Hagai 1:1-15

  • Anadzudzula anthu chifukwa chosamanganso kachisi (1-11)

    • ‘Kodi ino ndi nthawi yoti inu muzikhala mʼnyumba zokongoletsedwa ndi matabwa?’ (4)

    • “Ganizirani mofatsa zimene mukuchita” (5)

    • Kudzala zambiri nʼkukolola zochepa (6)

  • Anthu anamvera mawu a Yehova (12-15)

1  Mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Mfumu Dariyo, mʼmwezi wa 6, pa tsiku loyamba la mweziwo, mawu a Yehova anafika kwa Zerubabele+ yemwe anali bwanamkubwa wa Yuda mwana wa Salatiyeli, ndiponso kwa Yoswa yemwe anali mkulu wa ansembe mwana wa Yehozadaki. Mawuwa anafika kwa anthu amenewa kudzera mwa mneneri Hagai*+ kuti:  “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Anthu awa akunena kuti: “Nthawi yomanga* nyumba* ya Yehova sinakwane.”’”+  Yehova analankhulanso kudzera mwa mneneri Hagai+ kuti:  “Kodi ino ndi nthawi yoti inu muzikhala mʼnyumba zokongoletsedwa ndi matabwa, nyumba iyi ili bwinja?+  Tsopano Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ganizirani mofatsa zimene mukuchita.  Mwadzala mbewu zambiri, koma mukukolola zochepa.+ Mukudya, koma simukukhuta. Mukumwa koma simukukhutira. Mukuvala zovala, koma simukumva kutenthera. Ndipo amene akugwira ganyu akuika ndalama zake mʼmatumba obowoka.’”  “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ganizirani mofatsa zimene mukuchita.’  ‘Pitani kuphiri mukatenge mitengo yomangira nyumba.+ Mumange nyumbayi+ kuti ndisangalale nayo komanso kuti nditamandidwe,’+ watero Yehova.”  “‘Munkayembekezera zinthu zambiri, koma mwapeza zochepa. Mutabweretsa zinthuzo mʼnyumba zanu, ine ndaziuzira nʼkuzimwaza.+ Nʼchifukwa chiyani ndachita zimenezi? Chifukwa nyumba yanga ili ngati bwinja, pomwe aliyense wa inu akuthamangathamanga kuti asamalire nyumba yake,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 10  ‘Nʼchifukwa chake kumwamba sikunakugwetsereni mame ndipo dziko lapansi silinakupatseni zokolola. 11  Ndinalamula kuti chilala chigwe padziko lapansi, pamapiri, pambewu, pavinyo watsopano, pamafuta, pazomera zonse, pa anthu, paziweto ndiponso pantchito iliyonse ya manja anu.’” 12  Ndiyeno Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli,+ Yoswa mwana wa Yehozadaki+ mkulu wa ansembe ndiponso anthu ena onse anamvera mawu a Yehova Mulungu wawo ndi a mneneri Hagai, chifukwa Yehova Mulungu wawo ndi amene anamutuma. Ndipo anthuwo anayamba kuchita mantha chifukwa cha Yehova. 13  Hagai, amene anatumidwa ndi Yehova, analankhula ndi anthuwo mogwirizana ndi ntchito imene Yehova anamʼpatsa. Iye anati: “‘Ine ndili ndi inu,’+ watero Yehova.” 14  Choncho Yehova analimbikitsa+ Zerubabele mwana wa Salatiyeli bwanamkubwa wa Yuda,+ Yoswa+ mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe ndiponso anthu ena onse. Ndipo iwo anabwera nʼkuyamba kugwira ntchito panyumba ya Mulungu wawo, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+ 15  Zimenezi zinachitika pa tsiku la 24 la mwezi wa 6, mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Mfumu Dariyo.+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza, “Wobadwa Pachikondwerero.”
Kapena kuti, “yomanganso.”
Kapena kuti, “kachisi.”