwonjezera pamenepo, aliyense amene adzakupheni* ndidzamupatsa chilango. Ngati chamoyo chilichonse chapha munthu, chamoyocho chidzaphedwanso. Ndipo munthu aliyense wochotsa moyo wa mʼbale wake, ndidzamupatsa chilango.+  Aliyense wopha munthu, nayenso adzaphedwa ndi munthu,*+ chifukwa Mulungu anapanga munthu mʼchifaniziro chake.+  Koma inuyo muberekane ndi kuchuluka kwambiri, ndipo mudzaze padziko lonse lapansi.”+  Kenako Mulungu anauza Nowa ndi ana ake kuti:  “Tsopano ine ndikuchita pangano ndi inu+ komanso mibadwo yobwera pambuyo panu. 10  Ndikuchitanso panganoli ndi chamoyo chamtundu uliwonse chimene muli nacho limodzi, monga mbalame, zinyama komanso zamoyo zonse zapadziko lapansi, kutanthauza zonse zimene zinatuluka mʼchingalawa, kapena kuti chamoyo chilichonse chapadziko lapansi.+ 11  Pangano limene ndikuchita nanu ndi ili: Zamoyo zonse sizidzawonongedwanso ndi chigumula, ndipo chigumula sichidzachitikanso nʼkuwononga dziko lapansi.”+ 12  Mulungu anawonjezera kuti: “Ichi ndi chizindikiro cha pangano limene ndikuchita ndi inu komanso ndi chamoyo chilichonse chimene muli nacho, mpaka mibadwo yonse ya mʼtsogolo. 13  Ndaika utawaleza wanga mumtambo, ndipo ukhala chizindikiro cha pangano la pakati pa ine ndi dziko lapansi. 14  Ndikabweretsa mtambo padziko lapansi, utawaleza udzaonekeranso mumtambowo. 15  Ndizikumbukira ndithu pangano limene ndachita ndi inu komanso ndi chamoyo cha mtundu uliwonse. Ndipo chigumula sichidzachitikanso nʼkuwononga zamoyo zonse.+ 16  Utawalezawo udzaonekera mumtambo, ndipo ndikauona ndizikumbukira pangano limene lidzakhale mpaka kalekale, pakati pa ine ndi chamoyo cha mtundu uliwonse chimene chili padziko lapansi.” 17  Mulungu anabwereza kuuza Nowa kuti: “Ichi ndi chizindikiro cha pangano limene ine ndikukhazikitsa ndi zamoyo zonse zimene zili padziko lapansi.”+ 18  Ana a Nowa amene anatuluka mʼchingalawa anali Semu, Hamu ndi Yafeti.+ Patapita nthawi, Hamu anabereka Kanani.+ 19  Ana a Nowa anali atatu amenewa, ndipo anthu onse anachokera kwa iwowa nʼkufalikira padziko lonse lapansi.+ 20  Tsopano Nowa anayamba ulimi, ndipo analima munda wa mpesa. 21  Tsiku lina Nowa anamwa vinyo nʼkuledzera, ndipo ali mutenti yake, anavula zovala zake. 22  Ndiyeno Hamu, bambo ake a Kanani, anaona maliseche a bambo ake. Atatero, anapita panja nʼkukauza abale ake awiri aja. 23  Atamva zimenezo, Semu ndi Yafeti anatenga chofunda nʼkuchiika pamapewa awo ndipo anayenda chafutambuyo. Atalowa mutentimo, anafunditsa bambo awo nʼkuwabisa maliseche, iwo akuyangʼana kumbali moti sanaone maliseche a bambo awo. 24  Vinyo atamuthera mʼmutu mwake, Nowa anadzuka ndipo anamva zimene mwana wake wamngʼono anachita. 25  Ndiyeno iye anati: “Kanani+ akhale wotembereredwa. Akhale kapolo wotsika kwambiri wa abale ake.”+ 26  Anawonjezera kuti: “Atamandike Yehova, Mulungu wa Semu,Ndipo Kanani akhale kapolo wa Semu.+ 27  Mulungu apereke malo aakulu kwa Yafeti,Ndipo azikhala mʼmatenti a Semu. Koma Kanani akhalenso kapolo wa Yafeti.” 28  Pambuyo pa Chigumula,+ Nowa anakhalabe ndi moyo zaka zina 350. 29  Choncho Nowa anakhala ndi moyo zaka 950, kenako anamwalira.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ndakupatsani kuti muzizilamulira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “aliyense amene adzakhetse magazi anu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Aliyense wokhetsa magazi a munthu, nayenso magazi ake adzakhetsedwa ndi munthu.”