Habakuku 1:1-17

  • Mneneri anapempha thandizo (1-4)

    • ‘Inu Yehova, mpaka liti?’ (2)

    • “Nʼchifukwa chiyani mukulekerera kuponderezana?” (3)

  • Mulungu anagwiritsa ntchito Akasidi popereka chiweruzo (5-11)

  • Mneneri anachonderera Yehova (12-17)

    • ‘Inu Mulungu wanga, simufa’ (12)

    • ‘Ndinu woyera moti simungaonerere zinthu zoipa’ (13)

1  Uwu ndi uthenga umene ine, mneneri Habakuku,* ndinalandira mʼmasomphenya. Ndinati:   “Inu Yehova, kodi ndidzalirira thandizo koma inu osandimva mpaka liti?+ Kodi ndidzapempha thandizo kuti mundipulumutse ku chiwawa koma inu osachitapo kanthu mpaka liti?+   Nʼchifukwa chiyani mukundichititsa kuona zinthu zoipa? Nʼchifukwa chiyani mukulekerera kuponderezana? Nʼchifukwa chiyani kuwononga zinthu komanso chiwawa zikuchitika pamaso panga? Ndipo nʼchifukwa chiyani mikangano ndi kumenyana zachuluka?   Choncho lamulo latha mphamvu,Ndipo anthu sakuchitanso chilungamo. Oipa akupondereza anthu olungama,Nʼchifukwa chake chilungamo chikupotozedwa.+   Yangʼanani pakati pa mitundu ya anthu ndipo muyangʼanitsitse. Muyangʼane modabwa. Dabwani ndithu.Chifukwa pali zimene zichitike mʼmasiku anu,Zimene simungakhulupirire ngakhale wina atakufotokozerani.+   Ine ndikubweretsa Akasidi,+Mtundu wankhanza ndiponso waphuma. Umene umathamanga mʼmadera ambiri apadziko lapansi,Kukalanda nyumba zimene si zawo.+   Mtundu umenewu ndi woopsa ndiponso wochititsa mantha. Umapanga malamulo akeake ndipo umadzipatsa wokha ulamuliro.+   Mahatchi* ake ndi aliwiro kuposa akambuku,Ndi oopsa kuposa mimbulu usiku.+ Mahatchi ake ankhondo amathamanga kwambiri.Mahatchi awo amachokera kutali. Ndipo amauluka ngati chiwombankhanga chimene chikuthamanga kuti chikapeze chakudya.+   Mtunduwo umabwera wonse kuti udzachite chiwawa.+ Ukakumana pamodzi umayenda ngati mphepo yochokera kumʼmawa,+Ndipo anthu amene wagwira umawakokolola ngati mchenga. 10  Mtunduwu umanyodola mafumu,Ndipo umaseka nduna zapamwamba.+ Umasekanso malo alionse okhala ndi mpanda wolimba,+Ndipo umaunjika dothi kenako nʼkulanda malowo. 11  Kenako mtunduwo umayenda ngati mphepo ndipo umadutsa mʼdziko.Koma udzapalamula,+Chifukwa choganiza kuti mulungu wawo ndi amene wawapatsa mphamvu.”*+ 12  Inu Yehova, mwakhala mulipo kuyambira kalekale.+ Inu Mulungu wanga, Mulungu wanga Woyera, inu simufa.*+ Inu Yehova, mwasankha Akasidi kuti apereke chiweruzo chanu.Inu Thanthwe langa,+ mwawasankha kuti mupereke chilango.*+ 13  Maso anu ndi oyera kwambiri moti simungaonerere zinthu zoipa,Ndipo simungalekerere khalidwe loipa.+ Ndiye nʼchifukwa chiyani mukulekerera anthu achinyengo,+Komanso mukukhala chete pamene munthu woipa akumeza munthu wolungama kuposa iyeyo?+ 14  Nʼchifukwa chiyani mukuchititsa munthu kukhala ngati nsomba zamʼnyanja,Ndiponso ngati zokwawa zimene zilibe mtsogoleri? 15  Iye* amakola zonsezi ndi mbedza, Ndipo amazikokolola ndi khoka lake.Nʼkuzisonkhanitsa muukonde wophera nsomba. Nʼchifukwa chake iye amasangalala kwambiri.+ 16  Nʼchifukwa chake amapereka nsembe kwa khoka lake,Ndipo amapereka nsembe yautsi kwa ukonde wake wophera nsomba.Iye amatero chifukwa khoka ndi ukondewo zimamuthandiza kupeza chakudya chambiri.*Ndipo chakudya chake ndi chapamwamba. 17  Ndiye kodi adzapitirizabe kukhuthula nsomba zamʼkhoka* lake? Kodi iye adzapitirizabe kupha mitundu ya anthu mopanda chifundo?+

Mawu a M'munsi

Nʼkutheka kuti dzinali limatanthauza “Kukumbatira Mwachikondi.”
Ena amati “Mahosi.”
Mabaibulo ena amati, “mphamvu zawo, ndi mulungu wawo.”
Mabaibulo ena amati, “ife sitidzafa.”
Kapena kuti, “kuti mutidzudzule.”
Amenewa ndi Akasidi omwe ndi mdani.
Mʼchilankhulo choyambirira, “chonona.”
Mabaibulo ena amati, “adzapitirizabe kusolola lupanga lake.”