Habakuku 2:1-20

  • ‘Ndidzakhala tcheru kuti ndione zimene adzanene’ (1)

  • Zimene Yehova anayankha mneneri (2-​20)

    • ‘Uziyembekezerabe masomphenyawo’ (3)

    • Wolungama adzakhala ndi moyo chifukwa cha kukhulupirika (4)

    • Masoka 5 a Akasidi (6-20)

      • Anthu odziwa Yehova adzadzaza dziko lapansi (14)

2  Ine ndidzaimabe pamalo anga olondera.+Ndidzaima pamalo okwera omenyerapo nkhondo. Ndidzakhala tcheru kuti ndione zimene adzanene kudzera mwa ine,Ndiponso zimene ndingayankhe pamene iye akundidzudzula.   Kenako Yehova anandiyankha kuti: “Lemba masomphenyawa mooneka bwino pamiyala yosema,+Kuti wowerenga mokweza asavutike kuwerenga.*+   Chifukwa masomphenyawa akudikira nthawi yake yoikidwiratu,Atsala pangʼono kukwaniritsidwa* ndipo zimene zili mʼmasomphenyawa si zonama. Ngakhale atachedwa* uziwayembekezerabe,*+ Chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu. Sadzachedwa.   Taona munthu wodzikuza,Mtima wake si wowongoka. Koma wolungama adzakhala ndi moyo chifukwa cha kukhulupirika kwake.*+   Ndiye popeza vinyo ndi wachinyengo,Munthu wodzikuza sadzakwaniritsa cholinga chake. Iye amangolakalakabe ngati Manda,*Ndipo samakhutira ngati imfa. Iye amabweretsa mitundu yonse ya anthu,Ndipo amawasonkhanitsa kuti akhale ake.+   Kodi onsewa sadzamunenera mwambi, chiningʼa ndi mawu okuluwika?+ Adzanena kuti, ‘Tsoka kwa munthu amene amachulukitsa zinthu zomwe si zake.Ndiponso amene amachulukitsabe ngongole zake.Kodi adzachita zimenezi mpaka liti?   Kodi amene uli nawo ngongole sadzabwera modzidzimutsa? Adzadzuka nʼkukugwedeza mwamphamvu.Ndipo adzalanda zinthu zako.+   Chifukwa chakuti iwe unalanda zinthu za mitundu yambiri ya anthu,Anthu onse otsala a mitundu imeneyo adzalanda zinthu zako.+Adzachita zimenezi chifukwa unakhetsa magazi a anthu,Ndiponso unachitira chiwawa dziko lapansi,Komanso mizinda ndi anthu onse okhala mmenemo.+   Tsoka kwa munthu amene akupezera nyumba yake phindu mwachinyengo,Kuti amange chisa chake pamwamba,Nʼcholinga choti tsoka lisamupeze. 10  Wakonza zoti uchititse manyazi nyumba yako. Ndipo ukudzilakwira popha anthu a mitundu yambiri.+ 11  Mwala wapakhoma udzalira,Ndipo mtanda wapadenga udzayankha. 12  Tsoka kwa munthu amene amamanga mzinda pokhetsa magazi,Amenenso amakhazikitsa tauni pochita zosalungama. 13  Taona! Kodi si Yehova wa magulu ankhondo akumwamba amene adzachititse anthu kugwira ntchito mwakhama kuti moto uwononge ntchitoyo?Ndiponso kuti mitundu ya anthu idzitopetse pachabe?+ 14  Chifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa ulemerero wa Yehova,Ngati mmene madzi amadzazira nyanja.+ 15  Tsoka kwa amene amapatsa anzake chakumwa,Atasakanizamo mkwiyo ndi kupsa mtima kuti anzakewo aledzere,Nʼcholinga choti aone maliseche awo. 16  Iwe udzachita manyazi kwambiri mʼmalo mopeza ulemerero. Iwenso imwa ndipo udzaonekera kuti ndiwe wosadulidwa.* Kapu yochokera mʼdzanja lamanja la Yehova idzakupeza.+Ndipo ulemerero wako udzasanduka manyazi. 17  Chiwawa chimene unachitira Lebanoni chidzafika pa iwe.Ndipo chiwonongeko chimene chinaopseza nyama zakutchire chidzabwera kwa iwe.Chifukwa unakhetsa magazi a anthu,Ndiponso unachitira chiwawa dziko lapansi,Komanso mizinda ndi anthu onse okhala mmenemo.+ 18  Kodi chifaniziro chosema chili ndi phindu lanji,Pamene munthu wachisema? Nanga chifaniziro chachitsulo ndi mphunzitsi wonama zili ndi phindu lanji,Ngakhale kuti wochipanga amachikhulupirira,Nʼkumapanga milungu yopanda pake yosalankhula?+ 19  Tsoka kwa munthu amene amauza chikuni kuti: “Dzuka!” Kapena mwala wosalankhula kuti: “Dzuka! Tipatse malangizo”! Taona! Fanolo lakutidwa ndi golide ndi siliva,+Ndipo mkati mwake mulibe mpweya.+ 20  Koma Yehova ali mʼkachisi wake woyera.+ Inu anthu onse apadziko lapansi, khalani chete pamaso pake!’”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “awerenge mosadodoma.”
Kapena kuti, “Akuthamangira kumapeto kwake.”
Kapena kuti, “ataoneka ngati akuchedwa.”
Kapena kuti, “uziwayembekezerabe mwachidwi.”
Mabaibulo ena amati, “chikhulupiriro chake; zimene amakhulupirira.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mabaibulo ena amati, “ndipo udzadzandira.”